AMOSI 2
2
1 #
2Maf. 3.27; Yes. 15—16 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Mowabu, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatentha mafupa a mfumu ya ku Edomu asanduke njereza; 2koma ndidzatumiza moto pa Mowabu, udzanyeketsa nyumba zachifumu za Keriyoti; ndipo Mowabu adzafa ndi phokoso, ndi kufuula, ndi mau a lipenga; 3ndipo ndidzalikha woweruza pakati pake, ndi kupha akalonga ake onse, ati Yehova.
Chilango cha Mulungu pa Yuda ndi Israele
4 #
Lev. 26.14-17
Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Yuda, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza akaniza chilamulo cha Yehova, osasunga malemba ake; ndipo awalakwitsa mabodza ao amene makolo ao anawatsata; 5#Hos. 8.14koma ndidzatumiza moto pa Yuda, udzanyeketsa nyumba zachifumu za m'Yerusalemu. 6#2Maf. 4.1; Amo. 8.6Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Israele, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza agulitsa wolungama ndi ndalama, ndi wosowa chifukwa cha nsapato; 7ndiwo amene aliralira fumbi lapansi lili pamutu pa wosauka, napotoza njira ya wofatsa; ndipo munthu ndi atate wake amuka kwa namwali yemweyo, kuti aipse dzina langa loyera; 8#Eks. 22.26nagona pansi pa zofunda za chikole kumaguwa a nsembe ali onse, ndi m'nyumba ya Mulungu wao akumwa vinyo wa iwo olipitsidwa. 9#Num. 21.21-25Koma ndinaononga Ine pamaso pa Aamori, amene msinkhu wao unanga msinkhu wa mikungudza, nakhala nayo mphamvu ngati thundu; koma ndinaononga zipatso zao m'mwamba, ndi mizu yao pansi. 10#Eks. 12.51; Deut. 8.2Ndipo ndinakukwezani kuchokera m'dziko la Ejipito, ndi kukutsogolerani zaka makumi anai m'chipululu, kuti mulandire dziko la Aamori likhale cholowa chanu. 11#Num. 6.2-3Ndipo ndinaukitsa mwa ana anu aneneri, ndi mwa anyamata anu Anaziri. Si momwemo, inu ana a Israele, ati Yehova? 12Koma munamwetsa Anaziri vinyo, ndi kulamulira aneneri ndi kuti, Musamanenera. 13Taonani, ndidzakupsinjani m'malo mwanu, monga lipsinja galeta lodzala ndi mitolo fwa. 14#Mlal. 9.11; Mas. 33.16Ndipo populumukirapo padzasowera waliwiro, ndi wamphamvu; sadzalimbikitsa mphamvu yake, ndi ngwazi siidzapulumutsa moyo wake; 15#Mas. 33.17ndi wokoka uta sadzalimbika, ndi waliwiro sadzadzipulumutsa; ngakhale woyenda pa akavalo sadzapulumutsa moyo wake; 16ndi wolimba mtima mwa ngwazi adzathawa wamaliseche tsiku lomwelo, ati Yehova.
Currently Selected:
AMOSI 2: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi