YouVersion Logo
Search Icon

AMOSI 1

1
Chilango cha Mulungu pa amitundu ozinga Israele
1 # 2Sam. 14.2; 2Maf. 15.1, 13; Amo. 7.14 Mau a Amosi, amene anali mwa oweta ng'ombe a ku Tekowa, ndiwo amene anawaona za Israele masiku a Uziya mfumu ya Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele, zitatsala zaka ziwiri chisanafike chivomezi.
2Ndipo anati, Yehova adzadzuma ali m'Ziyoni, nadzamveketsa mau ake ali m'Yerusalemu; podyetsa abusa padzachita chisoni, ndi mutu wa Karimele udzauma.
3 # 2Maf. 10.32-33; 13.7; Yes. 23.1 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Damasiko, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anapuntha Giliyadi ndi zopunthira zachitsulo; 4#2Maf. 13.24-25koma ndidzatumiza moto kunyumba ya Hazaele, ndipo udzanyeketsa nyumba zachifumu za Benihadadi. 5#2Maf. 16.9; Yes. 8.4Ndipo ndidzathyola mpiringidzo wa Damasiko, ndi kulikha okhala m'chigwa cha Aveni, ndi iye wogwira ndodo yachifumu m'Betedeni; ndi anthu a Aramu adzalowa ndende ku Kiri, ati Yehova. 6#2Mbi. 28.17-18Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Gaza, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatenga ndende anthu onse kuwapereka kwa Edomu; 7koma ndidzatumiza moto pa linga la Gaza, ndipo udzatha nyumba zake zachifumu; 8#Zef. 2.4ndipo ndidzalikha okhala m'Asidodi, ndi iye wogwira ndodo yachifumu m'Asikeloni; ndipo ndidzabwezera Ekeroni dzanja langa limlange; ndi Afilisti otsala adzatayika, ati Ambuye Yehova.
9 # Yes. 23.1 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Tiro, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anapereka anthu onse kwa Edomu, osakumbukira pangano lachibale; 10koma ndidzatumiza moto pa linga la Tiro, ndipo udzanyeketsa nyumba zake zachifumu.
11 # Mas. 137.7 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Edomu, kapena zinani, sindidzabweza kulanga kwake; popeza analondola mphwake ndi lupanga, nafetsa chifundo chake chonse, ndi mkwiyo wake unang'amba ching'ambire nasunga mkwiyo wake chisungire; 12koma ndidzatumiza moto pa Temani, udzanyeketsa nyumba zachifumu za Bozira.
13 # Yer. 49.1-2 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za ana a Amoni, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatumbula akazi ali m'pakati a Giliyadi, kuti akuze malire ao; 14#Yer. 49.1-2koma ndidzayatsa moto pa linga la Raba, udzanyeketsa nyumba zachifumu zake, ndi kufuula tsiku la nkhondo, ndi namondwe, tsiku la kamvulumvulu; 15#Yer. 49.3ndipo mfumu yao idzalowa kundende, iyo ndi akalonga ake pamodzi, ati Yehova.

Currently Selected:

AMOSI 1: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in