Mau a Amosi, amene anali mwa oweta ng'ombe a ku Tekowa, ndiwo amene anawaona za Israele masiku a Uziya mfumu ya Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele, zitatsala zaka ziwiri chisanafike chivomezi.
Ndipo anati, Yehova adzadzuma ali m'Ziyoni, nadzamveketsa mau ake ali m'Yerusalemu; podyetsa abusa padzachita chisoni, ndi mutu wa Karimele udzauma.