AMOSI Mau Oyamba
Mau Oyamba
Amosi anali mneneri woyamba amene uthenga wake unalembedwa pafupifupi wonse. Ngakhale amachokera ku Yuda, iye analalikira kwa anthu a mu ufumu wa kumpoto kwa Israele m'zaka za pafupifupi 750 BC. Iyi inali nthawi imeneyo dziko linali pa mtendere, ndipo zinthu zimayenda bwino kumbali ya chuma komanso anthu amakonda kupembedza. Komabe Amosi adaona kuti odyerera chuma anali olemera okha basi, ndipo iwo amagwiritsa ntchito mphamvu zawo pofuna kupondereza osauka. Kupembedza kwao kunali kwachinyengo ndipo chitetezo sichinali monga zinthu zimaonekera. Analalikira ndi mtima wake wonse komanso mwamphamvu kuti Mulungu adzaononga dzikolo. Iye anawadandaulira kuti chilungamo chiyende “ngati mtsinje wosefuka” (5.24), ndi kuti pakutero, “kapena Yehova Mulungu wa makamu adzachitira chifundo otsala a Yosefe.” (5.15)
Za mkatimu
Chiweruzo pa maiko oyandikana ndi Israele 1.1—2.5
Chiweruzo pa Israele 2.6—6.14
Masomphenya asanu 7.1—9.15
Currently Selected:
AMOSI Mau Oyamba: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
![None](/_next/image?url=https%3A%2F%2Fimageproxy.youversionapi.com%2F58%2Fhttps%3A%2F%2Fweb-assets.youversion.com%2Fapp-icons%2Fen.png&w=128&q=75)
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi