YOWELE 3
3
Aneneratu za chilango cha Mulungu pa adani ake; Israele adzakonzekanso
1Pakuti taonani, masiku awo, ndi nthawi iyo, pamene ndibwera nao andende a Yuda ndi a Yerusalemu, 2#Yes. 66.16; Zek. 14.2-4ndidzasonkhanitsa amitundu onse, ndi kutsikira nao kuchigwa cha Yehosafati; ndipo ndidzaweruzana nao komweko za anthu anga, ndi cholowa changa Israele, amene anawabalalitsa mwa amitundu, nagawa dziko langa. 3Ndipo anachitira anthu anga maere, napereka mwana wamwamuna kusinthana ndi mkazi wadama, nagula vinyo ndi mwana wamkazi kuti amwe. 4#Amo. 1.9Ndiponso ndili ndi chiyani ndi inu, Tiro ndi Sidoni, ndi malire onse a Afilisti? Mudzandibwezera chilango kodi? Mukandibwezera chilango msanga, mofulumira, ndidzabwezera chilango chanu pamutu panu. 5Popeza inu munatenga siliva wanga ndi golide wanga, ndi kulonga zofunika zanga zokoma m'akachisi anu; 6munagulitsanso ana a Yuda ndi ana a Yerusalemu kwa ana a Yavani, kuwachotsa kutali kwa malire ao; 7#Yes. 43.5taonani, ndidzawautsa kumalo kumene munawagulitsako, ndi kubwezera chilango chanu pamutu panu; 8ndipo ndidzagulitsa ana ako aamuna ndi aakazi m'dzanja la ana a Yuda; ndipo iwo adzawagulitsa kwa anthu a Seba, kwa anthu okhala kutali; pakuti Yehova wanena.
9Mulalikire ichi mwa amitundu, mukonzeretu nkhondo; utsani amuna amphamvu; amuna onse a nkhondo ayandikire nakwere. 10Sulani makasu anu akhale malupanga, ndi zikwakwa zanu zikhale nthungo; wofooka anene, Ndine wamphamvu. 11#Yow. 3.2Fulumirani, idzani, amitundu inu nonse pozungulirapo; sonkhanani pamodzi, mutsitsire komweko amphamvu anu, Yehova. 12#Yow. 3.2Agalamuke amitundu, nakwerere kuchigwa cha Yehosafati; pakuti ndidzakhala komweko kuweruza amitundu onse ozungulira. 13#Mat. 13.39; Chiv. 14.15, 18Longani chisenga, pakuti dzinthu dzacha; idzani, pondani, pakuti chadzala choponderamo mphesa; zosungiramo zisefuka; pakuti zoipa zao nzazikulu. 14Aunyinji, aunyinji m'chigwa chotsirizira mlandu! Pakuti layandikira tsiku la Yehova m'chigwa chotsirizira mlandu. 15#Yow. 2.10, 31Dzuwa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zibweza kuwala kwao. 16#Yes. 51.5-6Ndipo Yehova adzadzuma ali ku Ziyoni, ndi kumveketsa mau ake ali ku Yerusalemu; ndi thambo ndi dziko lapansi zidzagwedezeka; koma Yehova adzakhala chopulumukirako anthu adzakhala chopulumukirako anthu ake, ndi linga la ana a Israele. 17Momwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu wakukhala m'Ziyoni, phiri langa lopatulika; pamenepo Yerusalemu adzakhala wopatulika, osapitanso alendo pakati pake, 18#Amo. 9.13Ndipo kudzachitika tsiku ilo mapiri adzakhetsa vinyo wozuna, ndi pazitunda padzayenda mkaka, ndi m'mitsinje yonse ya Yuda mudzayenda madzi; ndi madzi akasupe adzatuluka m'nyumba ya Yehova, nadzamwetsa madzi chigwa cha Sitimu. 19#Yes. 19.1-17; Yer. 49.17Ejipito adzasanduka bwinja, ndi Edomu adzasanduka chipululu chopanda kanthu, chifukwa cha chiwawachi anawachitira ana a Yuda; popeza anakhetsa mwazi wosachimwa m'dziko lao. 20#Mas. 125.1-2Koma Yuda adzakhala chikhalire, ndi Yerusalemu ku mibadwomibadwo. 21#Yes. 4.3-4; Yow. 3.17Ndipo ndidzayeretsa mwazi wao umene sindinauyeretsa, pakuti Yehova akhala m'Ziyoni.
Currently Selected:
YOWELE 3: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
![None](/_next/image?url=https%3A%2F%2Fimageproxy.youversionapi.com%2F58%2Fhttps%3A%2F%2Fweb-assets.youversion.com%2Fapp-icons%2Fen.png&w=128&q=75)
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi