AMOSI 6
6
Aisraele otsata zilakolako zao adzapsinjika ndi mtundu wina wa anthu
1 #
Eks. 19.5
Tsoka osalabadirawo m'Ziyoni, ndi iwo okhazikika m'phiri la Samariya, ndiwo anthu omveka a mtundu woposa wa anthu, amene nyumba ya Israele iwafikira! 2Pitani ku Kaline, nimuone; kuchokera komweko mupite ku Hamati wamkulu mutsikire ku Gati wa Afilisti; kodi awo ndi okoma koposa maufumu ano? Kapena malire ao aposa malire anu? 3#Ezk. 12.27Inu akutalikitsa tsiku loipa, ndi kusendeza pafupi mpando wachiwawa; 4ogona pamakama aminyanga, nadzithinula pa maguwa ao ogonapo, nadya anaankhosa a kuzoweta, ndi anaang'ombe ochoka pakati pa khola; 5akungoimba kutsata maliridwe a zeze, nadzilingiririra zoimbira nazo ngati Davide; 6#Gen. 37.25akumwera vinyo m'zipanda, nadzidzoza ndi mafuta abwino oposa, osagwidwa chisoni ndi kuthyoka kwa Yosefe. 7Chifukwa chake tsono, adzatengedwa ndende ndi oyamba kutengedwa ndende; ndi phokoso la iwo odzithinula lidzapita. 8#Ezk. 24.21Ambuye Yehova walumbira pali Iye mwini, ati Yehova Mulungu wa makamu, Ndinyansidwa nako kudzikuza kwa Yakobo, ndidana nazo nyumba zake zachifumu; m'mwemo ndidzapereka mudzi, ndi zonse zili m'menemo. 9Ndipo kudzachitika, mukatsala amuna khumi m'nyumba imodzi, adzafa. 10#Amo. 5.13; 8.3Ndipo mbale wake wa munthu akamnyamula, ndiye womtentha, kutulutsa mafupa m'nyumba, nakati kwa iye ali m'kati mwa nyumbamo, Atsala wina nawe kodi? Nakati Iai; pamenepo adzati, Khala chete; pakuti sitingatchule dzina la Yehova. 11Pakuti taonani, Yehova walamulira, nadzakantha nyumba yaikulu ichite mpata, ndi nyumba yaing'ono ichite mindala. 12#Amo. 5.7Kodi akavalo adzathamanga pathanthwe? Kodi adzalimako ndi ng'ombe pakuti mwasanduliza chiweruzo chikhale ndulu, ndi chipatso cha chilungamo chikhale chivumulo; 13inu okondwera nacho chopanda pake, ndi kuti, Kodi sitinadzilimbitsa tokha ndi kulanda Karinaimu mwa mphamvu yathuyathu? 14#Yer. 5.15Pakuti taonani, ndidzakuutsirani mtundu wa anthu, nyumba ya Israele, ati Yehova Mulungu wa makamu; ndipo adzakupsinjani kuyambira polowera ku Hamati kufikira mtsinje wa kuchidikha.
Currently Selected:
AMOSI 6: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi