YouVersion Logo
Search Icon

AMOSI 7

7
Masomphenya atatu, dzombe, moto wonyambita, ndi chingwe cholungamitsa chilili
1Ambuye Yehova anandionetsa chotere; ndipo taonani, anaumba dzombe, poyamba kuphuka kwa udzu a chibwereza; ndipo taonani, ndicho chibwereza atawasengera mfumu. 2Ndipo kunachitika m'mene lidatha kudya msipu wa dziko, ndinati, Ambuye Yehova, khululukiranitu Yakobo; adzakhala chilili bwanji? Popeza ndiye wamng'ono. 3Ndipo Yehova anachileka. Sichidzachitika, ati Yehova.
4Ambuye Yehova anandionetsa chotere; ndipo taonani, Ambuye Yehova anaitana kuti atsutse ndi moto; ndipo unanyambita chakuya chachikulu ukadanyambitanso dziko. 5Pamenepo ndinati, Ambuye Yehova, lekanitu; Yakobo adzakhala chilili bwanji? Pakuti ali wamng'ono. 6Ndipo Yehova anachileka. Ichi chomwe sichidzachitika, ati Ambuye Yehova.
7Anandionetsa chotere; ndipo taonani, Ambuye anaima pa khoma lomangidwa ndi chingwe cholungamitsira chilili; ndi chingwe cholungamitsira chilili m'dzanja lake. 8Ndipo Yehova anati kwa ine, Amosi, uona chiyani? Ndipo ndinati, Chingwe cholungamitsira chilili. Nati Ambuye, Taona, ndidzaika chingwe cholungamitsira chilili pakati pa anthu anga Israele, sindidzawalekanso: 9#2Maf. 15.10ndi misanje ya Isaki idzakhala bwinja; ndi malo opatulika a Israele adzapasuka; ndipo ndidzaukira nyumba ya Yerobowamu ndi lupanga.
Amosi ndi Amaziya atsutsana ku Betele
10Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Betele anatumiza kwa Yerobowamu mfumu ya Israele, ndi kuti, Amosi wapangira inu chiwembu pakati pa nyumba ya Israele; dziko silikhoza kulola mau ake onse. 11Pakuti atero Amosi, Yerobowamu adzafa ndi lupanga, ndi Israele adzatengedwadi ndende, kuchoka m'dziko lake. 12Amaziya anatinso kwa Amosi, Mlauli iwe, choka, thawira kudziko la Yuda, nudye, nunenere komweko; 13koma usaneneranso ku Betele; pakuti pamenepo mpa malo opatulika a mfumu, ndiyo nyumba yachifumu. 14#Amo. 1.1; Zek. 13.5Pamenepo Amosi anayankha, nati kwa Amaziya, Sindinali mneneri, kapena mwana wa mneneri, koma ndinali woweta ng'ombe, ndi wakutchera nkhuyu; 15ndipo Yehova ananditenga ndilikutsata nkhosa, nati kwa ine Yehova, Muka, nenera kwa anthu anga Israele. 16Chifukwa chake tsono, tamvera mau a Yehova, Iwe ukuti, Usamanenera chotsutsana ndi Israele, usadonthetsa mau akutsutsana ndi nyumba ya Isaki; 17chifukwa chake atero Yehova, Mkazi wako adzakhala wadama m'mudzi, ndi ana ako aamuna ndi aakazi adzagwa ndi lupanga, ndi dziko lako lidzagawanidwa ndi kuyesa chingwe, ndi iwe mwini udzafa m'dziko lodetsedwa; ndipo Israele adzatengedwadi ndende kuchoka m'dziko lake.

Currently Selected:

AMOSI 7: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in