MACHITIDWE A ATUMWI 5
5
Za Ananiya ndi Safira
1Koma munthu wina dzina lake Ananiya pamodzi ndi Safira mkazi wake, 2#Mac. 4.37anagulitsa chao, napatula pa mtengo wake, mkazi yemwe anadziwa, natenga chotsala, nachiika pa mapazi a atumwi. 3#Luk. 22.3Koma Petro anati, Ananiya, Satana anadzaza mtima wako chifukwa ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, ndi kupatula pa mtengo wake wa mundawo? 4Pamene unali nao, sunali wako kodi? Ndipo pamene unagulitsa sunali m'manja mwako kodi? Bwanji chinalowa ichi mumtima mwako? Sunanyenga anthu, komatu Mulungu. 5Koma Ananiya pakumva mau awa anagwa pansi namwalira: ndipo mantha akulu anagwera onse akumvawo. 6Ndipo ananyamuka anyamata, namkulunga, namnyamula, natuluka naye, namuika.
7Koma atapita monga maora atatu, ndipo mkazi wake, wosadziwa chidachitikacho, analowa. 8Ndipo Petro ananena naye, Undiuze, ngati munagulitsa mundawo pa mtengo wakuti. Ndipo ananena, Inde, wakuti. 9#Mat. 4.7Koma Petro anati kwa iye, Munapangana pamodzi bwanji kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona, mapazi ao a iwo amene anaika mwamuna wako ali pakhomo, ndipo adzakunyamula kutuluka nawe. 10Ndipo anagwa pansi pomwepo pa mapazi ake, namwalira; ndipo analowa anyamatawo, nampeza iye wafa, ndipo anamnyamula kutuluka naye, namuika kwa mwamuna wake. 11#Mac. 19.17Ndipo anadza mantha akulu pa Mpingo wonse, ndi pa onse akumva izi.
12 #
Mac. 14.3
Ndipo mwa manja a atumwi zizindikiro ndi zozizwa zambiri zinachitidwa pa anthu; ndipo anali onse ndi mtima umodzi m'khonde la Solomoni. 13Koma palibe mmodzi wa otsalawo analimba mtima kuphatikana nao; komatu anthu anawakuzitsa; 14ndipo makamaka anaonjezedwa kwa Ambuye okhulupirira ambiri, ndiwo amuna ndi akazi; 15#Mat. 14.36kotero kuti ananyamulanso natuluka nao odwala kumakwalala, nawaika pamakama ndi pamphasa, kuti, popita Petro, ngakhale chithunzi chake chigwere wina wa iwo. 16#Mrk. 16.17-18Komanso unasonkhana pamodzi unyinji wa anthu ochokera kumidzi yozungulira Yerusalemu, alikutenga odwala, ndi ovutika ndi mizimu yonyansa; ndipo anachiritsidwa onsewa.
Atumwi apulumutsidwa m'ndende, natengedwanso kupita nao kubwalo la akulu
17Koma anauka mkulu wa ansembe ndi onse amene anali naye, ndiwo a chipatuko cha Asaduki, nadukidwa, 18#Luk. 21.12nathira manja atumwi, nawaika m'ndende ya anthu wamba. 19#Mac. 12.7Koma mngelo wa Ambuye anatsegula pakhomo pa ndende usiku, nawatulutsa, nati, 20#Yoh. 6.68Pitani, ndipo imirirani, nimulankhule m'Kachisi kwa anthu onse mau a Moyo umene. 21Ndipo atamva ichi, analowa m'Kachisi mbandakucha, naphunzitsa. Koma anadza mkulu wa ansembe ndi iwo amene anali naye, nasonkhanitsa a bwalo la akulu, ndi akulu onse a ana a Israele, natuma kundende atengedwe ajawo. 22Koma anyamata amene adafikako sanawapeza m'ndende, ndipo pobwera anafotokoza, 23nanena, Nyumba yandende tinapeza chitsekere, ndi alonda alikuimirira pamakomo; koma pamene tinatsegula sitinapezamo mmodzi yense. 24Koma m'mene anamva mau awa mdindo wa Kachisi ndi ansembe aakulu anathedwa nzeru ndi iwo aja, kuti ichi chidzatani. 25Ndipo anadza wina nawafotokozera, kuti, Taonani, amuna aja mudawaika m'ndende ali m'Kachisi, alikuimirira ndi kuphunzitsa anthu. 26Pamenepo anachoka mdindo pamodzi ndi anyamata; anadza nao, koma osawagwiritsa, pakuti anaopa anthu, angaponyedwe miyala. 27Ndipo m'mene adadza nao, anawaika pa bwalo la akulu. Ndipo anawafunsa mkulu wa ansembe, 28#Mat. 27.25; Mac. 4.18nanena, Tidakulamulirani chilamulire, musaphunzitsa kutchula dzina ili; ndipo taonani, mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mufuna kutidzetsera ife mwazi wa munthu uja. 29#Mac. 4.19Ndipo anayankha Petro ndi atumwi, nati, Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu. 30#Mac. 10.39; 13.15Mulungu wa makolo athu anaukitsa Yesu, amene munamupha inu, ndi kumpachika pamtengo. 31#Luk. 24.47; Mac. 3.13-15Ameneyo Mulungu anamkweza ndi dzanja lake lamanja, akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi, kuti apatse kwa Israele kulapa, ndi chikhululukiro cha machimo. 32#Yoh. 15.26-27; Mac. 2.4Ndipo ife ndife mboni za zinthu izi; Mzimu Woyeranso, amene Mulungu anapatsa kwa iwo akumvera Iye.
33Koma m'mene anamva iwo analaswa mtima, nafuna kuwapha. 34#Mac. 22.3Koma ananyamukapo wina pa bwalo la akulu, ndiye Mfarisi, dzina lake Gamaliele, mphunzitsi wa chilamulo, wochitidwa ulemu ndi anthu onse, nalamula kuti atumwiwo akhale kunja pang'ono. 35Ndipo anati kwa iwo, Amuna inu a Israele, kadzichenjerani nokha za anthu awa, chimene muti muwachitire. 36Pakuti asanafike masiku ano anauka Teudasi, nanena kuti ali kanthu iye mwini; amene anthu anaphatikana naye, chiwerengero chao ngati mazana anai; ndiye anaphedwa; ndi onse amene anamvera iye anamwazika, napita pachabe. 37Atapita ameneyo, anauka Yudasi wa ku Galileya, masiku a kulembedwa, nakopa anthu amtsate. Iyeyunso anaonongeka, ndi onse amene anamvera iye anabalalitsidwa. 38#Mat. 15.13Ndipo tsopano ndinena ndi inu, Lekani anthu amenewa, nimuwalole akhale; pakuti ngati uphungu umene kapena ntchito iyi ichokera kwa anthu, idzapasuka; 39#Luk. 21.15; Mac. 7.51koma ngati ichokera kwa Mulungu simungathe kuwapasula; kuti kapena mungapezeke otsutsana ndi Mulungu. 40#Mat. 10.17Ndipo anavomerezana ndi iye; ndipo m'mene adaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kutchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula. 41#Mat. 5.12; Aro. 5.3; 1Pet. 4.13-14Pamenepo ndipo anapita kuchokera kubwalo la akulu, nakondwera kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzinalo. 42#Mac. 4.20, 29Ndipo masiku onse, m'Kachisi ndi m'nyumba, sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Khristu Yesu.
Currently Selected:
MACHITIDWE A ATUMWI 5: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi