MACHITIDWE A ATUMWI 6
6
Asankha atumiki asanu ndi awiri
1 #
Mac. 4.35
Koma masiku awo, pakuchulukitsa ophunzira, kunauka chidandaulo, Agriki kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye ao anaiwalika pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku. 2#Eks. 18.17-22Ndipo khumi ndi awiriwo anaitana unyinji wa ophunzira, nati, Sikuyenera kuti ife tisiye kulalikira mau a Mulungu ndi kutumikira podyerapo. 3#Eks. 18.17-22Chifukwa chake, abale, yang'anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge ntchito iyi. 4Koma ife tidzalimbika m'kupemphera, ndi kutumikira mau. 5#Mac. 8.5; 21.8Ndipo mau amene anakonda unyinji wonse; ndipo anasankha Stefano, ndiye munthu wodzala ndi chikhulupiriro ndi Mzimu Woyera, ndi Filipo, ndi Prokoro, ndi Nikanore ndi Timoni, ndi Parmenasi, ndi Nikolasi, ndiye wopinduka wa ku Antiokeya: 6#1Tim. 4.14amenewo anawaika pamaso pa atumwi; ndipo m'mene adapemphera, anaika manja pa iwo. 7#Yoh. 12.42Ndipo mau a Mulungu anakula; ndipo chiwerengero cha ophunzira chidachulukatu ku Yerusalemu; ndipo khamu lalikulu la ansembe linamvera chikhulupirirocho.
Stefano woyamba wophedwa chifukwa cha Khristu
8Ndipo Stefano, wodzala ndi chisomo ndi mphamvu, anachita zozizwa ndi zizindikiro zazikulu mwa anthu. 9Koma anauka ena a iwo ochokera m'sunagoge wa Alibertino, ndi Akirene, ndi Aaleksandriya, ndi mwa iwo a ku Silisiya ndi ku Asiya, natsutsana ndi Stefano. 10#Luk. 21.15Ndipo sanathe kuilaka nzeru ndi Mzimu amene analankhula naye. 11Pamenepo anafuna anthu akumpitira pansi, ndi kuti, Tidamumva iye alikunenera Mose ndi Mulungu mau amwano. 12Ndipo anautsa anthu, ndi akulu, ndi alembi, namfikira, namgwira iye, nadza naye kubwalo la akulu, 13naimika mboni zonama, zakunena, Munthu ameneyo saleka kunenera malo oyera amene, ndi chilamulo; 14pakuti tinamumva iye alikunena, kuti, Yesu Mnazarayo amene adzaononga malo ano, nadzasanduliza miyambo imene Mose anatipatsa. 15Ndipo anampenyetsetsa onse akukhala m'bwalo la akulu, naona nkhope yake ngati nkhope ya mngelo.
Currently Selected:
MACHITIDWE A ATUMWI 6: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi