YouVersion Logo
Search Icon

MACHITIDWE A ATUMWI 7

7
1Ndipo mkulu wa ansembe anati, Zitero izi kodi? 2Ndipo Stefano anati, Amuna inu, abale, ndi atate, tamverani. Mulungu wa ulemerero anaonekera kwa kholo lathu Abrahamu, pokhala iye m'Mesopotamiya, asanayambe kukhala m'Harani; 3#Gen. 12.1nati kwa iye, Tuluka kudziko lako ndi kwa abale ako, ndipo tiye kudziko limene ndidzakusonyeza iwe. 4#Gen. 11.31; 12.4Pamenepo anatuluka m'dziko la Akaldeya namanga m'Harani: ndipo, kuchokera kumeneko, atamwalira atate wake, Mulungu anamsuntha alowe m'dziko lino, m'mene mukhalamo tsopano; 5#Gen. 12.7ndipo sanampatsa cholowa chake m'menemo, ngakhale popondapo phazi lake iai; ndipo anamlonjezera iye kuti adzampatsa ili, likhale lake, ndi la mbeu yake yomtsatira, angakhale analibe mwana pamenepo. 6#Gen. 15.13, 16; Eks. 12.40Koma Mulungu analankhula chotero, kuti mbeu yake idzakhala alendo m'dziko la eni, ndipo adzawachititsa ukapolo, nadzawachitira choipa, zaka mazana anai. 7Ndipo mtundu amene udzawayesa akapolo, ndidzauweruza Ine, anatero Mulungu; ndipo zitapita izi adzatuluka, nadzanditumikira Ine m'malo muno. 8#Gen. 17.9-11; 21.2-4; 25.26; 29—30Ndipo anampatsa iye chipangano cha mdulidwe; ndipo kotero Abrahamu anabala Isaki, namdula tsiku lachisanu ndi chitatu; ndi Isaki anabala Yakobo, ndi Yakobo anabala makolo akulu aja khumi ndi awiri. 9#Gen. 37.4, 11, 28; 39.2, 21, 23Ndipo makolo akuluwa podukidwa naye Yosefe, anamgulitsa amuke naye ku Ejipito; ndipo Mulungu anali naye, 10#Gen. 41—42namlanditsa iye m'zisautso zake zonse, nampatsa chisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya ku Ejipito; ndipo anamuika iye kazembe wa pa Ejipito ndi pa nyumba yake yonse. 11#Gen. 41—42Koma inadza njala pa Ejipito ndi Kanani lonse, ndi chisautso chachikulu; ndipo sanapeza chakudya makolo athu. 12Koma pakumva Yakobo kuti muli tirigu m'Ejipito, anatuma makolo athu ulendo woyamba. 13#Gen. 45—46Ndipo pa ulendo wachiwiri Yosefe anazindikirika ndi abale ake; ndipo fuko la Yosefe linaonekera kwa Farao. 14#Gen. 45—46Ndipo Yosefe anatumiza, naitana Yakobo atate wake, ndi a banja lake lonse, ndiwo anthu makumi asanu ndi awiri mphambu asanu. 15#Gen. 45—46Ndipo Yakobo anatsikira ku Ejipito; ndipo anamwalira, iye ndi makolo athu; 16#Gen. 23.16; 33.19ndipo anawanyamula kupita nao ku Sekemu, nawaika m'manda amene Abrahamu adagula ndi mtengo wake wa ndalama kwa ana a Hamori m'Sekemu. 17Koma m'mene inayandikira nthawi ya lonjezo limene Mulungu adalonjezana ndi Abrahamu, anthuwo anakula nachuluka m'Ejipito, 18kufikira inauka mfumu ina pa Ejipito, imene siinamdziwa Yosefe. 19#Eks. 1.22Imeneyo inachenjerera fuko lathu, niwachitira choipa makolo athu, niwatayitsa tiana tao, kuti tingakhale ndi moyo. 20#Eks. 2.2-9Nyengo yomweyo anabadwa Mose, ndiye wokoma ndithu pamaso pa Mulungu; ndipo anamlera miyezi itatu m'nyumba ya atate wake: 21ndipo pakutayika iye, anamtola mwana wamkazi wa Farao, namlera akhale mwana wake. 22#Eks. 2.10Ndipo Mose anaphunzira nzeru zonse za Aejipito; nali wamphamvu m'mau ake ndi m'ntchito zake. 23#Eks. 2.11-12Koma pamene zaka zake zinafikira ngati makumi anai, kunalowa mumtima mwake kuzonda abale ake ana a Israele. 24#Eks. 2.11-12Ndipo pakuona wina woti alikumchitira choipa, iye anamtchinjiriza, nambwezera chilango wozunzayo, nakantha Mwejipito. 25#Eks. 4.1Ndipo anayesa kuti abale ake akazindikira kuti Mulungu alikuwapatsa chipulumutso mwa dzanja lake; koma sanazindikira. 26#Eks. 2.13Ndipo m'mawa mwake anawaonekera alikulimbana ndeu, ndipo anati awateteze, ayanjanenso, nati, Amuna inu, muli abale; muchitirana choipa bwanji? 27#Eks. 2.14Koma iye wakumchitira mnzake choipa anamkankha, nati, Wakuika iwe ndani mkulu ndi wotiweruzira? 28#Eks. 2.14Kodi ufuna kundipha ine, monga muja unapha Mwejipito dzulo? 29#Eks. 2.15Ndipo Mose anathawa pa mau awa, nakhala mlendo m'dziko la Midiyani; kumeneko anabala ana amuna awiri. 30#Eks. 3.2Ndipo zitapita zaka makumi anai, anamuonekera mngelo m'chipululu cha Sinai, m'lawi la moto wa m'chitsamba. 31#Eks. 3.4Koma Mose pakuona, anazizwa pa choonekacho; ndipo pakuyandikira iye kukaona, kunadza mau a Ambuye, 32#Eks. 3.6akuti, Ine ndine Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, ndi wa Isaki, ndi wa Yakobo. Ndipo Mose ananthunthumira, osalimbika mtima kupenyetsako. 33#Eks. 3.5Ndipo Ambuye anati kwa iye, Masula nsapato kumapazi ako; pakuti pa malo amene upondapo mpopatulika. 34#Eks. 3.7-10Kuona ndaona choipidwa nacho anthu anga ali m'Ejipito, ndipo amva kubuula kwao; ndipo ndatsika kuwalanditsa; ndipo tsopano, tiye kuno, ndikutume ku Ejipito. 35Mose uyu amene anamkana, ndi kuti, Wakuika iwe ndani mkulu ndi woweruza? Ameneyo Mulungu anamtuma akhale mkulu, ndi mombolo, ndi dzanja la mngelo womuonekera pachitsamba. 36#Eks. 7.11, 14Ameneyo anawatsogolera, natuluka nao atachita zozizwa ndi zizindikiro m'Ejipito, ndi m'Nyanja Yofiira, ndi m'chipululu zaka makumi anai. 37#Deut. 18.15, 18Uyu ndi Mose uja adati kwa ana a Israele, Mulungu adzakuutsirani Mneneri wa mwa abale anu, monga ine. 38#Eks. 19.3, 17; Agal. 3.19Uyu ndiye amene anali mu Mpingo m'chipululu pamodzi ndi mngelo wakulankhula naye m'phiri la Sinai, ndi makolo athu: amene analandira maneno amoyo akutipatsa ife; 39amene makolo athu sanafuna kumvera iye, koma anamkankha achoke, nabwerera m'mbuyo mumtima mwao ku Ejipito, 40#Eks. 32.11nati ndi Aroni, Tipangireni milungu yotitsogolera ife; pakuti Mose uja, amene anatitulutsa m'Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera. 41#Eks. 32.1Ndipo anapanga mwanawang'ombe masiku omwewo, nabwera nayo nsembe kwa fanolo, nasekerera ndi ntchito za manja ao. 42#Mas. 81.12; Amo. 5.25-26; Aro. 1.24Koma Mulungu anatembenuka, nawapereka iwo atumikire gulu la kumwamba; monga kwalembedwa m'buku la aneneri,
Kodi mwapereka kwa Ine nyama zophedwa ndi nsembe
zaka makumi anai m'chipululu, nyumba ya Israele inu?
43 # Amo. 5.25-26 Ndipo munatenga chihema cha Moleki,
ndi nyenyezi ya mulungu Refani,
zithunzizo mudazipanga kuzilambira;
ndipo ndidzakutengani kunka nanu m'tsogolo mwake mwa Babiloni.
44 # Eks. 25.40 Chihema cha umboni chinali ndi makolo athu m'chipululu, monga adalamula Iye wakulankhula ndi Mose, achipange ichi monga mwa chithunzicho adachiona. 45#Yos. 3.10, 14; 23.9Chimenenso makolo athu akudza m'mbuyo, analowa nacho ndi Yoswa polandira iwo zao za amitundu, amene Mulungu anawaingitsa pamaso pa makolo athu, kufikira masiku a Davide; 46amene anapeza chisomo pamaso pa Mulungu, napempha kuti apeze mokhalamo Mulungu wa Yakobo. 47#1Maf. 8.16-19Koma Solomoni anammangira nyumba. 48#1Maf. 8.27Komatu Wamwambamwambayo sakhala m'nyumba zomangidwa ndi manja; monga mneneri anena,
49 # Yes. 66.1-2 Thambo la kumwamba ndilo mpando wachifumu wanga,
ndi dziko lapansi chopondapo mapazi anga.
Mudzandimangira nyumba yotani, ati Ambuye,
kapena malo a mpumulo wanga ndi otani?
50Silinapanga dzanja langa zinthu izi zonse kodi?
51 # Yes. 48.4 Ouma khosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu Woyera nthawi zonse; monga anachita makolo anu, momwemo inu. 52#2Mbi. 36.16; Mat. 21.35Ndiye yani wa aneneri makolo anu sanamzunza? Ndipo anawapha iwo amene anaonetseratu za kudza kwake kwa Wolungamayo; wa Iye amene mwakhala tsopano akumpereka ndi akumupha; 53#Eks. 19.3, 17; Agal. 3.19inu amene munalandira chilamulo monga chidaikidwa ndi angelo, ndipo simunachisunga.
54Koma pakumva izi analaswa mtima, namkukutira mano. 55#Mac. 6.5Koma iye, pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, anapenyetsetsa Kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu, 56#Ezk. 1.1; Mat. 3.16; Mac. 10.11nati, Taonani, ndipenya m'Mwamba motseguka, ndi Mwana wa Munthu alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu. 57Koma anafuula ndi mau akulu, natseka m'makutu mwao, namgumukira iye ndi mtima umodzi; 58#Lev. 24.16; Mac. 22.20ndipo anamtaya kunja kwa mudzi, namponya miyala; ndipo mbonizo zinaika zovala zao pa mapazi a mnyamata dzina lake Saulo. 59#Luk. 23.34Ndipo anamponya miyala Stefano, alikuitana Ambuye, ndi kunena, Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga. 60#Luk. 23.34Ndipo m'mene anagwada pansi, anafuula ndi mau akulu, Ambuye, musawaikire iwo tchimo ili. Ndipo m'mene adanena ichi, anagona tulo.

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in