YouVersion Logo
Search Icon

MACHITIDWE A ATUMWI 4

4
Petro ndi Yohane ku bwalo la akulu
1Koma m'mene analikulankhula ndi anthu, ansembe ndi mdindo wa ku Kachisi ndi Asaduki anadzako, 2#Mat. 22.23ovutika mtima chifukwa anaphunzitsa anthuwo, nalalikira mwa Yesu kuuka kwa akufa. 3Ndipo anawathira manja, nawaika m'ndende kufikira m'mawa; pakuti mpa madzulo pamenepo. 4Koma ambiri a iwo amene adamva mau anakhulupirira; ndipo chiwerengero cha amuna chinali ngati zikwi zisanu.
5Koma panali m'mawa mwake, anasonkhana pamodzi m'Yerusalemu oweruza, ndi akulu, ndi alembi; 6#Yoh. 18.13ndi Anasi mkulu wa ansembe, ndi Kayafa, ndi Yohane, ndi Aleksandro, ndi onse amene anali a fuko la mkulu wa ansembe. 7#Mat. 21.23Ndipo m'mene anawaimika pakati, anafunsa kuti, Ndi mphamvu yanji, kapena m'dzina lanji, mwachita ichi inu? 8#Luk. 12.11-12Pamenepo Petro, wodzala ndi Mzimu Woyera anati kwa iwo, Oweruza a anthu inu, ndi akulu, 9ngati ife lero tiweruzidwa chifukwa cha ntchito yabwino ya pa munthu wodwala, ndi machiritsidwe ake, 10#Mac. 3.6, 16zindikirani inu nonse, ndi anthu onse a Israele, kuti m'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, amene inu munampachika pamtanda, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa, mwa Iyeyu munthuyu aimirirapo pamaso panu, wamoyo. 11#Mas. 118.22Iye ndiye mwalawo woyesedwa wopanda pake ndi inu omanga nyumba, umene unayesedwa mutu wa pangodya. 12#Mac. 10.43; 1Tim. 2.5-6Ndipo palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.
13 # Mat. 11.25; 1Ako. 1.27 Koma pakuona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo pozindikira kuti ndiwo anthu osaphunzira ndi opulukira, anazizwa ndipo anawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu. 14Ndipotu pakuona munthu wochiritsidwayo alikuimirira pamodzi nao, analibe kanthu kakunena kotsutsa. 15Koma pamene anawalamulira iwo achoke m'bwalo la akulu, ananena wina ndi mnzake, 16#Yoh. 11.47; Mac. 3.9-10kuti, Tidzawachitira chiyani anthu awa? Pakutitu chaoneka kwa onse akukhala m'Yerusalemu kuti chizindikiro chozindikirika chachitidwa ndi iwo, ndipo sitingathe kukana. 17Komatu tiwaopse asalankhulenso m'dzina ili kwa munthu aliyense, kuti chisabukenso kwa anthu. 18Ndipo anawaitana, nawalamulira kuti asanene konse kapena kuphunzitsa m'dzina la Yesu. 19#Mac. 5.29Koma Petro ndi Yohane anayankha nati kwa iwo, Weruzani, ngati nkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu; 20#Mac. 22.15pakuti sitingathe ife kuleka kulankhula zimene tinaziona ndi kuzimva. 21#Mat. 21.26Koma m'mene anawaopsanso anawamasula, osapeza kanthu kakuwalanga, chifukwa cha anthu; pakuti onse analemekeza Mulungu chifukwa cha chomwe chidachitika. 22Pakuti anali wa zaka zake zoposa makumi anai munthuyo, amene chizindikiro ichi chakumchiritsa chidachitidwa kwa iye.
Okhulupirira athamangira kupemphera
23 # Mac. 12.12 Ndipo m'mene anamasulidwa, anadza kwa anzao a iwo okha, nawauza zilizonse ansembe aakulu ndi akulu adanena nao. 24Ndipo m'mene adamva, anakweza mau kwa Mulungu ndi mtima umodzi, nati, Mfumu, Inu ndinu wolenga thambo la kumwamba ndi dziko, ndi nyanja, ndi zonse zili m'menemo; 25#Mas. 2.1amene mwa Mzimu Woyera, pakamwa pa kholo lathu Davide mtumiki wanu, mudati,
Amitundu anasokosera chifukwa chiyani?
Nalingirira zopanda pake anthu?
26Anadzindandalitsa mafumu a dziko,
ndipo oweruza anasonkhanidwa pamodzi,
kutsutsana ndi Ambuye, ndi Khristu wake.
27 # Yoh. 10.36 Pakuti zoonadi anasonkhanidwa m'mudzi muno Herode, ndi Pontio Pilato yemwe pamodzi ndi amitundu ndi anthu a Israele kumchitira choipa Mwana wanu wopatulika Yesu amene munamdzoza; 28#Mac. 2.23; 3.18kuti achite zilizonse dzanja lanu ndi uphungu wanu zidaweruziratu zichitike. 29#Mac. 4.13, 31; 14.3; 28.31Ndipo tsopano Ambuye, penyani mau ao akuopsa, ndipo patsani kwa akapolo anu alankhule mau anu ndi kulimbika mtima konse, 30#Mac. 3.6, 16m'mene mutambasula dzanja lanu kukachiritsa; ndi kuti zizindikiro ndi zozizwa zichitidwe mwa dzina la Mwana wanu wopatulika Yesu. 31#Mac. 2.2, 4; 4.29Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.
Madyerano a Akhristu oyamba
32 # Mac. 2.44; Afi. 1.27 Ndipo unyinji wa iwo akukhulupirira anali wa mtima umodzi ndi moyo umodzi; ndipo sananena mmodzi kuti kanthu ka chuma anali nacho ndi kake ka iye yekha; koma anali nazo zonse zodyerana. 33#Mac. 1.22Ndipo atumwi anachita umboni ndi mphamvu yaikulu za kuuka kwa Ambuye Yesu; ndipo panali chisomo chachikulu pa iwo onse. 34#Mac. 2.45Pakuti mwa iwo munalibe wosowa; pakuti onse amene anali nayo minda, kapena nyumba, anazigulitsa nabwera nao malonda ake a izo adazigulitsa, 35#Mac. 4.37nawaika pa mapazi a atumwi; ndipo anagawira yense monga kusowa kwake.
36Ndipo Yosefe, wotchedwa ndi atumwi Barnabasi (ndilo losandulika mwana wa chisangalalo), Mlevi, fuko lake la ku Kipro, 37#Mac. 4.35pokhala nao munda, anaugulitsa, nabwera nazo ndalama zake, naziika pa mapazi a atumwi.

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in