YouVersion Logo
Search Icon

MACHITIDWE A ATUMWI 3

3
Wopunduka chibadwire achiritsidwa. Chonenera Petro m'Kachisi
1Koma Petro ndi Yohane analikukwera kunka ku Kachisi pa ora lakupembedza, ndilo lachisanu ndi chinai. 2Ndipo munthu wina wopunduka miyendo chibadwire ananyamulidwa, amene akamuika masiku onse pa khomo la Kachisi lotchedwa Lokongola, kuti apemphe zaulere kwa iwo akulowa m'Kachisi; 3#Yoh. 9.8ameneyo, pakuona Petro ndi Yohane akuti alowe m'Kachisi, anapempha alandire chaulere. 4Ndipo Petro, pompenyetsetsa iye pamodzi ndi Yohane, anati, Tiyang'ane ife. 5Ndipo iye anavomereza iwo, nalingirira kuti adzalandira kanthu. 6#Mac. 4.10Koma Petro anati, Siliva ndi golide ndilibe; koma chimene ndili nacho, ichi ndikupatsa, M'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, yenda. 7Ndipo anamgwira iye kudzanja lake lamanja, namnyamutsa; ndipo pomwepo mapazi ake ndi mfundo za kumapazi zinalimbikitsidwa. 8#Yes. 35.6Ndipo anazunzuka, naimirira, nayenda; ndipo analowa pamodzi nao m'Kachisi, nayenda, nalumpha, nayamika Mulungu. 9Ndipo anthu onse anamuona iye, alikuyenda ndi kuyamika Mulungu; 10namzindikira iye, kuti ndiye amene anakhala pa Khomo Lokongola la Kachisi: ndipo anadzazidwa ndi kudabwa ndi kuzizwa pa ichi chidamgwera.
11Koma m'mene anagwira Petro ndi Yohane, anawathamangira pamodzi anthu onse kukhonde lotchedwa la Solomoni, alikudabwa ndithu. 12Koma m'mene Petro anachiona, anayankha kwa anthu, Amuna inu a Israele, muzizwa naye bwanji ameneyo? Kapena mutipenyetsetsa ife bwanji, monga ngati tamyendetsa iye ndi mphamvu ya ife eni, kapena ndi chipembedzo chathu? 13#Mat. 27.2, 20; Yoh. 12.16Mulungu wa Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, analemekeza Mwana wake Yesu; amene inu munampereka ndi kumkaniza pa Pilato, poweruza iyeyu kummasula. 14#Mat. 27.2, 20Koma inu munakaniza Woyera ndi Wolungamayo, ndipo munapempha kuti munthu wambanda apatsidwe kwa inu, 15#Mac. 2.24, 32ndipo munamupha Mkulu wa moyo; amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa; za ichi ife tili mboni. 16#Mat. 9.22Ndipo pa chikhulupiriro cha m'dzina lake dzina lakelo linalimbikitsa iye amene mumuona, nimumdziwa; ndipo chikhulupiriro chili mwa Iye chinampatsa kuchira konse kumeneku pamaso pa inu nonse. 17#Luk. 23.34Ndipo tsopano, abale, ndidziwa kuti munachichita mosadziwa, monganso akulu anu. 18Koma zimene Mulungu analalikiratu m'kamwa mwa aneneri onse, kuti adzamva kuwawa Khristu, Iye anakwaniritsa chotero. 19#Mac. 2.38Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera kunkhope ya Ambuye; 20ndipo atume amene anaikidwa kwa inu, Khristu Yesu; 21amene thambo la kumwamba liyenera kumlandira kufikira nthawi zakukonzanso zinthu zonse, zimene Mulungu analankhula za izo m'kamwa mwa aneneri ake oyera chiyambire. 22#Deut. 18.15, 18-19Mosetu anati, Mbuye Mulungu adzaukitsira inu mneneri mwa abale anu, ngati ine; mudzamvera iye m'zinthu zilizonse akalankhule nanu. 23Ndipo kudzali, kuti wamoyo aliyense samvera mneneri ameneyu, adzasakazidwa konse mwa anthu. 24Koma angakhale aneneri onse kuyambira Samuele ndi akumtsatira, onse amene analankhula analalikira za masiku awa. 25#Gen. 12.3; Agal. 3.8Inu ndinu ana a aneneri, ndi a panganolo Mulungu anapangana ndi makolo anu ndi kunena kwa Abrahamu, Ndipo mu mbeu yako mafuko onse a dziko adzadalitsidwa. 26#Mat. 1.21; 15.24Kuyambira ndi inu, Mulungu, ataukitsa Mwana wake, anamtuma kukudalitsani inu, ndi kukubwezani yense ku zoipa zake.

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in