YouVersion Logo
Search Icon

MACHITIDWE A ATUMWI 2

2
Tsiku la Pentekoste
1 # Lev. 23.15; Mac. 1.14 Ndipo pakufika tsiku la Pentekoste, anali onse pamodzi pa malo amodzi. 2#Mac. 4.31Ndipo mwadzidzidzi anamveka mau ochokera Kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene analikukhalamo. 3Ndipo anaonekera kwa iwo malilime ogawanikana, onga amoto; ndipo unakhala pa iwo onse wayekhawayekha. 4#Mrk. 16.17; Mac. 1.5; 1Ako. 12.10, 28, 30Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.
5Koma anali m'Yerusalemu okhalako Ayuda, amuna opembedza, ochokera kumtundu uliwonse pansi pa thambo. 6Koma pochitika mau awa, unyinji wa anthu unasonkhana, nusokonezedwa, popeza yense anawamva alikulankhula m'chilankhulidwe chake cha iye yekha. 7#Mac. 1.11Ndipo anadabwa onse, nazizwa, nanena, Taonani, awa onse alankhulawa sali Agalileya kodi? 8Ndipo nanga ife timva bwanji, yense m'chilankhulidwe chathu chimene tinabadwa nacho? 9Aparti ndi Amedi, ndi Aelamu, ndi iwo akukhala m'Mesopotamiya, m'Yudeya, ndiponso m'Kapadokiya, m'Ponto, ndi m'Asiya; 10m'Frijiya, ndiponso m'Pamfiliya, m'Ejipito, ndi mbali za Libiya wa ku Kirene, ndi alendo ochokera ku Roma, 11ndiwo Ayuda, ndiponso opinduka, Akrete, ndi Aarabu, tiwamva iwo alikulankhula m'malilime athu zazikulu za Mulungu. 12Ndipo anadabwa onse, nathedwa nzeru, nanena wina ndi mnzake, Kodi ichi nchiyani? 13Koma ena anawaseka, nanena kuti, Akhuta vinyo walero.
Chodzikanira cha Petro
14Koma Petro, anaimirira pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo, nakweza mau ake, nanena kwa iwo, nati, Amuna inu Ayuda, ndi inu nonse akukhala kwanu m'Yerusalemu, ichi chizindikirike kwa inu, ndipo tcherani khutu mau anga. 15Pakuti awa sanaledzera monga muyesa inu; pakuti ndi ora lachitatu lokha la tsiku; 16komatu ichi ndi chimene chinanenedwa ndi mneneri Yowele,
17 # Yow. 2.28-32; Yoh. 7.38-39; Mac. 10.45 Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu,
ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi lililonse,
ndipo ana anu amuna, ndi akazi adzanenera,
ndipo anyamata anu adzaona masomphenya,
ndi akulu anu adzalota maloto;
18ndiponso pa akapolo anga ndi pa adzakazi anga m'masiku awa
ndidzathira cha Mzimu wanga; ndipo adzanenera.
19Ndipo ndidzapatsa zodabwitsa m'thambo la kumwamba,
ndi zizindikiro pa dziko lapansi;
mwazi, ndi moto, ndi mpweya wa utsi;
20 # Mat. 24.29 dzuwa lidzasanduka mdima,
ndi mwezi udzasanduka mwazi,
lisanadze tsiku la Ambuye,
lalikulu ndi loonekera.
21 # Aro. 10.13 Ndipo kudzali, kuti yense amene akaitana
pa dzina la Ambuye adzapulumutsidwa.
22 # Yoh. 3.2 Amuna inu Aisraele, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wochokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndi zimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikiro, zimene Mulungu anazichita mwa Iye pakati pa inu monga mudziwa nokha; 23#Luk. 22.22; Mac. 5.30ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu, inu mwampachika ndi kumupha ndi manja a anthu osaweruzika; 24#Mac. 2.32; 10.40; Aro. 8.11; 1Ako. 15.15; Agal. 1.1yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti Iye agwidwe nayo. 25#Mas. 16.8-11Pakuti Davide anena za Iye,
Ndinaona Mbuye pamaso panga nthawi zonse;
chifukwa ali pa dzanja langa lamanja, kuti ndingasinthike;
26mwa ichi unakondwera mtima wanga,
ndipo linasangalala lilime langa;
ndipo thupi langanso lidzakhala m'chiyembekezo.
27Pakuti simudzasiya moyo wanga ku dziko la akufa,
kapena simudzapereka Woyera wanu aone chivunde,
28munandidziwitsa ine njira za moyo;
mudzandidzaza ndi kukondwera pamaso panu.
29 # 1Maf. 2.10 Amuna inu, abale, kuloleka kunena poyera posaopa kwa inu za kholo lija Davide, kuti adamwalira naikidwanso, ndipo manda ake ali ndi ife kufikira lero lino. 30#2Sam. 7.12-13Potero, pokhala mneneri iye, ndi kudziwa kuti ndi lumbiro anamlumbirira Mulungu, kuti mwa chipatso cha m'chuuno mwake adzakhazika wina pa mpando wachifumu wake; 31#Mas. 16.10iye pakuona ichi kale, analankhula za kuuka kwa Khristu, kuti sanasiyidwa m'dziko la akufa, ndipo thupi lake silinaona chivunde. 32#Mac. 2.24Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa; za ichi tili mboni ife tonse. 33#Yoh. 14.26; Afi. 2.9Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ichi, chimene inu mupenya nimumva. 34#Mas. 110.1; Mat. 22.44; 1Ako. 15.25Pakuti Davide sanakwera Kumwamba ai; koma anena yekha,
Ambuye anati kwa Mbuye wanga,
khalani kudzanja lamanja langa,
35kufikira ndikaike adani ako chopondapo mapazi ako.
36 # Mac. 5.31 Pamenepo lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israele, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Khristu, Yesu amene inu munampachika.
Otembenuka mtima oyamba
37 # Luk. 3.10 Koma pamene anamva ichi, analaswa mtima, natitu kwa Petro ndi atumwi enawo, Tidzachita chiyani, amuna inu, abale? 38#Luk. 24.47Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. 39#Yow. 2.28; Mac. 10.45; Aro. 8.30; Aef. 2.13, 17Pakuti lonjezano lili kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana. 40Ndipo ndi mau ena ambiri anachita umboni, nawadandaulira iwo, nanena, Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota. 41Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu. 42#Aef. 6.18; Aheb. 10.25Ndipo anali chikhalire m'chiphunzitso cha atumwi ndi m'chiyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero.
43 # Mrk. 16.17 Koma panadza mantha pa anthu onse; ndipo zozizwa ndi zizindikiro zambiri zinachitika ndi atumwi. 44#Mac. 4.32, 34Ndipo onse akukhulupirira anali pamodzi, nakhala nazo zonse zodyerana. 45Ndipo zimene anali nazo, ndi chuma chao, anazigulitsa, nazigawira kwa onse, monga momwe yense anasowera. 46#Luk. 24.53Ndipo tsiku ndi tsiku anali chikhalire ndi mtima umodzi m'Kachisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira chakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona; 47#Mac. 5.14; Aro. 14.17-18nalemekeza Mulungu, ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse. Ndipo Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in