Koma Petro anati, Ananiya, Satana anadzaza mtima wako chifukwa ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, ndi kupatula pa mtengo wake wa mundawo? Pamene unali nao, sunali wako kodi? Ndipo pamene unagulitsa sunali m'manja mwako kodi? Bwanji chinalowa ichi mumtima mwako? Sunanyenga anthu, komatu Mulungu. Koma Ananiya pakumva mau awa anagwa pansi namwalira: ndipo mantha akulu anagwera onse akumvawo.