YouVersion Logo
Search Icon

2 YOHANE 1

1
1 # 1Yoh. 3.18 Mkuluyo kwa mkazi womveka wosankhika, ndi ana ake, amene ine ndikondana nao m'choonadi; ndipo si ine ndekha, komanso onse akuzindikira choonadi; 2chifukwa cha choonadi chimene chikhala mwa ife, ndipo chidzakhala ndi ife ku nthawi yosatha: 3Chisomo, chifundo, mtendere zikhale ndi ife zochokera kwa Mulungu Atate, ndi kwa Yesu Khristu Mwana wa Atate, m'choonadi ndi m'chikondi.
Za chikondano. Za aphunzitsi onyenga
4 # 3Yoh. 3 Ndakondwera kwakukulu kuti ndapeza ena a ana anu alikuyenda m'choonadi, monga tinalandira lamulo lochokera kwa Atate. 5#1Yoh. 3.11Ndipo tsopano ndikupemphani, mkazi womveka inu, wosati monga kukulemberani lamulo latsopano, koma lomwelo tinali nalo kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mnzake. 6#Yoh. 14.15, 21Ndipo chikondi ndi ichi, kuti tiyende monga mwa malamulo ake. Ili ndi lamulolo, monga mudalimva kuyambira pachiyambi, kuti mukayende momwemo. 7#1Yoh. 3.18Pakuti onyenga ambiri adatuluka kulowa m'dziko lapansi, ndiwo amene savomereza kuti Yesu Khristu anadza m'thupi. Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Khristu. 8#Aheb. 10.32, 35Mudzipenyerere nokha, kuti mungataye zimene tazichita, koma kuti mulandire mphotho yokwanira. 9#1Yoh. 2.23Yense wakupitirira, wosakhala m'chiphunzitso cha Khristu, alibe Mulungu; iye wakukhala m'chiphunzitso, iyeyo ali nao Atate ndi Mwana. 10#Aro. 16.17Munthu akadza kwa inu, wosatenga chiphunzitso ichi, musamlandire iye kunyumba, ndipo musampatse moni. 11Pakuti iye wakumpatsa moni ayanjana nazo ntchito zake zoipa.
12 # Yoh. 17.13 Pokhala ndili nazo zambiri zakukulemberani, sindifuna kuchita ndi kalata ndi kapezi; koma ndiyembekeza kudza kwa inu, ndi kulankhula popenyana, kuti chimwemwe chanu chikwanire. 13#1Pet. 5.13Akupereka moni ana a mbale wanu wosankhika.

Currently Selected:

2 YOHANE 1: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in