2 YOHANE Mau Oyamba
Mau Oyamba
Kalata yachiwiri yolembedwa ndi mtumwi Yohane inalembedwa ndi “Mkuluyo” kupita kwa “mkazi womveka wosankhika, ndi ana ake”, amene mwina akutanthauza mpingo ndi anthu ake. Uthenga wake ndi waufupi ndipo ndi wolimbitsana za kukondana komanso kuchenjeza za aphunzitsi onyenga ndi ziphunzitso zawo zachinyengo.
Za mkatimu
Mau oyamba 1.1-3
Kufunikira kwa chikondi 1.4-6
Awachenjeze asatsate ziphunzitso zonyenga 1.7-11
Mau omaliza 1.12-13
Currently Selected:
2 YOHANE Mau Oyamba: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi