YouVersion Logo
Search Icon

1 SAMUELE 18

18
Ubwenzi wa Davide ndi Yonatani
1 # 1Sam. 20.17; 2Sam. 1.26 Ndipo kunali, pakutsiriza iye kulankhula ndi Saulo, mtima wa Yonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Yonatani anamkonda iye monga moyo wa iye yekha. 2Ndipo Saulo anamtenga tsiku lomwelo, osamlolanso apite kwao kwa atate wake. 3Pamenepo Yonatani ndi Davide anapangana pangano, pakuti adamkonda iye ngati moyo wa iye yekha. 4Ndipo Yonatani anavula malaya ake anali nao, napatsa Davide, ndi zovala zake, ngakhale lupanga lake, ndi uta wake, ndi lamba lake. 5Ndipo Davide anatuluka kunka kulikonse Saulo anamtumako, nakhala wochenjera; ndipo Saulo anamuika akhale woyang'anira anthu a nkhondo; ndipo ichi chinakomera anthu onse, ndi anyamata a Saulo omwe.
6Ndipo kunali pakudza iwo, pamene Davide anabwera atapha Afilistiwo, anthu akazi anatuluka m'midzi yonse ya Israele, ndi kuimba ndi kuvina, kuti akakomane ndi mfumu Saulo, ndi malingaka, ndi chimwemwe, ndi zoimbira. 7#Eks. 15.21Ndipo akazi anathirirana mang'ombe m'kuimba kwao, nati,
Saulo anapha zikwi zake,
koma Davide zikwi zake zankhani.
Saulo aipidwa ndi Davide
8 # 1Sam. 15.28 Koma Saulo anakwiya ndithu, ndi kunenaku kunamuipira; nati, Kwa Davide anawerengera zikwi zankhani, koma kwa ine zikwi zokha; chimperewera nchiyaninso, koma ufumu wokha? 9Ndipo kuyambira tsiku lomwelo ndi m'tsogolo mwake, Saulo anakhala maso pa Davide.
10 # 1Sam. 16.14 Ndipo kunali m'mawa mwake, mzimu woipa wochokera kwa Mulungu unamgwira Saulo mwamphamvu, iye nalankhula moyaluka m'nyumba yake; koma Davide anaimba ndi dzanja lake, monga amachita tsiku ndi tsiku; koma m'dzanja la Saulo munali mkondo. 11#1Sam. 19.9-10Ndipo Saulo anaponya mkondowo; pakuti anati, Ndidzapyoza Davide ndi kumphatikiza ndi khoma. Ndipo Davide analewa kawiri kuchoka pamaso pake. 12#Gen. 35.5; 1Sam. 16.14, 18; 18.15Ndipo Saulo anaopa Davide chifukwa Yehova anali naye, koma adamchokera Saulo.
13 # 2Sam. 5.2 Chifukwa chake Saulo anamchotsa kuti asakhale naye, namuika akhale mtsogoleri wake wa anthu chikwi chimodzi; ndipo iye anatsogolera anthu kutuluka ndi kubwera nao. 14Ndipo Davide anakhala wochenjera m'mayendedwe ake onse; ndipo Yehova anali naye. 15#1Sam. 18.12Ndipo pamene Saulo anaona kuti analikukhala wochenjera ndithu anamuopa. 16#1Sam. 18.5Koma Aisraele onse ndi Ayuda onse anamkonda Davide pakuti anawatsogolera kutuluka ndi kulowa nao.
Davide mkamwini wa Saulo
17 # 1Sam. 17.25; 18.25 Ndipo Saulo anati kwa Davide, Ona, mwana wanga wamkazi wamkulu, dzina lake Merabi, iyeyo ndidzakupatsa akhale mkazi wako; koma undikhalire ngwazi, nuponye nkhondo za Yehova. Pakuti Saulo anati, Dzanja langa lisamkhudze, koma dzanja la Afilisti ndilo. 18#2Sam. 7.18Ndipo Davide anati kwa Saulo, Ine ndiye yani, ndi moyo wanga uli wotani, kapena banja la atate wanga lili lotani m'Israele, kuti ine ndidzakhala mkamwini wa mfumu? 19Koma kunali nthawi imene akadapatsa Merabi mwana wamkazi wa Saulo kwa Davide, iye anapatsidwa kwa Adriyele Mmehola kukhala mkazi wake. 20#1Sam. 18.28Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo anakonda Davide; ndipo pakumva Saulo, anakondwera nako. 21#1Sam. 18.17Nati Saulo, Ndidzampatsa iye, kuti amkhalire msampha, ndi kuti dzanja la Afilisti limgwere. Chifukwa chake Saulo ananena ndi Davide, Lero udzakhala mkamwini wanga kachiwiri. 22Ndipo Saulo analamulira anyamata ake, nati, Mulankhule naye Davide m'tseri, ndi kuti, Taonani mfumu akondwera nanu, ndi anyamata ake onse akukondani; chifukwa chake tsono, khalani mkamwini wa mfumu. 23Ndipo anyamata a Saulo analankhula mau awa m'makutu a Davide. Nati Davide, Kodi muchiyesera chinthu chopepuka kukhala mkamwini wa mfumu, popeza ndili munthu wosauka, ndi wopeputsidwa. 24Ndipo anyamata a Saulo anamuuza, kuti, Anatero Davide. 25#1Sam. 18.17Nati Saulo, Mudzatero kwa Davide, kuti mfumu safuna cholowolera china, koma nsonga za makungu zana limodzi za Afilisti, kuti abwezere chilango adani a mfumu. Koma Saulo anaganizira kupha Davide ndi dzanja la Afilisti. 26Ndipo pamene anyamata ake anauza Davide mau awa, kudamkomera Davide kukhala mkamwini wa mfumu. 27Ndipo asanathe masikuwo, ananyamuka Davide, ndi anthu ake, nakaphako Afilisti mazana awiri, ndipo Davide anatenga nsonga za makungu ao nazipatsa mofikira kwa mfumu, kuti akhale mkamwini wa mfumu. Ndipo Saulo anampatsa Mikala mwana wake wamkazi akhale mkazi wake. 28Ndipo Saulo anaona, nadziwa kuti Yehova ali ndi Davide; ndi kuti Mikala mwana wa Saulo anamkonda Davide. 29Saulo nayamba kumuopa Davide kopambana; ndi Saulo anali mdani wa Davide masiku onse.
30 # 1Sam. 18.5 Pomwepo mafumu a Afilisti anatuluka; ndipo nthawi zonse anatuluka iwo, Davide anali wochenjera koposa anyamata onse a Saulo, chomwecho dzina lake linatamidwa kwambiri.

Currently Selected:

1 SAMUELE 18: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in