Ndipo akazi anathirirana mang'ombe m'kuimba kwao, nati,
Saulo anapha zikwi zake,
koma Davide zikwi zake zankhani.
Koma Saulo anakwiya ndithu, ndi kunenaku kunamuipira; nati, Kwa Davide anawerengera zikwi zankhani, koma kwa ine zikwi zokha; chimperewera nchiyaninso, koma ufumu wokha?