1 SAMUELE 17
17
Davide apha Goliyati
1Pamenepo Afilisti anasonkhanitsa makamu ao a nkhondo, naunjikana ku Soko wa ku Yuda, namanga zithando pakati pa Soko ndi Azeka ku Efesi-Damimu. 2Ndipo Saulo ndi anthu a Israele anasonkhana, namanga zithando pa chigwa cha Ela, nandandalitsa nkhondo yao kuti akaponyane ndi Afilisti. 3Ndipo Afilisti anaima paphiri tsidya lija, ndi Aisraele anaima paphiri tsidya lina; ndi pakati pao panali chigwa. 4Ndipo ku zithando za Afilisti kunatuluka chiwinda, dzina lake Goliyati wa ku Gati, kutalika kwake ndiko mikono isanu ndi umodzi ndi dzanja limodzi. 5Ndipo anali ndi chisoti chamkuwa pamutu pake, navala malaya aunyolo, olemera ngati masekeli zikwi zisanu za mkuwa, 6nakuta msongolo wake ndi chovala chamkuwa, ndiponso pachikota pake panali nthungo yamkuwa. 7Ndipo mtengo wa mkondo wake unali ngati mtanda woombera nsalu; ndi khali la mkondowo linalemera ngati masekeli mazana asanu ndi limodzi a chitsulo; ndipo womnyamulira chikopa anamtsogolera. 8Naima iye naitana makamu a nkhondo a Israele, nanena nao, Munatulukiranji kundandalitsa nkhondo yanu? Sindine Mfilisti kodi, ndi inu anyamata a Saulo? Mudzisankhire munthu, atsikire kwa ine. 9Akakhoza iyeyo kuponyana ndi ine ndi kundipha, tidzakhala ife akapolo anu; koma ine ndikamlaka, ndi kumupha, tsono mudzakhala inu akapolo athu, ndi kutitumikira ife. 10#1Sam. 17.26; 2Sam. 21.21Nati Mfilistiyo, Ine ndinyoza makamu a nkhondo a Israele lero; mundipatse munthu, kuti tilimbane ife awiri. 11Ndipo pamene Saulo ndi Aisraele onse anamva mau ao a Mfilistiyo, anadodoma, naopa kwambiri.
12Tsono Davide anali mwana wa Mwefurati uja wa ku Betelehemu-Yuda, dzina lake ndiye Yese; ameneyu anali nao ana amuna asanu ndi atatu; ndipo m'masiku a Saulo munthuyo anali nkhalamba, mwa anthu. 13Ndipo ana atatu akulu a Yese anatsata Saulo kunkhondoko; ndi maina ao a ana ake atatuwo adapita ku nkhondowo ndiwo Eliyabu woyambayo, ndi mnzake womponda pamutu pake Abinadabu, ndi wachitatu Sama. 14Ndipo Davide anali wotsiriza; ndi akulu atatuwo anamtsata Saulo. 15#1Sam. 16.19Koma Davide akamuka kwa Saulo, nabwerera kudzadyetsa nkhosa za atate wake ku Betelehemu. 16Ndipo Mfilistiyo anayandikira m'mawa ndi madzulo, nadzionetsera masiku makumi anai.
17Ndipo Yese anati kwa Davide mwana wake, Uwatengere abale ako efa wa tirigu uyu wokazinga, ndi mikate iyi khumi, nuthamangire nazo kuzithando kwa abale ako; 18#Gen. 37.14nunyamule nchinchi izi khumi zamase ukapatse mtsogoleri wa chikwi chao, nukaone m'mene akhalira abale ako, nulandire chikole chao. 19Tsono Saulo, ndi iwowa, ndi anthu onse a Israele, anali m'chigwa cha Ela, ku nkhondo ya Afilisti. 20Ndipo Davide anauka m'mamawa, nasiyira nkhosa wozisungira, nasenza zija, namuka, monga anamuuza Yese; ndipo iye anafika ku linga la magaleta, napeza khamu lilikutuluka kunka poponyanira nkhondo lilikufuula. 21Ndipo Israele ndi Afilisti anandandalitsa nkhondo zao, khamu lina kuyang'anana ndi khamu lina. 22Ndipo Davide anasiya akatundu ake m'dzanja la wosungira akatundu, nathamangira ku khamulo, nadza nawalonjera abale ake. 23#1Sam. 17.8Ndipo m'mene iye anali chilankhulire nao, onani chinakwerako chiwindacho, Mfilisti wa ku Gati, dzina lake Goliyati, wotuluka pakati pa mipambo ya Afilisti, nalankhula monga mau omwe aja; ndipo Davide anawamva. 24Ndipo Aisraele onse, pakumuona munthuyo, anamthawa, naopa kwambiri. 25#Yos. 15.16; Miy. 16.15Nati Aisraele, Kodi mwaona munthu uyu amene anakwera kuno? Zoonadi iye anakwera kuti adzanyoze Israele, ndipo munthu wakumupha iye, mfumu idzamlemeza ndi chuma chambiri, nidzampatsa mwana wake wamkazi, nidzayesa nyumba ya atate wake yaufulu m'Israele. 26#1Sam. 17.10; Deut. 5.26; Mas. 42.2Ndipo Davide analankhula ndi anthu akuima pafupi ndi iye, nati, Adzamchitira chiyani munthu wakupha Mfilisti uyu, ndi kuchotsa tonzo lake pakati pa Israele? Pakuti Mfilisti uyu wosadulidwa ndiye yani, kuti azinyoza makamu a Mulungu wamoyo? 27Ndipo anthuwo anamyankha motero, nati, Adzamchitira munthu wakumupha iye mwakutimwakuti. 28#Gen. 37.4, 8, 11; Mat. 10.36Ndipo Eliabu mkulu wake anamumva iye alikulankhula ndi anthu; ndipo Eliyabu anapsa mtima ndi Davide, nati, Unatsikiranji kuno? Ndi nkhosa zija zowerengeka unazisiya ndi yani, m'chipululu muja? Ine ndidziwa kudzikuza kwako ndi kuipa kwa mtima wako; pakuti watsika kuti udzaone nkhondoyi. 29#1Sam. 17.17Ndipo Davide anati, Ndachitanji tsopano? Palibe chifukwa kodi? 30Napotolokera iye kwa munthu wina, nalankhula mau omwewo; ndipo anthu anamyankhanso monga momwemo. 31Ndipo pamene mau adanena Davide anamveka, anawapitiriza kwa Saulo; ndipo iye anamuitana. 32#Deut. 20.1, 3; 1Sam. 16.18Ndipo Davide anati kwa Saulo, Asade nkhawa munthu aliyense chifukwa cha iyeyo; ine kapolo wanu ndidzapita kuponyana ndi Mfilisti uyu. 33Ndipo Saulo anati kwa Davide, Sukhoza iwe kukomana ndi Mfilisti uyu kukaponyana naye; pakuti iwe ndiwe mnyamata, koma iye anazolowera nkhondo kuyambira ubwana wake. 34Ndipo Davide anati kwa Saulo, Ine kapolo wanu ndinalikusunga nkhosa za atate wanga; ndipo pakubwera mkango, mwina chimbalangondo ndi kutenga nkhosa ya gululo, 35ndinachithamangira, ndi kuchikantha, ndi kuitulutsa m'kamwa mwake; ndipo pamene chinandiukira, ndinagwira tchowa lake ndi kuchikantha ndi kuchipha. 36#1Sam. 17.10, 26Ine kapolo wanu ndinapha mkango ndi chimbalangondo zonse ziwiri; ndipo Mfilisti uyu wosadulidwa adzakhala ngati mmodzi wa izo, popeza wanyoza makamu a Mulungu wamoyo. 37#1Sam. 20.13; 2Ako. 1.10Nati Davide, Yehova wakundipulumutsa pa mphamvu ya mkango, ndi mphamvu ya chimbalangondo, Iyeyu adzandipulumutsa m'dzanja la Mfilisti uyu. Ndipo Saulo anati kwa Davide, Muka, Yehova akhale nawe. 38Ndipo Saulo anaveka Davide zovala zake za iye yekha, namveka chisoti chamkuwa pamutu pake, namvekanso malaya aunyolo. 39Ndipo Davide anamanga lupanga lake pamwamba pa zovala zake, nayesa kuyenda nazo; popeza sanaziyesera kale. Ndipo Davide anati kwa Saulo, Sindikhoza kuyenda ndi izi; pakuti sindinazizolowera. Nazivula Davide. 40Natenga ndodo yake m'dzanja lake nadzisankhira miyala isanu yosalala ya mumtsinje, naiika m'thumba la kubusa, limene anali nalo ndilo chibete; ndi choponyera miyala chinali m'dzanja lake, momwemo anayandikira kwa Mfilistiyo. 41Ndipo Mfilistiyo anadza, nayandikira kwa Davide; ndi wonyamula chikopa chake anamtsogolera. 42Ndipo Mfilisti pakumwazamwaza maso, ndi kuona Davide, anampeputsa; popeza anali mnyamata chabe, wofiirira, ndi wa nkhope yokongola. 43#1Sam. 24.14Ndipo Mfilisti anati kwa Davide, Ine ndine galu kodi, kuti iwe ukudza kwa ine ndi ndodo? Ndi Mfilistiyo anatukwana Davide natchula milungu yake. 44#1Maf. 20.10-11Ndipo Mfilistiyo anati kwa Davide, Idza kuno kwa ine, ndidzapatsa mnofu wako kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zilombo za kuthengo. 45#1Sam. 17.10; 2Sam. 22.33; Mas. 124.8; 2Ako. 10.4; Aheb. 11.33-34Ndipo Davide anati kwa Mfilistiyo, Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, ndi mkondo, ndi nthungo; koma ine ndafika kwa iwe m'dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israele amene iwe unawanyoza. 46#Yos. 4.24; 1Maf. 18.36Lero lino Yehova adzakupereka iwe m'dzanja langa, ndipo ndidzakukantha, ndi kukuchotsera mutu wako. Ndipo lero ndidzapatsa mitembo ya makamu a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zilombo za dziko lapansi; kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israele kuli Mulungu. 47#2Mbi. 20.15; Hos. 1.7Ndi msonkhano wonse uno udzazindikira kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga, kapena ndi mkondo; pakuti Yehova ndiye mwini nkhondo, ndipo Iye adzakuperekani inu m'manja athu. 48Ndipo kunali, pamene Mfilistiyo anadzikonza, nadza, nasendera pafupi kuti akomane ndi Davide, Davide anafulumira, nathamangira ku khamulo, kuti akomane ndi Mfilistiyo. 49Ndipo Davide anapisa dzanja lake m'thumba mwake, natulutsamo mwala, nauponya, nalasa Mfilistiyo pamphumi; ndi mwalawo unalowa m'mphumi, ndipo iye anagwa pansi chafufumimba. 50Chomwecho Davide anapambana Mfilistiyo ndi mwala wa choponyera chake, nakantha Mfilistiyo, namupha. Koma m'dzanja la Davide munalibe lupanga. 51Potero Davide anathamanga naima pa Mfilistiyo, nagwira lupanga lake, nalisolola m'chimake, namtsiriza nadula nalo mutu wake. Ndipo pakuona Afilisti kuti chiwinda chao chidafa, anathawa. 52Ndipo anthu a Israele ndi Ayuda ananyamuka, nafuula, nathamangira Afilistiwo, mpaka ufika kuchigwako, ndi ku zipata za Ekeroni. Ndipo Afilistiwo olasidwa anagwa pa njira ya ku Saaraimu, kufikira ku Gati ndi ku Ekeroni. 53Ndipo ana a Israele atathamangira Afilisti, anabwerera nafunkha za m'zithando zao. 54Ndipo Davide anatenga mutu wa Mfilistiyo, napita nao ku Yerusalemu; koma zida zake anazisunga m'hema wake. 55Ndipo pamene Saulo anaona Davide alikutulukira kwa Mfilistiyo, iye anati kwa Abinere, kazembe wa khamu la nkhondo, Abinere, mnyamata uyu ndi mwana wa yani? Nati Abinere, Pali moyo wanu, mfumu, ngati ndidziwa. 56Ndipo mfumu inati, Ufunsire kuti mnyamatayo ndi mwana wa yani. 57#1Sam. 17.54Ndipo pamene Davide anabwera, atapha Mfilistiyo, Abinere anamtenga, nafika naye pamaso pa Saulo, mutu wa Mfilistiyo uli m'dzanja lake. 58#Rut. 4.17Ndipo Saulo anati kwa iye, Mnyamata iwe, ndiwe mwana wa yani? Davide nayankha, Ndili mwana wa kapolo wanu Yese wa ku Betelehemu.
Currently Selected:
1 SAMUELE 17: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi