1 SAMUELE 19
19
Yonatani anenera Davide kwa Saulo
1Ndipo Saulo analankhula kwa Yonatani mwana wake, ndi anyamata ake onse kuti amuphe Davide. 2#1Sam. 18.1Koma Yonatani mwana wa Saulo anakondwera kwambiri ndi Davide. Ndipo Yonatani anauza Davide, nati, Saulo atate wanga alikufuna kukupha; chifukwa chake tsono uchenjere m'mawa, mukhale m'malo mosadziwika, nubisale; 3ndipo ine ndidzakutuluka ndi kuima pa mbali ya atate wanga kumunda kumene kuli iwe, ndipo ndidzalankhula ndi atate wanga za iwe; ndipo ndikaona kanthu ndidzakudziwitsa. 4#Gen. 42.22; Mas. 35.12Ndipo Yonatani analankhula ndi Saulo atate wake movomereza Davide, nanena naye, Mfumu asachimwire mnyamata wake Davide; chifukwa iyeyo sanachimwire inu, ndipo ntchito zake anakuchitirani zinali zabwino ndithu; 5#Ower. 12.3; 1Mbi. 11.14; Mat. 27.4popeza iye anataya moyo wake nakantha Mfilistiyo, ndipo Yehova anachitira Aisraele onse chipulumutso chachikulu, inu munachiona, nimunakondwera; tsono mudzachimwiranji mwazi wosalakwa, ndi kumupha Davide popanda chifukwa? 6Ndipo Saulo anamvera mau a Yonatani; nalumbira, Pali Yehova, sadzaphedwa iye. 7Pamenepo Yonatani anaitana Davide, namuuza zonsezi. Ndipo Yonatani anafika naye Davide kwa Saulo, iye nakhalanso pamaso pake monga kale.
Saulo afuna kupha Davide, Mikala ampulumutsa
8Ndipo kunalinso nkhondo; ndipo Davide anatuluka, nakamenyana ndi Afilisti, nawapha ndi maphedwe akulu, ndipo iwo anamthawa iye. 9#1Sam. 16.14Ndipo mzimu woipa wochokera kwa Yehova unali pa Saulo, pakukhala iye m'nyumba mwake, ndi mkondo wake m'dzanja lake; ndipo Davide anaimba ndi dzanja lake. 10Ndipo Saulo anayesa kupyoza Davide kumphatikiza kukhoma ndi mkondowo; koma iye anadzilanditsa kuchoka pamaso pa Saulo; ndipo analasa khoma; ndipo Davide anathawa napulumuka usiku uja. 11Ndipo Saulo anatumiza mithenga kunyumba ya Davide imdikire, ndi kumupha m'mawa; koma Mikala mkazi wa Davide anamuuza, nati, Ukapanda kupulumutsa moyo wako usiku uno, udzaphedwa ndithu m'mawa. 12#Yos. 2.15Chomwecho Mikala anamtsitsira Davide pazenera, namuka iye, nathawa, napulumuka. 13Ndipo Mikala anatenga chifanizo nachiika pakama, naika mtsamiro wa ubweya wa mbuzi kumutu kwake, nachifunda zofunda. 14Ndipo pamene Saulo anatumiza mithenga kuti ikamgwire Davide, anati, Iye alikudwala. 15Ndipo Saulo anatumiza mithengayo kuti ikaone Davide, nati, Mumtengere iye pa kama wake, kuti ndidzamuphe. 16Ndipo pakulowa mithengayo, onani, pakama pali chifanizo ndi mtsamiro wa ubweya wa mbuzi kumutu kwake. 17#2Sam. 2.22Nati Saulo kwa Mikala, Wandinyengeranji chomwechi, ndi kulola mdani wanga apulumuke? Ndipo Mikala anayankha Saulo, Iye anati kwa ine, Undilole ndipite, ndingakuphe.
Saulo ndi amithenga ake anenera
18Chomwecho anathawa Davide, napulumuka, nafika kwa Samuele ku Rama, namuuza zonse Saulo anamchitira. Ndipo iye ndi Samuele anakhala ku Nayoti. 19Ndipo wina anauza Saulo, kuti, Onani Davide ali ku Nayoti m'Rama. 20#Yoh. 7.32, 45Ndipo Saulo anatumiza mithenga kuti igwire Davide, ndipo pamene inaona gulu la aneneri alikunenera, ndi Samuele mkulu wao alikuimapo, mzimu wa Mulungu unagwera mithenga ya Saulo, ninenera iyonso. 21#Num. 11.25; Yow. 2.28Ndipo pamene anauza Saulo, iye anatumiza mithenga ina; koma iyonso inanenera. Ndipo Saulo anatumiza mithenga kachitatu, nayonso inanenera. 22Pamenepo iyenso anamuka ku Rama, nafika ku chitsime chachikulu chili ku Seku, nafunsa nati, Samuele ndi Davide ali kuti? Ndipo wina anati, Taonani, ali ku Nayoti m'Rama. 23#1Sam. 10.10Ndipo anapita komweko ku Nayoti m'Rama; ndi mzimu wa Mulungu unamgwera iyenso; ndipo anapitirira, nanenera, mpaka anafika ku Nayoti m'Rama. 24#1Sam. 10.11; Yes. 20.2Ndiponso anavula zovala zake, naneneranso pamaso pa Samuele, nagona wamaliseche usana womwe wonse, ndi usiku womwe wonse. Chifukwa chake amati, Kodi Saulonso ali pakati pa aneneri?
Currently Selected:
1 SAMUELE 19: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi