YouVersion Logo
Search Icon

1 PETRO 5

5
Zoyenera akulu ndi anyamata; adzichepetse, adikire
1 # Luk. 24.48; Mac. 1.8, 22; Aro. 8.17-18 Akulu tsono mwa inu ndiwadandaulira, ine mkulu mnzanu ndi mboni ya zowawa za Khristu, ndinenso wolawana nao ulemerero udzavumbulutsikawo: 2#Yoh. 21.15-17; 1Ako. 9.17; 1Tim. 3.3, 8Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu; 3#Mat. 20.25-26; Afi. 3.17osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo. 4#1Ako. 9.25Ndipo pakuonekera Mbusa wamkulu, mudzalandira korona wa ulemerero, wosafota. 5#Aro. 12.10; Yak. 4.6Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa. 6#Yak. 4.10Potero dzichepetseni pansi pa dzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni; 7#Mat. 6.25ndi kutaya pa Iye nkhawa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu. 8#Luk. 22.31Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire: 9#Mac. 14.22; Yak. 4.7ameneyo mumkanize okhazikika m'chikhulupiriro, podziwa kuti zowawa zomwezo zilimkukwaniridwa pa abale anu ali m'dziko. 10#1Ako. 1.9; 2Ate. 2.17; Aheb. 13.21Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu. 11#1Pet. 4.11Kwa Iye kukhale mphamvu kunthawi za nthawi. Amen.
12 # 1Ako. 15.1; 2Ako. 1.19 Mwa Silivano, mbale wathu wokhulupirika monga ndimayesa, ndalembera kwa inu mwachidule, ndi kudandaulira, ndi kuchita umboni, kuti chisomo choona cha Mulungu ndi ichi; m'chimenechi muimemo. 13#Mac. 12.12, 25Iye wa ku Babiloni wosankhidwa pamodzi nanu akulankhulani; ateronso Marko mwana wanga. 14#Aro. 16.16; Aef. 6.23Mupatsane moni ndi chipsompsono cha chikondi.
Mtendere ukhale ndi inu nonse muli mwa Khristu.

Currently Selected:

1 PETRO 5: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in