YouVersion Logo
Search Icon

1 PETRO 4

4
1 # Akol. 3.3, 5; 1Pet. 3.18 Popeza Khristu adamva zowawa m'thupi, mudzikonzere mtima womwewo; pakuti iye amene adamva zowawa m'thupi walekana nalo tchimo; 2#Agal. 2.20kuti nthawi yotsalira simukakhalenso ndi moyo m'thupi kutsata zilakolako za anthu, koma chifuniro cha Mulungu. 3#Aef. 2.2Pakuti nthawi yapitayi idatifikira kuchita chifuno cha amitundu, poyendayenda ife m'kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, maimwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka; 4m'menemo ayesa nchachilendo kuti simuthamanga nao kufikira kusefukira komwe kwa chitayiko, nakuchitirani mwano; 5#Mac. 10.42amenewo adzamwerengera Iye wokhala wokonzeka kuweruza amoyo ndi akufa. 6#1Pet. 3.19Pakuti chifukwa cha ichi walalikidwa Uthenga Wabwino kwa iwonso adafawo, kuti akaweruzidwe monga mwa anthu m'thupi, koma akakhale ndi moyo monga mwa Mulungu mumzimu.
7 # Mat. 24.13-14; Akol. 4.2 Koma chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi; chifukwa chake khalani anzeru, ndipo dikirani m'mapemphero; 8#1Ako. 13.5-7; Akol. 3.14koposa zonse mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha; pakuti chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo; 9#Aro. 12.13mucherezane wina ndi mnzake, osadandaula: 10monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu; 11#Aro. 12.6-8; Aef. 5.20akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, achite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m'zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu, amene ali nao ulemerero ndi mphamvu kunthawi za nthawi. Amen.
12 # 1Ako. 3.13 Okondedwa, musazizwe ndi mayesedwe amoto adakugwerani inu akhale chakukuyesani, ngati chinthu chachilendo chachitika nanu: 13#Aro. 8.17-18; Afi. 3.10koma popeza mulawana ndi Khristu zowawa zake, kondwerani: kutinso pa vumbulutso la ulemerero wake mukakondwere kwakukulukulu. 14#2Ako. 12.10Mukatonzedwa pa dzina la Khristu, odala inu; pakuti Mzimu wa ulemerero, ndi Mzimu wa Mulungu apuma pa inu. 15#1Pet. 2.20Pakuti asamve zowawa wina wa inu ngati wambanda, kapena mbala, kapena wochita zoipa, kapena ngati wodudukira; 16#Mac. 5.41koma akamva zowawa ngati mkhristu asachite manyazi; koma alemekeze Mulungu m'dzina ili. 17#Yer. 25.29; Mala. 3.5Chifukwa yafika nthawi kuti chiweruziro chiyambe pa nyumba ya Mulungu; koma ngati chiyamba ndi ife, chitsiriziro cha iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu chidzakhala chiyani? 18#Luk. 23.31Ndipo ngati munthu wolungama apulumuka ndi kuyesetsa kokhakokha, munthu wosapembedza ndi wochimwa adzaoneka kuti? 19#2Tim. 1.12Koteronso iwo akumva zowawa monga mwa chifuniro cha Mulungu aike moyo wao ndi kuchita zokoma m'manja a Wolenga wokhulupirika.

Currently Selected:

1 PETRO 4: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in