1 PETRO 3
3
Zoyenera akazi ndi amuna
1 #
Gen. 3.16; 1Ako. 9.22; Akol. 3.18 Momwemonso, akazi inu, mverani amuna anu a inu nokha; kuti, ngatinso ena samvera mau, akakodwe opanda mau mwa mayendedwe a akazi; 2pakuona mayendedwe anu oyera ndi kuopa kwanu. 3#1Tim. 2.9Amene kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kuvala za golide, kapena kuvala chovala; 4#Zef. 2.3koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu. 5Pakuti koteronso kale akazi oyera mtima, akuyembekezera Mulungu, anadzikometsera okha, namvera amuna ao a iwo okha; 6monga Sara anamvera Abrahamu, namutcha iye mbuye; ameneyo mukhala ana ake ngati muchita bwino, osaopa choopsa chilichonse.
7 #
Mat. 5.23-24; Aef. 5.25 Momwemonso amuna inu, khalani nao monga mwa chidziwitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu, monganso wolowa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.
Za chikondano. Za kulola masautso monga anachita Ambuye
8 #
Aro. 12.10, 16 Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa; 9#Mat. 5.39osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ichi mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso. 10#Mas. 34.12-16Pakuti,
Iye wofuna kukonda moyo,
ndi kuona masiku abwino,
aletse lilime lake lisanene choipa,
ndi milomo yake isalankhule chinyengo;
11 #
Mas. 34.12-16
ndipo apatuke pachoipa, nachite chabwino;
afunefune mtendere ndi kuulondola.
12 #
Mas. 34.12-16
Pakuti maso a Ambuye ali pa olungama,
ndi makutu ake akumva pembedzo lao;
koma nkhope ya Ambuye ili pa ochita zoipa.
13 #
Aro. 8.28
Ndipo ndani iye amene adzakuchitirani choipa, ngati muchita nacho changu chinthu chabwino? 14#Mat. 5.10-12Komatu ngatinso mukumva zowawa chifukwa cha chilungamo, odala inu; ndipo musaope pakuwaopa iwo, kapena musadere nkhawa; 15#Mas. 119.46; Mac. 4.8koma mumpatulikitse Ambuye Khristu m'mitima yanu; okonzeka nthawi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha; 16#Tit. 2.8ndi kukhala nacho chikumbu mtima chabwino, kuti umo akunenerani, iwo akunenera konama mayendedwe anu abwino m'Khristu akachitidwe manyazi. 17Pakuti, kumva zowawa chifukwa cha kuchita zabwino, ndi kumva zowawa chifukwa cha kuchita zoipa, nkwabwino kumva zowawa chifukwa cha kuchita zabwino, ngati chitero chifuniro cha Mulungu. 18#Aro. 5.6Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu; 19#1Pet. 4.6m'menemonso anapita, nalalikira mizimu inali m'ndende, 20#Gen. 6—7imene inakhala yosamvera kale, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira, m'masiku a Nowa, pokhala m'kukonzeka chingalawa, m'menemo owerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi; 21#Aef. 5.26; 1Pet. 1.3chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbu mtima chokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Khristu; 22#Aheb. 1.3amene akhala pa dzanja lamanja la Mulungu, atalowa m'Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zonse zimgonjera.
Currently Selected:
1 PETRO 3: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi