YouVersion Logo
Search Icon

1 PETRO 2

2
1 # Akol. 3.8 Momwemo pakutaya choipa chonse, ndi chinyengo chonse, ndi maonekedwe onyenga, ndi kaduka, ndi masinjiriro onse, 2#1Ako. 3.1-2lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda chinyengo, kuti mukakule nao kufikira chipulumutso; 3ngati mwalawa kuti Ambuye ali wokoma mtima; 4#Mas. 118.22amene pakudza kwa Iye, mwala wamoyo, wokanidwatu ndi anthu, koma ndi Mulungu wosankhika, waulemu, 5#Yes. 61.6; Aro. 12.1; Aef. 2.21-22inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Khristu. 6#Yes. 28.16Chifukwa kwalembedwa m'lembo,
Taona, ndiika m'Ziyoni mwala wotsiriza wa pangodya,
wosankhika, wa mtengo wake;
ndipo wokhulupirira Iye sadzanyazitsidwa.
7 # Mas. 118.22 Kwa inu tsono akukhulupirira, ali wa mtengo wake; koma kwa iwo osakhulupirira,
Mwala umene omangawo anaukana,
womwewo unayesedwa mutu wa pangodya.
8 # Yes. 8.14; Luk. 2.34 Ndipo,
Mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lophunthwitsa.
Kwa iwo akukhumudwa ndi mau, pokhala osamvera, kumenekonso adaikidwako.
9 # Eks. 19.5-6; Deut. 10.15 Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa; 10#Aro. 9.5, 25inu amene kale simunali anthu, koma tsopano muli anthu a Mulungu; amene kale simunalandira chifundo, koma tsopano mwalandira chifundo.
Za mayendedwe ao pakati pa akunja. Agonje kwa akulu
11 # Agal. 5.24 Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo; 12#Mat. 5.16; Aro. 12.17ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira.
13 # Mat. 22.21 Tadzigonjani kwa zoikika zonse za anthu, chifukwa cha Ambuye; ngakhale kwa mfumu, monga mutu wa onse; 14#Aro. 13.4kapena kwa akazembe, monga otumidwa ndi iye kukalanga ochita zoipa, koma kusimba ochita zabwino. 15#Tit. 2.7-8Pakuti chifuniro cha Mulungu chitere, kuti ndi kuchita zabwino mukatontholetse chipulukiro cha anthu opusa; 16#Agal. 5.1, 13monga mfulu, koma osakhala nao ufulu monga chobisira choipa, koma ngati akapolo a Mulungu. 17#Miy. 24.21; Afi. 2.3; Aheb. 13.1Chitirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Opani Mulungu, Chitirani mfumu ulemu.
Zoyenera anyamata Akhristu
18 # Aef. 6.5 Anyamata inu, gonjerani ambuye anu ndi kuopa konse, osati abwino ndi aulere okha, komanso aukali. 19#1Pet. 3.14Pakuti ichi ndi chisomo ngati munthu, chifukwa cha chikumbumtima pa Mulungu alola zachisoni, pakumva zowawa wosaziyenera. 20#1Pet. 4.14-16Pakuti mbiri yokoma yanji, mukapirira pochimwa ndi kubwanyulidwapo? Komatu, ngati pochita zabwino, ndi kumvako ndiko chisomo pa Mulungu. 21#Yoh. 13.15; 1Pet. 3.18Pakuti kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Khristu anamva zowawa m'malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake; 22#Yes. 53.9; Yoh. 8.46amene sanachita tchimo, ndipo m'kamwa mwake sichinapezedwa chinyengo; 23#Yes. 53.7; Yoh. 8.48-49; Luk. 23.46amene pochitidwa chipongwe sanabwezera chipongwe, pakumva zowawa, sanaopsa, koma anapereka mlandu kwa Iye woweruza kolungama; 24#Yes. 53.5; Mat. 8.17; Aro. 6.2, 11, 13amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo. 25#Yes. 53.6; Yoh. 10.11, 14, 16Pakuti munalikusochera ngati nkhosa; koma tsopano mwabwera kwa Mbusa ndi Woyang'anira wa moyo wanu.

Currently Selected:

1 PETRO 2: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in