YouVersion Logo
Search Icon

1 PETRO 1

1
1 # Yak. 1.1 Petro, mtumwi wa Yesu Khristu, kwa osankhidwa akukhala alendo a chibalaliko a ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya, ndi Bitiniya, 2#Aro. 8.29; 2Ate. 2.13; Aheb. 10.22monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'chiyeretso cha Mzimu, chochitira chimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Khristu: Chisomo, ndi mtendere zichulukire inu.
Chiyamiko chifukwa cha chipulumutso
3 # 1Ako. 15.20; Tit. 3.5 Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu; 4#Aro. 8.17; 1Pet. 5.4kuti tilandire cholowa chosavunda ndi chosadetsa ndi chosafota, chosungikira m'Mwamba inu, 5#Yoh. 10.28-29amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa chikhulupiriro, kufikira chipulumutso chokonzeka kukavumbulutsidwa nthawi yotsiriza. 6#Yak. 1.2M'menemo mukondwera, kungakhale tsopano kanthawi, ngati kuyenera, mukachitidwe chisoni ndi mayesero a mitundumitundu, 7#1Ako. 3.13; 2Ate. 1.7-12; Yak. 1.3, 12kuti mayesedwe a chikhulupiriro chanu, ndiwo a mtengo wake woposa wa golide amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa vumbulutso la Yesu Khristu; 8#Yoh. 20.29; 1Yoh. 4.20amene mungakhale simunamuona mumkonda; amene mungakhale simumpenya tsopano, pokhulupirira, mukondwera naye ndi chimwemwe chosaneneka, ndi cha ulemerero: 9#Aro. 6.22ndi kulandira chitsiriziro cha chikhulupiriro chanu, ndicho chipulumutso cha moyo wanu. 10#Dan. 2.44Kunena za chipulumutso ichi anafunafuna nasanthula aneneri, pakunenera za chisomo chikudzerani; 11#Mas. 22; Yes. 53ndi kusanthula nthawi yiti, kapena nthawi yanji Mzimu wa Khristu wokhala mwa iwo analozera, pakuchitiratu umboni wa masautso a Khristu, ndi ulemerero wotsatana nao. 12#Dan. 9.24Kwa iwo amene kudavumbulutsidwa, kuti sanadzitumikira iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.
Awadandaulira atsate kuyera mtima
13 # Luk. 21.34 Mwa ichi, podzimanga m'chuuno, kunena za mtima wanu, mukhale odzisunga, nimuyembekeze konsekonse chisomo chilikutengedwa kudza nacho kwa inu m'vumbulutso la Yesu Khristu; 14#Aro. 12.2monga ana omvera osadzifanizitsanso ndi zilakolako zakale, pokhala osadziwa inu; 15#2Ako. 7.1komatu monga Iye wakuitana inu ali woyera mtima, khalani inunso oyera mtima m'makhalidwe anu onse; 16#Lev. 11.44popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima. 17#Aro. 2.11Ndipo mukamuitana ngati Atate, Iye amene aweruza monga mwa ntchito ya yense, wopanda tsankho, khalani ndi mantha nthawi ya chilendo chanu; 18#1Ako. 6.20podziwa kuti simunaomboledwa ndi zovunda, golide ndi siliva, kusiyana nao makhalidwe anu achabe ochokera kwa makolo anu: 19#Eks. 12.5; Yes. 53.7; Mac. 20.28koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali monga wa mwanawankhosa wopanda chilema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Khristu: 20#Aro. 3.25; 16.25-26amene anazindikirikatu lisanakhazikike dziko lapansi, koma anaonetsedwa pa chitsiriziro cha nthawi, 21#Mac. 2.24chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu wakumuukitsa Iye kwa akufa, ndi kumpatsa Iye ulemerero; kotero kuti chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu chikhale pa Mulungu. 22#Mac. 15.9; Aro. 12.9-10Popeza mwayeretsa moyo wanu pakumvera choonadi kuti mukakonde abale ndi chikondi chosanyenga, mukondane kwenikweni kuchokera kumtima; 23#Yoh. 1.13; 3.5; Yak. 1.18inu amene mudabadwanso, osati ndi mbeu yofeka, komatu yosaola, mwa mau a Mulungu amoyo ndi okhalitsa. 24#Mas. 103.15Popeza,
Anthu onse akunga udzu,
ndi ulemerero wao wonse ngati duwa la udzu.
Udzuwo ungofota, ndi duwa lake lingogwa;
25 # Yes. 40.6-8; 1Yoh. 1.1, 3 koma Mau a Mulungu akhala chikhalire.
Ndipo mau olalikidwa kwa inu ndi awo.

Currently Selected:

1 PETRO 1: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in