YouVersion Logo
Search Icon

2 PETRO Mau Oyamba

Mau Oyamba
Kalata yachiwiri ya Petro kwa gulu lalikulu la akhristu oyambirira. Cholinga chenicheni cha kalatayi ndicho kulimbana ndi zonena za aphunzitsi onyenga ndi makhalidwe oipa amene amabwera chifukwa cha chiphunzitsochi. Yankho lake la mavutowa lipezeka pogwiritsitsa chidziwitso chenicheni cha Mulungu ndi cha Ambuye Yesu Khristu. Chidziwitso chimenechi chinaperekedwa ndi anthu amene iwo eni adamuona Yesu chamaso namumva iye akulalikira. Wolembayo akukhudzidwa makamaka ndi chiphunzitso chakuti Khristu sadzabweranso. Iye akunena kuti kuchedwa kubweranso kwa Khristu ndi chifukwa chakuti, “Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.” (3.9)
Za mkatimu
Mau oyamba 1.1-2
Maitanidwe a Chikhristu 1.3-21
Aphunzitsi onyenga 2.1-22
Kubweranso komaliza kwa Khristu 3.1-18

Currently Selected:

2 PETRO Mau Oyamba: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in