YouVersion Logo
Search Icon

2 PETRO 1

1
1 # Aro. 1.12 Simoni Petro, kapolo ndi mtumwi wa Yesu Khristu kwa iwo amene adalandira chikhulupiriro cha mtengo wake womwewo ndi ife, m'chilungamo cha Mulungu wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu: 2#Dan. 4.1; 6.25; 1Pet. 1.2Chisomo kwa inu ndi mtendere zichulukitsidwe m'chidziwitso cha Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu.
Atsate zokoma za Chikhristu
3 # Yoh. 17.3 Popeza mphamvu ya umulungu wake idatipatsa ife zonse za pamoyo ndi chipembedzo, mwa chidziwitso cha Iye amene adatiitana ife ndi ulemerero ndi ukoma wake wa Iye yekha; 4#2Ako. 7.1; 3.18; 2Pet. 2.20mwa izi adatipatsa malonjezano a mtengo wake ndi akulu ndithu; kuti mwa izi mukakhale oyanjana nao umulungu wake, mutapulumuka kuchivundi chili pa dziko lapansi m'chilakolako. 5Ndipo mwa ichi chomwe, pakutengeraponso changu chonse, muonjezerapo ukoma pa chikhulupiriro chanu, ndi paukoma chizindikiritso; ndi pachizindikiritso chodziletsa; 6ndi pachodziletsa chipiriro; 7ndi pachipiriro chipembedzo; ndi pachipembedzo chikondi cha pa abale; ndi pachikondi cha pa abale chikondi. 8#Tit. 3.14Pakuti izi zikakhala ndi inu, ndipo zikachuluka, zidzachita kuti musakhale aulesi kapena opanda zipatso pa chizindikiritso cha Ambuye Yesu Khristu. 9#1Yoh. 2.9, 11Pakuti iye wakusowa izi ali wakhungu, wa chimbuuzi, woiwala matsukidwe ake potaya zoipa zake zakale. 10#1Yoh. 3.19Momwemo abale, onjezani kuchita changu kukhazikitsa maitanidwe ndi masankhulidwe anu; pakuti mukachita izi, simudzakhumudwa nthawi zonse; 11pakuti kotero kudzaonjezedwa kwa inu kolemerera khomo lakulowa ufumu wosatha wa Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu.
12 # Afi. 3.1; 2Pet. 3.1 Mwa ichi sindidzaleka kukukumbutsani inu nthawi zonse za izi, mungakhale muzidziwa nimukhazikika m'choonadi chili ndi inu. 13#Afi. 3.1; 2Pet. 3.1Ndipo ndichiyesa chokoma, pokhala ine m'msasa uwu, kukutsitsimutsani ndi kukukumbutsani; 14#Yoh. 21.18-19; 2Tim. 4.6podziwa kuti kuleka kwa msasa wanga kuli pafupi, monganso Ambuye wathu Yesu Khristu anandilangiza. 15Koma ndidzachitanso changu kosalekeza kuti nditachoka ine, mudzakhoza kukumbukira izi. 16#Mat. 17.1; 2Ako. 4.2Pakuti sitinatsata miyambi yachabe, pamene tinakudziwitsani mphamvu ndi maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Khristu, koma tinapenya m'maso ukulu wake. 17#Mat. 3.17Pakuti analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumdzera Iye mau otere ochokera ku ulemerero waukulu, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene Ine ndikondwera naye; 18#Mat. 17.6ndipo mau awa ochokera Kumwamba tidawamva ife, pokhala pamodzi ndi Iye m'phiri lopatulika lija. 19#Yoh. 5.35; Chiv. 2.28Ndipo tili nao mau a chinenero okhazikika koposa; amene muchita bwino powasamalira, monga nyali younikira m'malo a mdima, kufikira kukacha, nikauka nthanda pa mtima yanu; 20#Aro. 12.6ndi kudziwa ichi poyamba, kuti palibe chinenero cha lembo chitanthauzidwa pa chokha, 21#2Sam. 23.2; 1Pet. 1.11pakuti kale lonse chinenero sichinadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.

Currently Selected:

2 PETRO 1: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in