1 MAFUMU 11
11
Solomoni adzipereka kupembedza mafano, Mulungu aipidwa naye
1 #
Neh. 13.26
Ndipo mfumu Solomoni anakonda akazi ambiri achilendo, pamodzi ndi mwana wamkazi wa Farao, akazi a ku Mowabu, ndi a ku Amoni, ndi a ku Edomu, ndi a ku Sidoni, ndi Ahiti; 2#Eks. 34.16a mitundu ija Yehova adanena ndi ana a Israele za iwo, kuti, Inu musakalowa kwa iwo, ndipo iwo asadzalowe kwa inu; zedi adzatembenuza mitima yanu kutsata milungu yao; amenewo Solomoni anawaumirira kuwakonda. 3Ndipo anali nao akazi mazana asanu ndi awiri, ana akazi a mafumu, ndi akazi aang'ono mazana atatu; ndipo akazi ake anapambutsa mtima wake. 4#Deut. 17.17Ndipo kunali, atakalamba Solomoni, akazi ake anapambutsa mtima wake atsate milungu ina; ndipo mtima wake sunakhala wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide atate wake. 5#2Maf. 23.13Tsono Solomoni anatsata Asitoreti fano la anthu a Sidoni, ndi Milikomu fano lonyansitsa la Aamoni. 6Ndipo Solomoni anachita choipa pamaso pa Yehova, osatsata Yehova ndi mtima wonse monga Davide atate wake. 7Pamenepo Solomoni anamangira Kemosi fano lonyansitsa la Amowabu ndi Moleki fano lonyansitsa la ana a Amoni misanje, pa phiri lili patsogolo pa Yerusalemu. 8Ndipo momwemo anachitiranso akazi ake onse achilendo, amene amafukizira naphera nsembe mafano ao.
9 #
1Maf. 3.5; 9.2; 11.2-3 Ndipo Yehova anakwiya ndi Solomoni, pokhala mtima wake unapatuka kwa Yehova Mulungu wa Israele, amene adamuonekera kawiri, 10#1Maf. 6.12; 9.6namlamulira za chinthu chomwechi, kuti asatsate milungu ina, koma iye sanasunge chimene Yehova anachilamula. 11#1Maf. 11.31; 1Maf. 12.15-16Chifukwa chake Yehova ananena ndi Solomoni, Popeza chinthu ichi chachitika ndi iwe, ndipo sunasunga chipangano changa ndi malemba anga amene ndinakulamulira, zedi, ndidzakung'ambira ufumu ndi kuupatsa mnyamata wako. 12Koma m'masiku ako sindidzatero chifukwa cha Davide atate wako, koma ndidzaung'ambira m'manja mwa mwana wako; 13#2Sam. 7.15; 1Maf. 12.20komatu sindidzachotsa ufumu wonsewo; fuko limodzi ndidzapatsa mwana wako, chifukwa cha Davide mtumiki wanga, ndi chifukwa cha Yerusalemu amene ndinamsankha.
Mulungu amuutsira Solomoni adani
14Ndipo Yehova anamuutsira Solomoni mdani, ndiye Hadadi Mwedomu; iyeyo anali wa mbumba ya mfumu ya ku Edomu. 15Pakuti pamene Davide adali m'Edomu, ndipo Yowabu kazembe wa nkhondo adanka kukaika akufawo, atapha amuna onse m'Edomu; 16pakuti Yowabu ndi Aisraele onse anakhalako miyezi isanu ndi umodzi, mpaka atawapha amuna onse m'Edomu; 17Hadadi uja anathawa, iyeyo ndi a ku Edomu ena, akapolo a atate wake pamodzi naye, kunka ku Ejipito, Hadadiyo akali mwana. 18Ndipo anachoka ku Midiyani nafika ku Parani, natenga anthu a ku Parani pamodzi nao, nafika ku Ejipito kwa Farao mfumu ya Aejipito, ameneyo anampatsa nyumba, namnenera zakudya, nampatsako dziko. 19Ndipo Farao anamkomera mtima ndithu Hadadiyo, nampatsa mkazi ndiye mbale wa mkazi wake, mbale wake wa Tapenesi mkazi wamkulu wa mfumu. 20Ndipo mbale wa Tapenesi anamuonera Genubati mwana wake, ameneyo Tapenesi anamletsera kuyamwa m'nyumba ya Farao, ndipo Genubati anakhala m'banja la Farao pamodzi ndi ana amuna a Farao. 21Ndipo atamva Hadadi ku Ejipito kuti Davide anagona ndi makolo ake, ndi kuti Yowabu kazembe wa nkhondo adafanso, Hadadi ananena ndi Farao, Mundilole ndimuke ku dziko la kwathu. 22Tsono Farao anati kwa iye, Koma chikusowa iwe nchiyani kwa ine, kuti ufuna kumuka ku dziko la kwanu? Nayankha iye, Palibe kanthu, koma mundilole ndimuke ndithu.
23 #
2Sam. 8.3
Ndipo Mulungu anamuutsira mdani wina, ndiye Rezoni mwana wa Eliyada, amene adathawa mbuye wake Hadadezere mfumu ya ku Zoba. 24Iye nasonkhanitsa anthu, nakhala kazembe wa nkhondo, muja Davide anawapha a ku Zobawo, napita ku Damasiko, nakhala komweko, nakhala mfumu ya ku Damasiko. 25Ndipo iye anali mdani wa Israele masiku onse a Solomoni, kuonjezerapo choipa anachichita Hadadi, naipidwa nao Aisraele, nakhala mfumu ya ku Aramu.
Mneneri Ahiya agawira Yerobowamu ufumuwo
26 #
2Mbi. 13.6
Ndipo Yerobowamu mwana wa Nebati Mwefuremu wa ku Zereda mnyamata wa Solomoni, dzina la amake ndiye Zeruya, mkazi wamasiye, iyenso anakweza dzanja lake pa mfumu. 27Ndipo chifukwa chakukweza iye dzanja lake pa mfumu ndi chimenechi: Solomoni anamanga Milo, namanganso pogumuka pa linga la mudzi wa Davide atate wake. 28Ndipo munthu ameneyo Yerobowamu anali ngwazi; ndipo pamene Solomoni anamuona mnyamatayo kuti ngwachangu, anamuika akhale woyang'anira wa ntchito yonse ya nyumba ya Yosefe. 29#1Maf. 12.15Ndipo kunali nthawi yomweyo kuti Yerobowamu anatuluka m'Yerusalemu, ndipo mneneri Ahiya wa ku Silo anampeza m'njira; tsono iyeyo anavaliratu chovala chatsopano, ndipo iwo awiri anali okha kuthengo, 30#1Sam. 15.27Ndipo Ahiyayo anagwira chovala chake chatsopano, naching'amba khumi ndi pawiri. 31#1Maf. 11.11, 13Nati kwa Yerobowamu, Takwaya magawo khumi; popeza atero Yehova Mulungu wa Israele, Taona ndidzaung'amba ufumu m'dzanja la Solomoni ndi kukupatsa iwe mafuko khumi. 32Koma iye adzakhala nalo fuko limodzi, chifukwa cha Davide mtumiki wanga, ndi cha Yerusalemu, mudzi umene ndinausankha m'mafuko onse a Israele. 33#1Maf. 11.5-7Nditero popeza iwo anandisiya, napembedza Asitoreti mulungu wa Asidoni, ndi Kemosi mulungu wa Amowabu, ndi Milikomu mulungu wa ana a Amoni, osayenda m'njira zanga, kuchita chimene chiyenera pamaso panga, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga, monga umo anatero Davide atate wake. 34Koma sindidzalanda ufumu wonse m'dzanja lake, koma ndidzamkhalitsa mfumu masiku ake onse, chifukwa cha Davide mtumiki wanga amene uja ndinamsankha, chifukwa kuti anasunga malamulo anga ndi malemba anga. 35Koma ndidzalanda ufumu m'dzanja la mwana wake, ndi kupatsa iwe mafuko khumi amene. 36#2Sam. 21.17; 1Maf. 11.32; 15.4Ndipo ndidzamninkha mwana wake fuko limodzi, kuti Davide mtumiki wanga akhale chikhalire ndi nyali pamaso panga m'Yerusalemu, mudzi umene ndinadzisankhira kuikapo dzina langa. 37Ndipo ndidzakutenga iwe, ndipo udzachita ufumu monga umo ukhumbira moyo wako, nudzakhala mfumu ya Israele. 38#2Sam. 7.11, 27Ndipo kudzakhala kuti ukadzamvera iwe zonse ndikulamulirazo, nukadzayenda m'njira zanga ndi kuchita chilungamo pamaso panga, kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga anatero Davide mtumiki wanga pamenepo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndidzakumangira ndi kukukhazikitsira nyumba, monga ndinammangira Davide, ndipo ndidzakupatsa iwe Israele. 39Ndipo chifukwa cha ichi ndidzazunza mbumba ya Davide, koma si masiku onse ai. 40Chifukwa chake Solomoni anafuna kupha Yerobowamu, ndipo Yerobowamu anathawira ku Ejipito kwa Sisake mfumu ya Aejipito, nakhala m'Ejipito kufikira imfa ya Solomoni.
Imfa ya Solomoni
41 #
2Mbi. 9.29-31
Ndipo machitidwe otsiriza a Solomoni, ndi ntchito zake zonse anazichita, ndi nzeru zake, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a Solomoni? 42Ndipo masiku amene Solomoni anakhala mfumu ya Aisraele onse m'Yerusalemu anali zaka makumi anai. 43Ndipo Solomoni anagona ndi makolo ake, naikidwa m'mudzi wa Davide atate wake; ndipo Rehobowamu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.
Currently Selected:
1 MAFUMU 11: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi