1 MAFUMU 10
10
Mfumu yaikazi ya ku Sheba adzacheza kwa Solomoni ku Yerusalemu
1 #
Ower. 14.12; 2Mbi. 9.1-12; Mat. 12.42 Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Sheba mbiri ya Solomoni yakubukitsa dzina la Yehova, anadza kumuyesera iye ndi miyambi yododometsa. 2Nafika ku Yerusalemu ndi ulendo wake waukulu, ndi ngamira zakunyamula zonunkhira, ndi golide wambiri, ndi timiyala ta mtengo wapatali; ndipo atafika kwa Solomoni anakamba naye zonse za m'mtima mwake. 3Ndipo Solomoni anamyankha miyambi yake yonse, panalibe kanthu kobisika ndi mfumu kamene sanamfotozere iye. 4Ndipo pamene mfumu yaikazi ya ku Sheba adaona nzeru zonse za Solomoni, ndi nyumba adaimangayo, 5ndi zakudya za pa gome lake, ndi makhalidwe a anyamata ake, ndi maimiriridwe a atumiki ake, ndi zovala zao, ndi otenga zikho ake, ndi nsembe yake yopsereza imene amapereka m'nyumba ya Yehova, anakhululuka malungo. 6Ndipo anati kwa mfumu, Idali yoonadi mbiri ija ndinaimva ine ku dziko langa ya machitidwe anu ndi nzeru zanu. 7Koma sindinakhulupirira mau amenewo mpaka ndafika ine kuno, ndaona ndi maso anga; ndipo taonani, anangondiuza dera lina lokha; nzeru zanu ndi zokoma zanu zakula pa mbiri ndinaimvayo. 8Odala anthu anu, odala anyamata anu akukhala nthawi zonse pamaso panu, akumvaimva nzeru yanu. 9#1Maf. 5.7Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu amene anakondwera nanu, kukuikani pa mpando wachifumu wa Israele; popeza Yehova anakonda Israele nthawi yosatha, chifukwa chake anakulongani inu ufumu, kuti muchite chiweruzo ndi chilungamo. 10#Mas. 72.10, 15Ndipo mkaziyo ananinkha mfumu matalente a golide zana limodzi mphambu makumi awiri, ndi zonunkhira zaunyinji ndi timiyala ta mtengo wapatali; sunafikanso unyinji wotero wa zonunkhira wolingana ndi uja mfumu yaikazi ya ku Sheba inapereka kwa mfumu Solomoni. 11#1Maf. 9.27Ndipo zombo za Hiramu zotengera golide ku Ofiri zinatenganso ku Ofiri mitengo yambiri yambawa, ndi timiyala ta mtengo wapatali. 12#2Mbi. 9.10-11Ndipo mfumu inasema mitengo yambawayo, ikhale mizati ya nyumba ya Yehova, ndi ya nyumba ya mfumu; ndiponso azeze ndi zisakasa za oimbawo; siinafika kapena kuonekanso mpaka lero mitengo yotero yambawa. 13Ndipo mfumu Solomoni ananinkha mfumu yaikazi ya ku Sheba chifuniro chake chonse anachipempha iye, osawerenga chimene Solomoni anamninkha mwa ufulu wake. Momwemo iye anabwerera namukanso ku dziko lake, iyeyo ndi anyamata ake.
Chuma ndi ukulu wa Solomoni
14Tsono kulemera kwake kwa golide anafika kwa Solomoni chaka chimodzi kunali matalente mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi a golide. 15Osawerenganso winayo wa anthu a malonda oyendayenda, ndi wa amalonda ena, ndi wa mafumu onse a Arabiya, ndi wa akazembe onse a madera. 16Ndipo mfumu Solomoni anapanga zikopa mazana awiri zagolide wonsansantha, chikopa chimodzi chinapangidwa ndi masekeli mazana asanu ndi limodzi. 17#1Maf. 14.26Ndi malihawo mazana atatu a golide wonsansantha, lihawo limodzi linapangidwa ndi miyeso ya mina itatu ya golide; ndipo mfumu inazisungira zonse m'nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni. 18#2Mbi. 9.17-19Ndipo mfumu inapanga mpando waukulu wachifumu waminyanga, naukuta ndi golide woyengetsa. 19Mpandowo wachifumu unali ndi makwerero asanu ndi limodzi, ndi pamwamba pa mpando wachifumu panali pozunguniza kumbuyoko, ndipo munali ngati manja m'mbali zonse ziwiri za pokhalirapo, naimika mikango iwiri m'mbali mwa manjawo. 20Ndipo anaimika mikango khumi ndi iwiri mbali ina ndi ina, pa makwerero asanu ndi limodzi aja; m'dziko lililonse lina simunapangidwa wotere. 21Ndipo zikho zomwera zonse za mfumu Solomoni zinali zagolide, ndi zotengera zonse za nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni zinali zagolide yekhayekha, panalibe zasiliva, pakuti siliva anangoyesedwa opanda pake masiku onse a Solomoni. 22Popeza mfumu inali nazo panyanja zombo za ku Tarisisi, pamodzi ndi zombo za Hiramu; zombo za ku Tarisisi zinafika kamodzi zitapita zaka zitatu, zili nazo golide, ndi siliva, ndi minyanga, ndi apusi, ndi mbalame za zitsukwa zazitali za mawangamawanga. 23#1Maf. 3.3, 12-13Ndipo mfumu Solomoni anawaposa mafumu onse a dziko lapansi pa chuma ndi nzeru. 24Ndipo anthu onse a pa dziko anafuna nkhope ya Solomoni, kudzamva nzeru zake zimene Mulungu analonga m'mtima mwake. 25Ndipo akafika munthu yense ndi mtulo wake, zotengera zasiliva, ndi zotengera zagolide, ndi zovala, ndi mure, ndi zonunkhira, ndi akavalo, ndi nyuru; momwemo chaka ndi chaka. 26#Deut. 17.16Ndipo Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi apakavalo; anali nao magaleta chikwi chimodzi mphambu mazana anai, ndi apakavalo zikwi khumi mphambu ziwiri, nawasungira m'midzi yosungamo magaleta, ndi kwa mfumu m'Yerusalemu. 27Ndipo mfumu inachulukitsa siliva ngati miyala m'Yerusalemu, ndi mitengo yamikungudza anailinganiza ndi mikuyu ya m'madambo. 28#1Maf. 10.26Ndipo akavalo a Solomoni anachokera ku Ejipito; anthu a malonda a mfumu anawagula magulumagulu, gulu lililonse mtengo wake. 29Ndipo galeta limodzi linachokera kutuluka m'Ejipito mtengo wake masekeli a siliva mazana asanu ndi limodzi, ndi kavalo mtengo wake masekeli zana limodzi mphambu makumi asanu; momwemonso iwo anawagulira mafumu onse a Ahiti ndi mafumu a Aramu.
Currently Selected:
1 MAFUMU 10: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi