1 MAFUMU 12
12
Rehobowamu samvera uphungu wa akulu
1 #
2Mbi. 10.1-19
Ndipo Rehobowamu ananka ku Sekemu, popeza Aisraele onse anadza ku Sekemu kumlonga ufumu. 2#1Maf. 11.40Ndipo kunali kuti Yerobowamu mwana wa Nebati anachimva akali m'Ejipito, kumene anathawira kuchokera ku maso a Solomoni mfumu, pakuti Yerobowamu anakhala ku Ejipito. 3Ndipo anatuma kukamuitana. Ndipo Yerobowamu ndi msonkhano wonse wa Israele anadza, nalankhulana ndi Rehobowamu, nati, 4#1Maf. 4.7Atate wanu analemeretsa goli lathu, ndipo inu tsono pepuzaniko ntchito zosautsa za atate wanu, ndi goli lolemera lake limene anatisenza, ndipo tidzakutumikirani. 5Ndipo iye anati kwa iwo, Bamukani, mukagone masiku atatu, pamenepo mukabwera kwa ine. Ndipo anthu anamuka. 6Ndipo mfumu Rehobowamu anafunsira kwa mandoda, amene anaimirira pamaso pa Solomoni atate wake, akali moyo iyeyo, nati, Inu mundipangire bwanji kuti ndiyankhe anthu awa? 7#Miy. 15.1Ndipo iwo anamuuza kuti, Mukakhala inu mtumiki wa anthu awa lero, ndi kuwatumikira ndi kuwayankha ndi kukamba nao mau okoma, tsono iwo adzakhala chikhalire atumiki anu. 8Koma iye analeka uphungu wa mandodawo, umene anampangirawo, nakafunsira kwa achinyamata anzake oimirira pamaso pake, 9nati kwa iwo, Kodi inu mundipangire bwanji kuti tiyankhe anthu awa anandiuza ine, kuti, Mupepuze goli limene atate wanu anatisenza ife? 10Ndipo achinyamata anzake ananena naye, nati, Mzitero ndi anthu awa adalankhula nanu, nati, atate wanu analemeretsa goli lathu, koma inu mutipepuzire limenelo; mzitero nao, Kanense wanga adzaposa m'chuuno mwa atate wanga. 11Ndipo tsopano, popeza atate wanga anakusenzani goli lolemera, ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu, atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira. 12Ndipo Yerobowamu ndi anthu onse anabwera kwa Rehobowamu tsiku lachitatu monga momwe anawauzira mfumu, nati, Bweraninso kwa ine tsiku lachitatu. 13Ndipo mfumu inayankha anthu mau okalipa, naleka uphungu anampangira mandodawo, 14nalankhula nao monga mwa uphungu wa achinyamata, nati, Atate wanga analemeretsa goli lanu, koma ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakupulani ndi zinkhanira. 15#1Maf. 11.31; 12.24Potero mfumu siinamvera anthuwo, pakuti kusintha uku kunachokera kwa Yehova, kuti akhazikitse mau ake amene Yehova ananenetsa Ahiya wa ku Silo kwa Yerobowamu mwana wa Nebati. 16#2Sam. 20.1Ndipo pakuona Aisraele onse kuti mfumu siinawamvera iwo, anthuwo anayankha mfumu, Tili naye chiyani Davide? Inde tilibe cholowa m'mwana wa Yese; tiyeni kwathu Aisraele inu; yang'aniranitu nyumba yako, Davide. Momwemo Aisraele anachoka kunka ku mahema ao. 17Koma ana aja a Israele akukhala m'midzi ya Yuda, Rehobowamu anakhalabe mfumu yao. 18Pamenepo mfumu Rehobowamu anatuma Adoramu wamsonkho, ndipo Aisraele onse anamponya miyala, nafa. Ndipo mfumu Rehobowamu anafulumira kulowa m'galeta wake kuthawira ku Yerusalemu. 19#2Maf. 17.21Motero Aisraele anapandukana ndi nyumba ya Davide kufikira lero. 20Ndipo kunali, atamva Aisraele onse kuti Yerobowamu wabweranso, anatuma kumuitanira iye kumsonkhano, namlonga iye mfumu ya Aisraele onse; palibe munthu anatsata nyumba ya Davide koma fuko lokha la Yuda.
21 #
2Mbi. 11.1-4
Ndipo Rehobowamu anafika ku Yerusalemu, nasonkhanitsa nyumba yonse ya Yuda, ndi fuko la Benjamini, ankhondo osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, kuyambana nayo nyumba ya Israele, kubwezanso ufumu kwa Rehobowamu mwana wa Solomoni. 22Ndipo mau a Mulungu anafika kwa Semaya mneneri wa Mulungu, nati, 23Lankhula kwa Rehobowamu mwana wa Solomoni mfumu ya Yuda, ndi kwa nyumba yonse ya Yuda, ndi Benjamini, ndi kwa anthu otsalawo, nuti, 24#1Maf. 12.15Yehova atero, Musamuka, ndipo musakayambana ndi abale anu ana a Israele, bwererani yense kunyumba kwake; popeza chinthuchi chachokera kwa Ine. Ndipo iwo anamvera mau a Yehova, natembenuka, nabwerera monga mwa mau a Yehova.
Kupembedza mafano kwa Yerobowamu
25Ndipo Yerobowamu anamanga Sekemu m'mapiri a Efuremu, nakhalamo, natulukamo, namanga Penuwele. 26Ndipo Yerobowamu ananena m'mtima mwake, Ufumuwu udzabwereranso kunyumba ya Davide. 27#Deut. 12.5-6Anthu awa akamakwera kukapereka nsembe m'nyumba ya Yehova m'Yerusalemu, pamenepo mitima ya anthu awa idzatembenukiranso kwa mbuye wao, kwa Rehobowamu mfumu ya Yuda; ndipo adzandipha, nadzabweranso kwa Rehobowamu mfumu ya Yuda. 28#Eks. 32.4, 8Potero mfumu inakhala upo, napanga anaang'ombe awiri agolide, nati kwa iwo, Kukulemetsani kukwera ku Yerusalemu; tapenyani Aisraele inu milungu yanu, imene inakutulutsani m'dziko la Ejipito. 29Ndipo anaimika mmodzi ku Betele, naimika wina ku Dani. 30#1Maf. 13.34Koma chinthu ichi chinasanduka tchimo, ndipo anthu ananka ku mmodziyo wa ku Dani. 31#Num. 3.10; 1Maf. 13.32Iye namanga nyumba za m'misanje, nalonga anthu achabe akhale ansembe, osati ana a Levi ai. 32#Lev. 23.34; Amo. 7.13Ndipo Yerobowamu anaika madyerero mwezi wachisanu ndi chitatu, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi olingana ndi madyerero aja a ku Yuda, napereka nsembe pa guwa la nsembe; anatero m'Betele, nawaphera nsembe anaang'ombe aja anawapanga, naika m'Betele ansembe a misanje imene anaimanga. 33Ndipo anapereka nsembe pa guwa la nsembe analimanga m'Betele, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chitatu, m'mwezi umene anaulingirira m'mtima mwa iye yekha, nawaikira ana a Israele madyerero, napereka nsembe pa guwa la nsembe, nafukiza zonunkhira.
Currently Selected:
1 MAFUMU 12: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi