1 MAFUMU 13
13
Mneneri adzudzula Yerobowamu
1 #
1Maf. 12.32-33
Ndipo onani, munthu wa Mulungu anachokera ku Yuda mwa mau a Yehova nadza ku Betele; ndipo Yerobowamu anali kuimirira m'mbali mwa guwa la nsembe kufukiza zonunkhira. 2#2Maf. 23.15-16Ndipo iye anafuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe, nati, Guwa la nsembe, guwa la nsembe, atero Yehova, Taona mwana adzabadwa m'nyumba ya Davide, dzina lake ndi Yosiya, adzaphera pa iwe ngati nsembe anthu ansembe a misanje, amene alikufukiza zonunkhira pa iwe, nadzatentha pa iwe mafupa a anthu. 3#Yes. 7.14Ndipo iye anapatsa chizindikiro tsiku lomwelo, nati, Chizindikiro chimene Yehova ananena ndi ichi, Taonani guwali la nsembe lidzang'ambika, ndi phulusa lili pa ilo lidzatayika. 4Ndipo kunachitika, pakumva mfumu mau a munthu wa Mulungu amene anawafuula, kutemberera guwa la nsembe m'Betele, Yerobowamu anatansa dzanja lake ali ku guwalo, nati, Mgwireni iye. Ndipo dzanja lake analitansira kwa iye linauma, kuti sanathe kulifunyatitsanso. 5Ndiponso guwalo linang'ambika, ndi phulusa la pa guwalo linatayika, monga mwa chizindikiro chimene munthu wa Mulungu anapatsa mwa mau a Yehova. 6#Eks. 8.8; Mac. 8.2Ndipo mfumu inayankha niti kwa munthu wa Mulungu, Undipembedzere Yehova Mulungu wako, nundipempherere, kuti dzanja langa libwerenso kwa ine. Ndipo munthuyo wa Mulungu anapembedza Yehova, ndipo dzanja la mfumu linabwezedwa kwa iye momwemo mwa kale. 7Mfumu niti kwa munthu wa Mulungu, Tiye kwathu, ukapumule, ndikupatse mphatso. 8#2Maf. 5.15-16Ndipo munthu wa Mulungu ananena ndi mfumu, Mungakhale mundigawira pakati ndi pakati nyumba yanu, sindilowa kwa inu, kapena kudya mkate, kapena kumwa madzi kuno. 9Pakuti potero ndinalamulidwa ndi mau a Yehova, ndi kuti, Usakadye mkate, kapena kumwa madzi, kapena kubwerera njira yomweyo unadzerayo. 10Tsono iye anayenda njira ina osabwerera njira yomweyo anaidzera pakudza ku Betele.
Mneneri wosamverayo aphedwa ndi mkango
11Ndipo ku Betele kunakhala mneneri wokalamba, ndipo mwana wake wina anadzamfotokozera machitidwe onse anawachita munthu wa Mulunguyo tsiku lomwelo m'Betele ndi mau ake anawanena ndi mfumu; inde omwe aja iwo anamfotokozera atate wao. 12Ndipo atate wao anati kwa iwo, Wapitira njira yiti? Popeza ana ake adaona njira analowera munthu wa Mulungu anachokera ku Yudayo. 13Nanena ndi ana ake, Ndimangireni mbereko pa bulu. Namangira iwo mbereko pa bulu, naberekekapo iye. 14Natsata munthu wa Mulungu, nampeza ali tsonga patsinde pa mtengo wathundu, nanena naye, Kodi ndiwe munthu wa Mulungu amene uja anachokera ku Yuda? Nati, Ndine amene. 15Tsono ananena naye, Tiye kwathu, ukadye mkate. 16#1Maf. 13.8Nati iye, Sindingabwerere nawe kukalowa kwanu, kapena kudya mkate, kapena kumwa nawe madzi pano; 17pakuti mau a Yehova anadza kwa ine, nati Usakadye mkate, kapena kubwerera njira yomweyo unadzerayo. 18Ndipo anati kwa iye, Inenso ndine mneneri wonga iwe, ndipo mthenga analankhula ndi ine mwa mau a Yehova, nati, Kambwezere kwanu, kuti akadye mkate, namwe madzi. Koma anamnamiza. 19Tsono anabwerera naye, nakadya kwao, namwa madzi. 20Ndipo kunachitika iwo ali chikhalire pagome, mau a Yehova anadza kwa mneneri amene anambwezayo, 21nafuula iye kwa munthu uja wa Mulungu anachokera ku Yudayo, nati, Atero Yehova Pokhala sunamvera mau a pakamwa pa Yehova, osasunga lamulo lija Yehova Mulungu wako anakulamulira, 22koma unabwerera nudya mkate, ndi kumwa madzi paja pomwe Iye anakuuza, Usakadye mkate, kapena kumwa madzi, mtembo wako tsono sudzaikidwa ku manda a atate ako. 23Ndipo kunachitika, atadya iye mkate, ndi kumwa madzi, anammangira mbereko pa bulu mneneri amene anambwezayo. 24#1Maf. 20.36Ndipo atachoka iye, mkango unakomana naye panjira, numupha ndipo mtembo wake unagwera m'njiramo, bulu naima pafupi, mkangonso unaima pafupi ndi mtembo. 25Ndipo onani, anthu anapitapo naona mtembo wogwera m'njiramo, ndi mkango uli chiimire pafupi ndi mtembo, nadzanena m'mudzi m'mene munakhala mneneri wokalamba uja. 26Ndipo mneneri amene uja anambweza panjirayo atamva, anati, Ndiye munthu uja wa Mulungu amene sanamvere mau a Yehova; chifukwa chake Yehova wampereka kwa mkango, numkadzula numupha, monga mwa mau a Yehova analankhula nayewo. 27Iye nanena ndi ana ake, nati, Ndimangireni mbereko pa bulu. Namangira mbereko. 28Namuka iye, napeza mtembo wake wogwera m'njira, ndi bulu ndi mkango zili chiimire pafupi ndi mtembo. Mkango udalibe kudya mtembo, kapena kukadzula bulu. 29Ndipo mneneri ananyamula mtembo wa munthu wa Mulunguyo, nausenza pa bulu, nabwera nao, nalowa m'mudzi mneneri wokalamba kumlira ndi kumuika. 30#Yer. 22.18Ndipo mtembo wake anauika m'manda a iye mwini, namlira iwo maliro, nati, Mayo, mbale wanga! 31#2Maf. 23.17-18Ndipo kunachitika, atamuika iye, ananena ndi ana ake, nati, Nkadzamwalira ine mudzandiike ine m'manda momwemo mwaikidwa munthu wa Mulunguyo, ikani mafupa anga pafupi ndi mafupa ake. 32Popeza mau aja anawafuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe la ku Betele, ndi kutemberera nyumba zonse za misanje ili m'midzi ya ku Samariya, adzachitika ndithu.
33 #
1Maf. 12.31-32
Pambuyo pa ichi Yerobowamu sanabwerere pa njira yake yoipa, koma analonganso anthu achabe akhale ansembe a misanje, yense wakufuna yemweyu anampatula akhale wansembe wa misanje. 34#1Maf. 14.10Ndimo umu munali tchimo la nyumba ya Yerobowamu, limene linaidula ndi kuiononga pa dziko lapansi.
Currently Selected:
1 MAFUMU 13: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi