YouVersion Logo
Search Icon

1 MAFUMU 14

14
Ahiya aneneratu kugwa kwa Yerobowamu
1Nthawi yomweyo Abiya mwana wa Yerobowamu anadwala. 2#1Maf. 11.30-31Ndipo Yerobowamu ananena ndi mkazi wake, Unyamuke, nudzizimbaitse, ungadziwike kuti ndiwe mkazi wa Yerobowamu, nupite ku Silo; taona, kumeneko kuli Ahiya mneneri uja anandiuza ine ndidzakhala mfumu ya anthu awa. 3#1Sam. 9.7-8Nupite nayo mikate khumi, ndi timitanda, ndi chigulu cha uchi, numuke kwa iye; adzakuuza m'mene umo akhalire mwanayo. 4Natero mkazi wa Yerobowamu, nanyamuka namka ku Silo, nalowa m'nyumba ya Ahiya. Koma Ahiya sanatha kupenya, popeza maso ake anali tong'o, chifukwa cha ukalamba wake. 5Ndipo Yehova ananena ndi Ahiya, Taona, mkazi wa Yerobowamu akudza kukufunsa za mwana wake, popeza adwala; udzanena naye mwakutimwakuti; popeza kudzakhala pakulowa iye adzadzizimbaitsa. 6Ndipo kunachitika, pamene Ahiya anamva mgugu wa mapazi ake alinkulowa pakhomo, anati, Lowa mkazi iwe wa Yerobowamu, wadzizimbaitsiranji? Pakuti ine ndatumidwa kwa iwe ndi mau olasa. 7#2Sam. 12.7-8Kauze Yerobowamu, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Ndingakhale ndinakukulitsa pakati pa anthu, ndi kukukhalitsa pakati pa anthu ndi kukukhalitsa mfumu ya anthu anga Aisraele, 8#1Maf. 11.31ndipo ndinalanda nyumba ya Davide ufumu, ndi kuupereka kwa iwe, koma sunafanana ndi Davide mtumiki wanga uja, amene anasunga malamulo anga, nanditsata ndi mtima wake wonse kuchita zolunjika zokhazokha pamaso panga; 9#1Maf. 12.28; Neh. 9.26koma wachimwa koposa onse akale, nukadzipangira milungu ina ndi mafano yoyenga kundikwiyitsa, nunditaya Ine kumbuyo kwako; 10#1Maf. 15.29chifukwa chake, taona ndidzafikitsa choipa pa nyumba ya Yerobowamu, ndi kugulula mwana wamwamuna yense wa Yerobowamu womangika ndi womasuka m'Israele, ndipo ndidzachotsa psiti nyumba yonse ya Yerobowamu, monga munthu achotsa ndowe kufikira idatha yonse. 11#1Maf. 16.4Agalu adzadya aliyense wa Yerobowamu wakufa m'mudzi; ndi mbalame za m'mlengalenga zidzadya yense wakufera kuthengo; popeza wanena ndi Yehova. 12#1Maf. 14.17Tanyamuka tsono, numuke kwanu; pakulowa mapazi ako m'mudzi mwanayo adzatsirizika. 13Ndipo Aisraele onse adzamlira, nadzamuika, popeza iye yekha wa ana a Yerobowamu adzalowa m'manda; pakuti mwa iye mwapezedwa chokoma cha kwa Yehova Mulungu wa Israele m'nyumba ya Yerobowamu. 14#1Maf. 15.27-29Ndiponso Yehova adzadziukitsira mfumu ya Israele, idzaononga nyumba ya Yerobowamu tsiku lomwelo; nchiyani ngakhale tsopano apa? 15#2Maf. 15.28-29Popeza Yehova adzawakantha Aisraele monga bango ligwedezeka ndi madzi, nadzazula Aisraele m'dziko lino labwino analipatsa makolo ao, nadzawamwazira ku tsidya lija la Yufurate, popeza iwo anapanga zifanizo zao zokwiyitsa Yehova. 16Ndipo adzapereka Aisraele chifukwa cha machimo a Yerobowamu anachimwawo, nachimwitsa nao Aisraele. 17#1Maf. 14.12Ndipo mkazi wa Yerobowamu ananyamuka nachoka, nafika ku Tiriza; ndipo polowa iye pa khomo la nyumba yake anatsirizika mwanayo. 18Ndipo anamuika, namlira Aisraele, monga mwa mau a Yehova anawalankhula pa dzanja la mtumiki wake Ahiya mneneri. 19#2Mbi. 13.2-20Ndipo machitidwe ena a Yerobowamu m'mene umo anachitira ufumu, taona, analembedwa m'buku la machitidwe a mafumu a Israele. 20Ndipo masiku akukhala Yerobowamu mfumu anali zaka makumi awiri mphambu ziwiri, nagona iye ndi makolo ake, nalowa ufumu m'malo mwake Nadabu mwana wake.
Yuda aipsidwa mwa Rehobowamu
21 # 2Mbi. 12.13 Ndipo Rehobowamu mwana wa Solomoni anali mfumu ya dziko la Yuda. Rehobowamu anali wa zaka makumi anai mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri m'Yerusalemu, m'mudzi m'mene Yehova adausankha m'mafuko onse a Israele kukhazikamo dzina lake. Ndipo dzina la amake linali Naama Mwamoni. 22#2Mbi. 12.1Ndipo Ayuda anachita zoipa pamaso pa Yehova, namchititsa nsanje ndi zoipa zao anazichitazo, zakuposa zija adazichita makolo ao. 23#Ezk. 16.24-25Pakuti anadzimangiranso misanje, ndi zoimiritsa, ndi zifanizo, pa chitunda chonse chachitali, ndi patsinde pa mtengo wogudira uliwonse; 24panalinso anyamata ochitirana dama m'dzikomo; iwo amachita monga mwa zonyansitsa za amitundu, amene Yehova anapirikitsa pamaso pa ana a Israele. 25#1Maf. 11.40Ndipo kunachitika, Rehobowamu atakhala mfumu zaka zisanu, Sisake mfumu ya Aejipito anakwera ndi nkhondo ku Yerusalemu, 26#2Mbi. 12.9-11nachotsa chuma cha m'nyumba ya Yehova, ndi chuma cha m'nyumba ya mfumu; inde anachotsa chonsecho, nachotsanso zikopa zagolide zonse adazipanga Solomoni. 27Ndipo mfumu Rehobowamu anapanga m'malo mwa izo zikopa zina zamkuwa, nazipereka m'manja a akapitao a olindirira, akusunga pakhomo pa nyumba ya mfumu. 28Ndipo kunachitika, pakulowa mfumu m'nyumba ya Yehova, olindirira aja anazinyamula, nabweranso nazo ku chipinda cha olindirirawo. 29Tsono, machitidwe ake ena a Rehobowamu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? 30Ndipo panali nkhondo pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu masiku ao onse. 31Nagona Rehobowamu ndi makolo ake, naikidwa kwa makolo ake m'mudzi wa Davide. Ndipo dzina la amake linali Naama Mwamoni, nalowa ufumu m'malo mwake Abiya mwana wake.

Currently Selected:

1 MAFUMU 14: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in