YouVersion Logo
Search Icon

ZEKARIYA 1

1
Mneneri adandaulira anthu Ayuda aleke zoipa zao
1 # Ezr. 4.24; Mat. 23.35 Mwezi wachisanu ndi chitatu, chaka chachiwiri cha Dariusi, mau a Yehova anadza kwa Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido mneneri, ndi kuti, 2Yehova anakwiya kwambiri ndi makolo anu. 3#Mala. 3.7; Luk. 15.20Chifukwa chake uziti nao, Atero Yehova wa makamu: Bwererani kudza kwa Ine, ati Yehova wa makamu, ndipo Ine ndidzabwerera kudza kwa inu, ati Yehova wa makamu. 4#2Mbi. 36.15-16; Yes. 31.6Musamakhala ngati makolo anu, amene aneneri akale anawafuulira, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu Bwereranitu kuleka njira zanu zoipa, ndi machitidwe anu oipa; koma sanamve, kapena kumvera Ine ati Yehova. 5Makolo anu, ali kuti iwowo? Ndi aneneri, akhala ndi moyo kosatha kodi? 6Koma mau anga ndi malemba anga, amene ndinalamulira atumiki anga aneneriwo, kodi sanawapeze makolo anu? Ndipo anabwera, nati, Monga umo Yehova wa makamu analingirira kutichitira ife, monga mwa njira zathu ndi monga mwa machitidwe athu, momwemo anatichitira.
Masomphenya oyamba: akavalo
7Tsiku la makumi awiri ndi chinai la mwezi wakhumi ndi chimodzi, ndiwo mwezi wa Sebati, chaka chachiwiri cha Dariusi, mau a Yehova anadza kwa Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido mneneri, ndi kuti, 8#Chiv. 6.4Ndinaona usiku, taonani, munthu woyenda pa kavalo wofiira, alikuima pakati pa mitengo yamchisu inali kunsi; ndi pambuyo pake panali akavalo ofiira, odera ndi oyera. 9Pamenepo ndinati, Awa ndi chinai, mbuyanga? Ndi mthenga wakulankhula ndi ine anati kwa ine, Ndidzakuonetsa awa ndi chiyani. 10#Aheb. 1.14Ndipo wakuima pakati pa mitengo yamchisu anayankha, nati, Awa ndiwo amene Yehova anawatumiza ayendeyende m'dziko. 11Ndipo iwo anamyankha mthenga wa Yehova wakuima pakati pa mitengo yamchisu, nati, Tayendayenda m'dziko, ndipo taonani, dziko lonse likhala chete, lipumula. 12#Mas. 102.13Ndipo mthenga wa Yehova anayankha nati, Yehova wa makamu, mudzakhala mpaka liti osachitira chifundo Yerusalemu, ndi mizinda ya Yuda, imene munakwiya nayo zaka izi makumi asanu ndi awiri? 13#Yer. 29.10-11Ndipo Yehova anamyankha mthenga wakulankhula ndi ine mau okoma, mau akutonthoza mtima. 14#Yow. 2.18Ndipo mthenga wakulankhula ndi ine anati kwa ine, fuula, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Ndichitira nsanje Yerusalemu ndi Ziyoni ndi nsanje yaikulu. 15#Yes. 47.6Ndipo ndikwiya nao amitundu okhala osatekeseka ndi mkwiyo waukulu; pakuti ndinakwiya pang'ono, ndipo anathandizira choipa. 16#Yes. 54.8Chifukwa chake atero Yehova: Ndabwera kudza ku Yerusalemu ndi zachifundo; nyumba yanga idzamangidwamo, atero Yehova wa makamu, ndipo adzayesa Yerusalemu ndi chingwe. 17#Yes. 51.3Fuulanso, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Mizinda yanga idzalemerera ndi kufalikiranso; ndipo Yehova adzasangalatsanso Ziyoni, nadzasankhamo Yerusalemu.
Masomphenya achiwiri: nyanga zinai ndi osula anai
18Ndipo ndinakweza maso anga, ndinapenya, taonani, nyanga zinai. 19#Ezr. 4.1; 4.7; 5.3Ndipo ndinati kwa mthenga wakulankhula ndi ine, Izi nziyani? Ndipo anandiyankha, Izi ndi nyangazi zinabalalitsa Yuda, Israele, ndi Yerusalemu. 20Ndipo Yehova anandionetsa osula anai. 21Pamenepo ndinati, Adzeranji awa? Ndipo ananena, nati, Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda, wopandanso wina woweramutsa mutu wake; koma awa anadza kuziopsa, kugwetsa nyanga za amitundu, amene anakwezera dziko la Yuda nyanga zao kulimwaza.

Currently Selected:

ZEKARIYA 1: BLP-2018

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in