YouVersion Logo
Search Icon

ZEKARIYA 2

2
Masomphenya achitatu: Yerusalemu ayesedwa ndi chingwe
1 # Ezk. 40.3 Ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, munthu ndi chingwe choyesera m'dzanja lake. 2#Chiv. 21.15-16Ndipo ndinati, Upita kuti? Ndipo anati kwa ine, Kukayesa Yerusalemu, kuona ngati chitando chake nchotani, ndi m'litali mwake motani. 3Ndipo taonani, mthenga wolankhula nane anatuluka, ndi mthenga wina anatuluka kukomana naye, 4#Ezk. 36.1, 11nanena naye, Thamanga, lankhula ndi mnyamata uyu, ndi kuti, Mu Yerusalemu mudzakhala anthu ngati m'midzi yopanda malinga, chifukwa cha kuchuluka anthu ndi zoweta momwemo. 5#Yes. 4.5Pakuti Ine, ati Yehova, ndidzakhala kwa iye linga lamoto pozungulira pake, ndipo ndidzakhala ulemerero m'kati mwake. 6#Yes. 48.20Haya, haya, thawani kudziko la kumpoto ati Yehova; pakuti ndinakubalalitsani ngati mphepo zinai za kuthambo, ati Yehova. 7#Chiv. 18.4Haya Ziyoni, thawa iwe wakukhala ndi mwana wamkazi wa Babiloni. 8#Deut. 32.10Pakuti atero Yehova wa makamu: Utatha ulemererowo ananditumiza kwa amitundu amene anakufunkhani; pakuti iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m'diso lake. 9Pakuti, taonani, ndidzawayambasira dzanja langa, ndipo adzakhala zofunkha za iwo amene anawatumikira; ndipo mudzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma. 10#Zef. 3.14-15Imba, nukondwere, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti taonani, ndilinkudza, ndipo ndidzakhala pakati pako, ati Yehova. 11#Yes. 60.3Ndipo amitundu ambiri adzaphatikidwa kwa Yehova tsiku ilo, nadzakhala anthu anga; ndipo ndidzakhala pakati pako, ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa iwe. 12#Deut. 32.9Ndipo Yehova adzalandira cholowa chake Yuda, ngati gawo lake m'dziko lopatulikalo, nadzasankhanso Yerusalemu. 13#Hab. 2.20Khalani chete, anthu onse, pamaso pa Yehova; pakuti wagalamuka mokhalira mwake mopatulika.

Currently Selected:

ZEKARIYA 2: BLP-2018

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in