ZEKARIYA 3
3
Masomphenya achinai: Satana atsutsana ndi Yoswa, Mulungu amuyesa wolungama
1 #
Ezr. 3.2; Hag. 1.1; Chiv. 12.10 Pamenepo anandionetsa Yoswa mkulu wa ansembe alikuima pamaso pa mthenga wa Yehova, ndi Satana alikuima padzanja lake lamanja, atsutsana naye. 2#Amo. 4.11; Aro. 11.5; Yud. 9Ndipo Yehova anati kwa Satana, Yehova akudzudzula, Satana iwe; inde Yehova amene anasankha Yerusalemu akudzudzula; uyu sindiye muuni wofumulidwa kumoto? 3#Yud. 23Koma Yoswa analikuvala nsalu zonyansa naima pamaso pa mthenga. 4#Yes. 61.10; Luk. 15.22Ndipo Iye anayankha nanena ndi iwo akuima pamaso pake, ndi kuti, Mumvule nsalu zonyansazi. Nati kwa iye, Taona, ndakuchotsera mphulupulu zako, ndipo ndidzakuveka zovala za mtengo wake. 5#Eks. 29.6Ndipo ndinati, Amuike nduwira yoyera pamutu pake. Naika nduwira yoyera pamutu pake, namveka ndi zovala; ndi mthenga wa Yehova anaimirirapo. 6Ndipo mthenga wa Yehova anamchitira Yoswa umboni, ndi kuti, 7#1Maf. 2.3Atero Yehova wa makamu: Ukadzayenda m'njira zanga, ndi kusunga udikiro wanga, pamenepo udzaweruza nyumba yanga, ndi kusunga mabwalo anga, ndipo ndidzakupatsa malo oyendamo mwa awa oimirirapo. 8#Yes. 42.1; Ezk. 3.3Tamvera tsono, Yoswa mkulu wa ansembe, iwe ndi anzako akukhala pansi pamaso pako; pakuti iwo ndiwo chizindikiro; pakuti taonani, ndidzafikitsa mtumiki wanga, ndiye Mphukira. 9#Chiv. 5.6Pakuti taona mwalawo ndinauika pamaso pa Yoswa; pamwala umodzi pali maso asanu ndi awiri; taonani, ndidzalocha malochedwe ake, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzachotsa mphulupulu ya dziko lija tsiku limodzi. 10#Mik. 4.4Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, mudzaitanizana yense mnansi wake patsinde pa mpesa ndi patsinde pa mkuyu.
Currently Selected:
ZEKARIYA 3: BLP-2018
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi