Logo ng YouVersion
Hanapin ang Icon

Ntc. 26

26
Paulo adziteteza pamaso pa mfumu Agripa
1Agripa adauza Paulo kuti, “Tikukulola kuti unene mau ako.” Tsono Paulo adatambalitsa dzanja lake nayamba kunena nkhani yake. Adati, 2“Inu Mfumu Agripa, ine ndikuganiza kuti ndine wamwai kuti ndi pamaso panu pamene ndiyankhe lero zonse zimene Ayuda akhala akundineneza. 3Makamaka chifukwa inu mumaidziŵa bwino miyambo yonse yachiyuda, ndiponso mikangano yao yonse, ndikukupemphani kuti mundimvere moleza mtima.
4“Ayuda onse akudziŵa za moyo wanga wonse kuyambira ndili mwana. Akudziŵa m'mene ndinkakhalira chiyambire pakati pa anthu a mtundu wanga, ndiponso ku Yerusalemu. 5#Ntc. 23.6; Afi. 3.5Iwo adandidziŵa kuyambira kale, ndipo ngati afuna, angathe kundichitira umboni kuti moyo wanga wonse ndakhala Mfarisi, mmodzi wa gulu lija limene limasamala chipembedzo chathu koposa. 6Ndipo tsopano ngati akundizenga mlandu, nchifukwa chakuti ndikuyembekeza zimene Mulungu adalonjeza makolo athu. 7Mafuko onse khumi ndi aŵiri a mtundu wathu, popembedza Mulungu usana ndi usiku mosafookera, amayembekeza kudzalandira zimene Iye adalonjezazo. Mwakuti nchifukwa cha chiyembekezo chimenechi, amfumu, kuti Ayuda akundineneza. 8#2Am. 7.9Bwanji ena mwa inu Ayuda mumayesa kuti nkosatheka kukhulupirira kuti Mulungu nkuukitsa anthu kwa akufa?
9 # Ntc. 8.3; 22.4, 5 “Ine ndemwe ndinkaganiza kuti ndinkayenera kuchita zinthu zambiri pofuna kuthetsa mbiri ya Yesu wa ku Nazarete. 10Ndipo ndidaazichitadi ku Yerusalemu. Akulu a ansembe atandipatsa ulamuliro, ine ndinkaŵatsekera m'ndende anthu ambiri a Mulungu. Pamene iwo ankaphedwa, ine ndinkavomereza. 11Kaŵirikaŵiri ndinkaŵalanga m'nyumba zonse zamapemphero, ndi kuyesa kuŵakakamiza kuti amnyoze Yesuyo. Ndinkaŵachitira ukali woopsa, kotero kuti ndinkaŵazunza ngakhale ku mizinda ya ku maiko achilendo.”
Paulo afotokozera Agripa za m'mene adaatembenukira mtima
12“Pa ulendo wina wotere, ndinkapita ku Damasiko ndi ulamuliro ndi mphamvu zondipatsa akulu a ansembe. 13Pa njira, nthaŵi yamasana dzuŵa lili pa mutu, inu amfumu, ndidaona kuŵala kochokera kumwamba. Kuŵalako kunali koposa kuŵala kwa dzuŵa, ndipo kudatizinga tonse, ine ndi anzanga aulendo. 14Tonse tidagwa pansi, ndipo ine ndidamva mau ondiwuza pa Chiyuda kuti, ‘Saulo, Saulo, ukundizunziranji? Ukungodzipweteka#26.14: Ukungodzipweteka…chobayira: Ng'ombe yokana kuguza ngolo, kutsogolo kwa ngoloyo amamangirirako mtengo umene uli ndi zobaya. Ng'ombe ija imadzipweteka pamene iponda zidyali. Iyi inali njira yophunzitsira ng'ombe kumvera. wekha ngati ng'ombe yoponda zidyali pa chobayira.’ 15Apo ndidafunsa kuti, ‘Ndinu yani, Ambuye?’ Ambuyewo adati, ‘Ine ndiye Yesu, amene ukumzunza. 16Koma dzuka, imirira. Pakuti ndakuwonekera kuti ndikuike kuti ukhale mtumiki wanga ndi mboni yanga. Ndifuna kuti ukhale mboni ya m'mene wandiwonera lero, ndiponso ya zimene ndidzakuwonetsa m'tsogolo. 17Ndidzakulanditsa kwa anthu a mtundu wako, ndiponso kwa anthu a mitundu ina kumene ndikukutuma. 18Ndikukutuma kuti anthu ameneŵa uŵatsekule maso, kuti atembenuke kuchoka mu mdima wa machimo nkuloŵa m'kuŵala, ndiponso kuchoka m'mphamvu ya Satana nkutsata Mulungu. Ndifuna kuti akhulupirire Ine, kuti machimo ao akhululukidwe, ndipo alandire nao madalitso pamodzi ndi anthu amene Mulungu adaŵasankha kuti akhale akeake.’
Paulo afotokoza za ntchito yake
19“Nchifukwa chake, mfumu Agripa, sindidakane kumvera zimene Mulungu adandiwonetsa m'masomphenyazo. 20#Ntc. 9.20, 28, 29Koma ndidalalika poyamba kwa anthu a ku Damasiko ndi a ku Yerusalemu, ndipo bwino lake ku dziko lonse la Yudeya, ndiponso kwa anthu a mitundu ina. Ndidalalika kuti atembenuke mtima, kutembenukira kwa Mulungu, ndi kuchita ntchito zotsimikiza kuti atembenukadi mtima. 21Chifukwa cha zimenezi Ayuda adandigwira m'Nyumba ya Mulungu nafuna kundipha. 22Koma Mulungu wakhala akundithandiza mpaka lero. Motero ndaimirira pano kuti ndichite umboni pamaso pa anthu onse, aakulu ndi ang'ono omwe. Zimene ndikuŵauza si zina ai, koma ndi zomwezo zimene aneneri ndi Mose adanena kuti zidzachitika. 23#1Ako. 15.20; Yes. 42.6; 49.6Paja iwo adati Mpulumutsi wolonjezedwa uja adzamva zoŵaŵa, ndipo popeza kuti Iye adzakhala woyamba kuuka kwa akufa, adzalengeza Ayuda ndi amene sali Ayuda za kuŵala kwa chipulumutso.”
Paulo ayankha Fesito ndi Agripa
24Pamene Paulo ankadziteteza ku zomnenezazo, Fesito adanena mokweza mau kuti, “Misalatu imeneyi, iwe Paulo! Kuphunziritsa kwako kukukupengetsa.” 25Koma Paulo adati, “Pepani, a Fesito olemekezeka, sindine wamisala ai. Zimene ndikunenazi nzoona ndi zanzeru. 26Mfumu Agripa akudziŵa zonsezi, nkuwona ndikulankhula pamaso pao momasuka. Ndikhulupirira kuti palibe kanthu nkamodzi komwe pa zimenezi kamene iwo sakadziŵa. Pakuti sizidachitike mobisika ai. 27Inu mfumu Agripa, kodi mumakhulupirira mau a aneneri? Ndikudziŵa kuti mumaŵakhulupirira.” 28Apo Agripa adauza Paulo kuti, “Uganiza kuti nkundisandutsa mkhristu pa kanthaŵi kochepa, komweka?” 29Paulo adati, “Kaya ndi pa kanthaŵi kochepa kaya nthaŵi yaitali, Mulungu akadalola kuti osati inu nokha, komanso anthu onse amene alikumva mau anga lero, akhale monga momwe ndiliri inemu, kupatula maunyolo okhaŵa.”
30Pamenepo mfumu Agripa, bwanamkubwa, Berenise, ndi onse amene anali nawo adaimirira. 31Atachokapo adauzana kuti, “Munthuyu sakuchita chilichonse choyenera kumuphera kapena kumponyera m'ndende.” 32Tsono Agripa adauza Fesito kuti, “Tikadammasula munthuyu akadapanda kupempha kuti mlandu wakewu ukazengedwe ndi Mfumu ya ku Roma.”

Kasalukuyang Napili:

Ntc. 26: BLY-DC

Haylayt

Ibahagi

Kopyahin

None

Gusto mo bang ma-save ang iyong mga hinaylayt sa lahat ng iyong device? Mag-sign up o mag-sign in