Ntc. 25
25
1Fesito adayamba ntchito yoweruza m'chigawo chake, ndipo patapita masiku atatu, adapita ku Yerusalemu kuchokera ku Kesareya. 2Kumeneko akulu a ansembe ndiponso atsogoleri a Ayuda adamufotokozera za mlandu wa Paulo. Iwo adapempha Fesito 3kuti aŵakomere mtima pakumtumiza Paulo ku Yerusalemu. Adaatero chifukwa anali atapangana zomulalira Paulo kuti amuphe pa njira. 4Fesito adaŵauza kuti, “Paulo akusungidwa m'ndende ku Kesareya, ndipo ine ndipita komweko posachedwa. 5Tsono atsogoleri anu apite nane pamodzi kumeneko, kuti akamneneze munthuyo ngatidi iye adachitapo cholakwa.”
6Fesito atakhala pakati pao ku Yerusalemu kuja masiku osapitirira asanu ndi atatu kapena khumi, adapita ku Kesareya. M'maŵa mwake adakhala pa mpando woweruzira milandu, naitanitsa Paulo kuti abwere pamaso pake. 7Paulo atafika, Ayuda amene adaabwera kuchokera ku Yerusalemu aja adamzinga, nayamba kumneneza zinthu zoopsa zambiri, zimene iwo sadathe kuzitsimikiza.
8Paulo poyankha zomnenezazo adati, “Ine sindidalakwirepo Malamulo a Ayuda, kapena Nyumba ya Mulungu, kapenanso Mfumu ya ku Roma.” 9Fesito pofuna kuchita mkomya kwa Ayuda, adafunsa Paulo kuti, “Kodi ungakonde kupita ku Yerusalemu kuti mlandu wakowu ukazengedwere kumeneko pamaso panga?” 10Koma Paulo adati, “Ine ndaima pa bwalo lamilandu la Mfumu ya ku Roma, ndiko kumene ayenera kundiweruza. Ayudaŵa ine sindidaŵalakwire chilichonse, monga inu mukudziŵa bwino. 11Ngati ndili wolakwa, ndipo ngati ndachita kanthu koyenera kuti ndiphedwe, sindikukana kuphedwa ai. Koma ngati zimene aŵa akundinenezazi si zoona, palibe munthu angathe kundipereka kwa iwo. Ine ndikupempha kuti mlandu wangawu ndikagwade kwa Mfumu ya ku Roma.” 12Tsono Fesito atakambirana ndi abwalo ake, adati, “Wachita apilo kwa Mfumu ya ku Roma. Chabwino, udzapitadi ku Romako kwa Mfumu yaikulu.”
Fesito afotokozera mfumu Agripa mlandu wa Paulo
13Patapita masiku, mfumu Agripa pamodzi ndi mkazi wake Berenise adadza ku Kesareya kudzalonjera Fesito. 14Atakhala kumeneko masiku angapo, Fesitoyo adafotokozera mfumoyo za mlandu wa Paulo. Adati, “Kuli munthu wina kuno amene Felikisi adamsiya m'ndende. 15Pamene ndinali ku Yerusalemu, akulu a ansembe pamodzi ndi atsogoleri a Ayuda adandifotokozera za iye, nandipempha kuti ndizenge mlandu wake ndi kugamula kuti ngwolakwa. 16Ine ndidaŵayankha kuti si mwambo wa Aroma kungompereka munthu ai. Munthu wonenezedwayo amayamba wakumana nawo omnenezawo, kuti iyeyo akhale ndi mwai woyankhapo pa zimene akumnenezazo. 17Tsono iwo atadzasonkhana kuno, ineyo mosataya nthaŵi, m'maŵa mwake ndidakakhala pa mpando woweruzira milandu, nkumuitanitsa munthuyo kuti abwere pamaso panga. 18Omneneza aja ataimirira, sadamneneze choipa nchimodzi chomwe pa zimene ndinkaganiza ine. 19Ankangokangana naye za chipembedzo chao, ndiponso ati za munthu wina dzina lake Yesu, amene adafa, koma Paulo amatsimikiza kuti ali moyo. 20Ine ndidaathedwa nzeru, osadziŵa kuti ndiifufuze bwanji nkhani imeneyi. Choncho ndidamufunsa Pauloyo ngati akadakonda kupita ku Yerusalemu kuti mlandu wakewo ukazengedwere kumeneko. 21Koma Paulo adapempha kuti abasungidwa m'ndende mpaka Mfumu ya ku Roma itatsimikiza za mlandu wake. Pamenepo ndidalamula kuti amsunge m'ndende kufikira nditamtumiza kwa Mfumuyo.” 22Apo Agripa adauza Fesito kuti, “Inenso nkadakonda kuti ndidzimvere ndekha zimene munthuyu anene.” Fesito adati, “Mumumva maŵa.”
23M'maŵa mwake Agripa ndi Berenise adabwera ndi ulemu waukulu wachifumu. Adaloŵa m'bwalo la milandu pamodzi ndi akulu a asilikali ndiponso akuluakulu a mumzindamo. Fesito adaitanitsa Paulo kuti abwere, iye nkubweradi. 24Tsono Fesito adati, “Mfumu Agripa, ndi inu nonse amene muli nafe muno, mukumuwona munthu uyu. Ayuda onse adandipempha ku Yerusalemu ndi kuno komwe mofuula kuti ameneyu sayenera kukhalanso moyo. 25Koma ine sindidapeze konse kuti iye adachita kanthu koyenera kumuphera. Ndiye popeza kuti mwiniwakeyu adapempha kuti mlandu wake ukazengedwe ndi Mfumu ya ku Roma, ndidatsimikiza zomtumiza. 26Komabe ndilibe kanthu kenikeni koti ndilembere mfumuyo za iyeyu. Motero ndabwera naye kwa inu, makamaka kwa inuinuyo mfumu Agripa, kuti mutamufunsitsa, ndikhale nkanthu koti ndilembe. 27Ine ndiye ndikuwona kuti ndi chinthu chopusa kutumiza mkaidi popanda kutchula zifukwa za mlandu wake.”
Kasalukuyang Napili:
Ntc. 25: BLY-DC
Haylayt
Ibahagi
Kopyahin

Gusto mo bang ma-save ang iyong mga hinaylayt sa lahat ng iyong device? Mag-sign up o mag-sign in
Bible Society of Malawi