Fesito atakhala pakati pao ku Yerusalemu kuja masiku osapitirira asanu ndi atatu kapena khumi, adapita ku Kesareya. M'maŵa mwake adakhala pa mpando woweruzira milandu, naitanitsa Paulo kuti abwere pamaso pake. Paulo atafika, Ayuda amene adaabwera kuchokera ku Yerusalemu aja adamzinga, nayamba kumneneza zinthu zoopsa zambiri, zimene iwo sadathe kuzitsimikiza.