Ndidzakulanditsa kwa anthu a mtundu wako, ndiponso kwa anthu a mitundu ina kumene ndikukutuma. Ndikukutuma kuti anthu ameneŵa uŵatsekule maso, kuti atembenuke kuchoka mu mdima wa machimo nkuloŵa m'kuŵala, ndiponso kuchoka m'mphamvu ya Satana nkutsata Mulungu. Ndifuna kuti akhulupirire Ine, kuti machimo ao akhululukidwe, ndipo alandire nao madalitso pamodzi ndi anthu amene Mulungu adaŵasankha kuti akhale akeake.’