Ntc. 19
19
Za ku Efeso
1Pamene Apolo anali ku Korinto, Paulo adayendera maiko apamtunda, nakafika ku Efeso. Kumeneko adapezako ophunzira ena, 2ndipo adaŵafunsa kuti, “Kodi mudalandira Mzimu Woyera pamene mudakhulupirira?” Iwo adati, “Nkumva komwe sitinamve kuti kuli Mzimu Woyera.” 3Paulo adaŵafunsa kuti, “Nanga tsono mudabatizidwa ndi ubatizo wotani?” Iwo adati, “Ndi ubatizo wa Yohane.” 4#Mt. 3.11; Mk. 1.4, 7, 8; Lk. 3.4, 16; Yoh. 1.26, 27 Paulo adati, “Yohane ankabatiza anthu otembenuka mtima, koma iye yemwe ankauza anthuwo kuti akhulupirire wina amene analikudza pambuyo pa iyeyo. Winayo ndiye Yesu.” 5Okhulupirira aja atamva zimenezi, adabatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu. 6Pamene Paulo adaŵasanjika manja, Mzimu Woyera adadza pa iwo, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zosadziŵika, ndi kumalalika mau ochokera kwa Mulungu. 7Anthuwo onse pamodzi analipo ngati khumi ndi aŵiri.
8Paulo adaloŵa m'nyumba yamapemphero ya Ayuda, ndipo pa miyezi itatu adakhala akulankhula molimba mtima. Ankakamba ndi anthu za ufumu wa Mulungu, nayesa kuŵakopa. 9Koma ena adaumitsa mitima yao, osafuna kukhulupirira, nkumanyoza Njira ya Ambuye pamaso pa gulu lonse. Pamenepo Paulo adaŵasiya nachoka nawo ophunzira aja, ndipo tsiku ndi tsiku ankakambirana m'sukulu ya Tirano.#19.9: Sukulu ya Tirano: Pa nthaŵi imeneyo anzeru ena anali ndi nyumba kapena chipinda chachikulu m'mene ankaphunzitsira ophunzira ao. Sitidziŵa zina za Tirano kapena za sukulu yake. 10Adachita zimenezi pa zaka ziŵiri, kotero kuti anthu onse okhala ku Asiya, Ayuda ndi Agriki omwe, adamva mau a Ambuye.
Za ana a Skeva
11Mulungu adachita zozizwitsa kwambiri kudzera kwa Paulo. 12Anthu ankati akatenga zitambaya kapena nsalu zina zimene Paulo ankagwiritsa ntchito, nakaziika pa anthu odwala, odwalawo ankachira, ndipo mizimu yoipa inkatuluka mwa iwo.
13Ayuda ena oyendayenda, otulutsa mizimu yoipa, nawonso adayesa kutchula dzina la Ambuye Yesu pa anthu ogwidwa ndi mizimu yoipa. Ankati, “M'dzina la Yesu amene Paulo amamlalika, ndikukulamulani kuti mutuluke.” 14Amene ankachita zimenezi ndi ana aamuna asanu ndi aŵiri a Skeva, mkulu wa ansembe onse wachiyuda. 15Koma mzimu woipawo udayankha kuti, “Yesu ndimamdziŵa, Paulonso ndimamdziŵa, koma inuyo ndinu yani?” 16Kenaka munthu wogwidwa ndi mizimu yoipa uja adaŵalumphira naŵagwira onse. Adaŵagonjetsa kotero kuti iwowo adathaŵanso m'nyumba muja ali maliseche ndiponso atapwetekedwa. 17Anthu onse okhala ku Efeso, Ayuda ndi Agriki atamva zimenezi, adachita mantha. Ndipo anthu ankatamanda dzina la Ambuye Yesu kopambana. 18Ambiri amene tsopano adaayamba kukhulupirira, adabwera nkumavomera poyera ndi kuulula zoipa zimene ankachita. 19Ambiri amene ankakonda kuchita matsenga, adasonkhanitsa mabuku ao naŵatentha pamaso pa anthu onse. Pamene adaonkhetsa mtengo wa mabukuwo, adapeza kuti udaakwanira ngati ndalama zikwi makumi asanu.
20Motero mau a Mulungu adanka nafalikirafalikira ndi kugwira ntchito mwamphamvu.
Anthu achita chipongwe ku Efeso
21Zitachitika zimenezi, Paulo adatsimikiza zopita ku Yerusalemu kudzera ku Masedoniya ndi ku Akaiya. Adati, “Kuchokera kumeneko ndiyeneranso kukayenda ku Roma.” 22Tsono adatuma Timoteo ndi Erasito ku Masedoniya. Ameneŵa anali aŵiri mwa anthu omuthandiza. Koma mwiniwakeyo adakhalirabe ku Asiya kanthaŵi.
23Nthaŵi yomweyo padabuka chipolowe chachikulu chifukwa cha Njira ya Ambuye. 24Mmisiri wina wa ntchito za siliva, dzina lake Demetrio, ankapanga timafanizo tasiliva ta nyumba yopembedzeramo Aritemi,#19.24: Timafanizo...Aritemi: Aritemiyo anali mulungu wina wamkazi wa Agriki. Aroma ankamutcha Diana. Ku Efeso kunali nyumba yaikulu ndi yokongola kwambiri yopembedzeramo mulungu ameneyo. Tsono amisiri ankapanga tinyumba tasiliva tofanizira nyumbayo, ndi kumatigulitsa kwa anthu. mulungu wao wamkazi, ndipo ntchito yakeyo inkaŵapindulitsa kwambiri antchito ake. 25Demetrioyo adasonkhanitsa anthu akewo, pamodzi ndi ena ogwira ntchito ya mtundu womwewo, naŵauza kuti, “Abale anga, mukudziŵa kuti chuma chathu chimachokera ku ntchito imeneyi. 26Mukuwona ndi kumva zimene akuchita mkulu uyu amati Pauloyu. Iye akunena kuti ati milungu yopangidwa ndi anthu si milungu konse. Ndipo wakopa anthu ambiri nkuŵapatutsa, osati ku Efeso kokha kuno ai, komanso pafupi dziko lonse la Asiya. 27Tsono choopsa nchakuti ntchito yathuyi ifika ponyozeka. Si pokhapo ai, komanso nyumba yopembedzeramo Aritemi, mulungu wathu wamkulu, anthu sadzaiyesa kanthu. Ndiye basitu udzawonongeka ulemerero wonse wa Aritemiyo, amene anthu onse a ku Asiya ndi a pa dziko lonse lapansi amampembedza.”
28Anthu aja atamva mau ameneŵa, adakwiya kwabasi, nayamba kufuula kuti, “Ndi wamkulu Aritemi wa Aefeso!” 29Choncho mumzinda monse mudadzaza chisokonezo. Tsono anthuwo adagwira Gayo ndi Aristariko, anthu a ku Masedoniya, anzake aulendo a Paulo, nathamangira nawo ku bwalo lamaseŵera. 30Paulo adaafuna kuloŵa pakati pa anthuwo, koma ophunzira sadamloleze. 31Akulu ena a Boma a ku Asiya komweko, amene anali abwenzi ake, adamtumiranso mau omupempha kuti asaloŵe dala m'bwalo lamaseŵeralo. 32Msonkhano wonse wa anthu aja udangoti pwirikiti: ena akufuula zina, enanso zina; ambiri osadziŵa ndi chimene asonkhanira chomwe. 33Ena m'khamumo adaaganiza kuti Aleksandro alipo ndi chonena, ataona kuti Ayuda amkankhira kutsogolo. Tsono iye adakweza dzanja kuti aŵakhalitse chete, kuti afotokozere anthu mlanduwo. 34Koma pamene anthu aja adazindikira kuti iyeyo ndi Myuda, onsewo adafuula pamodzi pa maola aŵiri kuti, “Ndi wamkulu Aritemi wa Aefeso!”
35Mlembi wa mzindawo ataŵatontholetsa anthu aja, adaŵauza kuti, “Inu Aefeso, ndani amene sadziŵa kuti mzinda wa Aefeso ndiwo wosunga nyumba yopembedzeramo Aritemi wamkulu, ndiponso wosunga mwala wopatulika uja umene udachita kugwa kuchokera kumwamba?#19.35: nyumba yopembedzeramo Aritemi: Anthu ku Efeso aja ankakhulupirira kuti fano la Aritemi, limene linali m'nyumba yao yompembedzeramo, lidagwa kuchokera Kumwamba. 36Tsono popeza kuti palibe amene angatsutse zimenezi, inu muyenera kukhala chete, osachita zinthu mopupuluma. 37Inu mwabwera ndi anthu aŵa kuno, ngakhale iwo sadabe za m'nyumba ya mulungu wathu wamkazi, kapena kumchita chipongwe. 38Ngati Demetrio ndi amisiri anzake ali ndi kanthu ndi munthu wina, mabwalo amilandu alipo, oweruza aliponso. Akakambirane milandu yao komweko. 39Koma ngati mukufunanso kanthu kena, kameneko msonkhano waulamuliro wa anthu onse ndiwo ukatsirize. 40Pakuti pali choopsa chakuti tingathe kuimbidwa mlandu wochita chipolowe chifukwa cha zimene zachitika lerozi. Palibe chifukwa chilichonse cha chipolowechi, ndipo tikasoŵa ponena akatifunsa.” 41Atanena zimenezi, adauza anthu aja kuti azipita.
Kasalukuyang Napili:
Ntc. 19: BLY-DC
Haylayt
Ibahagi
Kopyahin

Gusto mo bang ma-save ang iyong mga hinaylayt sa lahat ng iyong device? Mag-sign up o mag-sign in
Bible Society of Malawi