Ntc. 18
18
Za ku Korinto
1Pambuyo pake Paulo adachoka ku Atene napita ku Korinto. 2Kumeneko adapezako Myuda wina, dzino lake Akwila, mbadwa ya ku Ponto. Iye anali atangofika chatsopano kuchokera ku Italiya pamodzi ndi mkazi wake Prisila, chifukwa Klaudio, Mfumu ya ku Roma, adaalamula kuti Ayuda onse achoke ku Roma. Tsono Paulo adapita kukaŵaona. 3Ndiye popeza kuti iwo anali amisiri a ntchito imodzimodzi ngati yake, yosoka mahema, iyeyo adakhala nawo namagwirira limodzi ntchito. 4Pa tsiku la Sabata lililonse iye ankakambirana ndi anthu ku nyumba yamapemphero ya Ayuda, namayesetsa kukopa Ayuda ndi Agriki omwe.
5Silasi ndi Timoteo atafika kuchokera ku Masedoniya, Paulo tsopano ankangogwira ntchito yolalikira, ndi kuŵauza Ayuda monenetsa kuti Yesu ndiye anali Mpulumutsi wolonjezedwa uja. 6Koma pakuti iwo adaatsutsana naye ndi kumchita chipongwe, Paulo adalekana nawo pakukutumula zovala zake, naŵauza kuti, “Mwadziphetsa ndi mtima wanu. Tsono izo nzanu, ine ndilibe chifukwa. Kuyambira tsopano ndipita kwa akunja.” 7Motero adachoka kumeneko napita ku nyumba ya munthu wina, dzina lake Tito Yusto. Iyeyu anali munthu wopembedza Mulungu, ndipo nyumba yake idaayandikana ndi nyumba yamapemphero. 8Krispo, mkulu wa nyumba yamapempheroyo pamodzi ndi onse a pa banja lake adakhulupirira Ambuye. Ndipo anthu ambiri a ku Korinto atamva mau a Paulo, adakhulupirira nabatizidwa.
9Tsiku lina usiku Ambuye adaonekera Paulo m'masomphenya namuuza kuti, “Usaope, koma upitirire kulalika, osakhala chete ai, 10pakuti Ine ndili nawe pamodzi. Palibe munthu adzakukhudza kuti akuchite choipa, ndipo ndili nawo anthu ambiri mumzinda muno.” 11Choncho Paulo adakhala komweko chaka chimodzi ndi miyezi isanu ndi umodzi, akuŵaphunzitsa mau a Mulungu.
Ayuda amtengera Paulo ku bwalo la Galio
12Pamene Galio anali bwanamkubwa wa ku Akaiya, Ayuda onse pamodzi adaukira Paulo, namtengera ku bwalo la milandu. 13Iwo adati, “Munthu uyu akukopa anthu kuti azipembedza Mulungu mwa njira zotsutsana ndi Malamulo athu.” 14Koma pamene Paulo adati azilankhula, Galio adauza Ayuda kuti, “Ukadakhala mlandu wakuti munthu wachimwira lamulo, kapena wakuti walakwira mnzake, bwenzi nditakumverani bwinobwino, Ayuda inu. 15Koma popeza kuti ndi nkhani yokhudza mau, ndi maina, ndiponso Malamulo anu, mudziwonere nokha. Kuti ndiweruze zimenezi, ine toto.” 16Atatero adaŵapirikitsa kubwaloko. 17Pamenepo onsewo adagwira Sostene, mkulu wa nyumba yamapemphero ya Ayuda, nammenyera m'bwalo momwemo. Koma Galio sadasamaleko zimenezi.
Paulo abwerera ku Antiokeya
18 #
Num. 6.18
Paulo adakhalabe ku Korinto masiku ambiri. Pambuyo pake adalaŵirana ndi abale, naloŵa m'chombo kupita ku Siriya pamodzi ndi Prisila ndi Akwila. Asanaloŵe m'chombomo, Paulo adameta tsitsi lake ku Kenkrea, chifukwa anali atachita lumbiro kwa Mulungu. 19Iwo adakafika ku Efeso, ndipo kumeneko Paulo adasiyako Akwila ndi Prisila. Koma iye yekha adaloŵa m'nyumba yamapemphero nakambirana ndi Ayuda. 20Pamene ameneŵa adampempha kuti akhale nawo nthaŵi yaitali, iye sadavomere. 21Adaŵatsazika naŵauza kuti, “Mulungu akalola ndidzabweranso.” Atatero adachoka ku Efeso m'chombo.
22Pamene adafika ku Kesareya, adapita ku Yerusalemu kukacheza pang'ono ndi mpingo. Kuchokera kumeneko adapita ku Antiokeya. 23Atakhala kumeneko kanthaŵi ndithu, adachokako nakayendera dziko la Galatiya ndi la Frijiya, akulimbikitsa ophunzira onse.
Za Apolo
24Myuda wina, dzina lake Apolo, mbadwa ya ku Aleksandriya, adabwera ku Efeso. Anali munthu wodziŵa kulankhula ndi wodziŵa Malembo kwambiri. 25Iyeyu adaaphunzitsidwa Njira ya Ambuye, ndipo ndi changu chachikulu ankalankhula ndi kuphunzitsa za Yesu molongosoka, chonsecho ankangodziŵa za ubatizo wa Yohane wokha. 26Tsono adayamba kulankhula molimba mtima m'nyumba yamapemphero ya Ayuda. Koma pamene Prisila ndi Akwila anamumva, adamtenga namufotokezera Njira ya Mulungu molongosoka koposa.
27Pamene Apolo adafuna kuwolokera ku Akaiya, abale adamlimbikitsa, nalembera ophunzira akumeneko kalata kuti amlandire bwino. Tsono atafikako, adaŵathandiza kwambiri amene anali atakhulupirira chifukwa cha kukoma mtima kwa Mulungu. 28Pakuti iye adaatsutsa Ayuda mwamphamvu pamaso pa anthu, natsimikiza ndi Malembo kuti Yesu ndiyedi Mpulumutsi wolonjezedwa uja.
Kasalukuyang Napili:
Ntc. 18: BLY-DC
Haylayt
Ibahagi
Kopyahin

Gusto mo bang ma-save ang iyong mga hinaylayt sa lahat ng iyong device? Mag-sign up o mag-sign in
Bible Society of Malawi