Gen. 32

32
Yakobe akonzekera kukakumana ndi Esau
1Yakobe adanyamuka ulendo wake, ndipo angelo a Mulungu adakumana naye. 2Ataŵaona, adati, “Ili ndi gulu la ankhondo a Mulungu.” Motero malowo adaŵatcha Mahanaimu.#32.2: Mahanaimu: Mauŵa akutanthauza kuti magulu aŵiri a ankhondo. Onani pa 32.7,10. 3Tsono Yakobe adatuma amithenga ake kwa Esau mbale wake ku Seiri, ku dziko la Edomu. 4Adaŵalangiza kuti akauze Esau kuti, “Ine Yakobe mtumiki wanu ndinkakhala kwa Labani, ndipo ndakhalitsako mpaka tsopano lino. 5Ndili ndi ng'ombe, abulu, nkhosa ndi mbuzi ndiponso akapolo ndi adzakazi. Ndikutumiza mau ameneŵa kwa inu mbuyanga, kuti mundikomere mtima!” 6Amithengawo atabwerera kwa Yakobe adati, “Tidapita kwa mbale wanu Esau, ndipo akubwera kudzakumana nanu. Ali ndi anthu 400 pamodzi.” 7Apo Yakobe adachita mantha kwambiri ndi kutaya mtima. Motero anthu amene anali nawo adaŵagaŵa m'magulu aŵiri, pamodzi ndi nkhosa, mbuzi, ng'ombe ndiponso ngamira. 8Mumtima mwake ankaganiza kuti, “Esau akabwera, ndipo akachita nkhondo ndi gulu loyambali, gulu linalo lingathe kuthaŵa.”
9Pamenepo Yakobe adayamba kupemphera. Adati, “Mulungu wa kholo langa Abrahamu, Mulungu wa bambo wanga Isaki, mundimve ine! Inu Chauta mudandiwuza kuti, ‘Bwerera ku dziko lako, dziko la abale ako, ndidzasamala kuti zinthu zikuyendere bwino.’ 10Ine sindiyenera kulandira chifundo ndi chikhulupiriro chonse chimene mwandiwonetsa ine mtumiki wanu. Ndidaoloka Yordani ndilibe nkanthu komwe, koma ndodo yokha, koma tsopano ndabwerera ndi magulu aŵiri aŵa. 11Ndapota nanu, pulumutseni ku mphamvu za mbale wanga Esau. Ndikuwopa kuti mwina akubwera kudzatithira nkhondo, ndipo tonsefe adzatiwononga pamodzi ndi akazi ndi ana omweŵa. 12#Gen. 22.17Kumbukirani lonjezo lanu lija lakuti, ‘Ndithu ndidzasamala kuti zinthu zikuyendere bwino, ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zambiri zosaŵerengeka. Zidzakhala zochuluka ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja.’ ”
13Atagona kumeneko, pambuyo pake adasankhula mphatso izi pa chuma chonse chimene anali nacho: 14mbuzi zazikazi 200 ndi atonde makumi aŵiri, nkhosa zazikazi 200 ndi zamphongo makumi aŵiri, 15ngamira zamkaka makumi atatu pamodzi ndi ana ake, ng'ombe zazikazi makumi anai, ndi zazimuna khumi, ndi abulu aakazi makumi aŵiri ndi amphongo khumi. 16Gulu lililonse la zoŵeta adalipatsa mnyamata wosamala, ndipo adaŵauza onsewo kuti, “Inu mutsogoleko, ndipo poyenda ndi magulu a zoŵeta, muzisiya mpata pakati pa gulu lililonse.” 17Adauza mnyamata woyamba kuti, “Mbale wanga Esau akakumana nawe ndi kukufunsa kuti, ‘Kodi mbuyako ndani? Nanga ukupita kuti? Nanga zoŵeta zili patsogolo pakozi nza yani?’ 18Iwe ukayankhe kuti, ‘Zimenezi ndi za mtumiki wanu Yakobe, ndipo akuzitumiza kwa inu mbuyake, kuti zikhale mphatso. Yakobe mwiniwake ali m'mbuyo mwathumu.’ ” 19Tsono adauzanso mnyamata wake wachiŵiri mau omwewo, ndi wachitatu, mpaka onse amene ankayenda motsogoza zoŵeta. Adaŵauza kuti, “Zimenezi ndizo mukauze Esau, mukakumana naye. 20Muzikati, ‘Ndiponso mtumiki wanu Yakobe ali m'mbuyo mwathumu.’ ” Yakobe ankaganiza kuti, “Ndimtsitsa mtima ndi mphatso zimene ndamtumizirazi, ndipo ndikakumana naye, mwina adzandilandira bwino.” 21Choncho mphatsozo zidatsogola, ndipo usiku umenewo Yakobe adagona kumahema konkuja.
Yakobe alimbana ndi munthu ku Penuwele
22Usiku womwewo Yakobe adadzuka natenga akazi ake aŵiri, ndi adzakazi ake aŵiri aja, pamodzi ndi ana ake khumi ndi mmodzi, naoloka mtsinje wa Yaboki padooko pake. 23#Lun. 10.12Ataŵaolotsa onse aja, adaolotsanso chuma chake chonse. 24#Hos. 12.3, 4 Iye adangotsala yekha. Tsono kudadza munthu wina amene adalimbana naye mpaka m'matandakucha. 25Munthuyo ataona kuti sakuphulapo kanthu, adamenya Yakobe m'nyung'unyu, nyung'unyuyo nkuguluka polimbanapo. 26Apo munthuyo adati, “Taye ndizipita, chifukwa kulikucha.” Koma Yakobe adayankha kuti, “Sindikulola kuti upite mpaka utandidalitsa.” 27Munthuyo adamufunsa kuti, “Dzina lako ndiwe yani?” Yakobe adayankha kuti, “Dzina langa ndine Yakobe.” 28#Gen. 35.10 Munthu uja adati, “Dzina lako silidzakhalanso Yakobe. Walimbana ndi Mulungu ndi anthu, ndipo wapambana. Motero dzina lako lidzakhala Israele.” 29#Owe. 13.17, 18 Pomwepo Yakobe adati, “Choncho nanunso tandiwuzani dzina lanu.” Koma munthuyo adati, “Chifukwa chiyani ukundifunsa dzina?” Ndipo pompo munthu uja adadalitsa Yakobe. 30Yakobe adati, “Ndamuwona Mulungu maso ndi maso, ndipo ndili moyobe.” Tsono malowo adaŵatcha Penuwele.#32.30: Penuwele: Dzina limeneli limamveka ngati mau achihebri otanthauza kuti “nkhope ya Mulungu”. 31Dzuŵa lidamtulukira Yakobe pamene ankachoka ku Penuwele, ndipo ankayenda chotsimphina chifukwa cha nyung'unyu ija. 32Nchifukwa chake mpaka lero lino zidzukulu zonse za Israele sizidya nyama yapanyung'unyu, chifukwa ndi pa mtsempha wa panyung'unyu pomwe Yakobe adaamenyedwa.

ที่ได้เลือกล่าสุด:

Gen. 32: BLY-DC

เน้นข้อความ

แบ่งปัน

คัดลอก

None

ต้องการเน้นข้อความที่บันทึกไว้ตลอดทั้งอุปกรณ์ของคุณหรือไม่? ลงทะเบียน หรือลงชื่อเข้าใช้

วิดีโอสำหรับ Gen. 32