Gen. 33
33
Yakobe akumana ndi Esau
1Yakobe adaona Esau akubwera ndi anthu ake 400. Motero ana ake aja adaŵagaŵira Leya, Rakele ndi adzakazi aŵiri aja. 2Adatsogoza adzakaziwo pamodzi ndi ana ao. Leya ndi ana ake ankatsata pambuyo pao, Rakele ndi Yosefe ankadza pambuyo penipeni. 3Yakobe adatsogola, ndipo adaŵerama mpaka pansi kasanu ndi kaŵiri akuyandikira mbale wake.
4Koma Esau adathamanga kukakumana naye, namkumbatira, ndi kumlonjera pakumumpsompsona. Onse aŵiriwo ankangolira. 5Esau atayang'ana, adaona akazi ndi ana omwe aja, ndipo adamufunsa kuti, “Anthu aŵa ali ndi iweŵa nga yani?” Yakobe adayankha kuti, “Aŵa, mbuyanga, ndi ana amene Mulungu adandipatsa mwa chifundo chake.” 6Tsono adzakazi aja adadza pamodzi ndi ana ao, nagwada pansi. 7Adabweranso Leya pamodzi ndi ana ake, ndipo wotsirizira anali Rakele. Onsewo adagwada pansi. 8Esau adati, “Nanga gulu la zoŵeta ndakumana nalo lija ndi lachiyani?” Yakobe adayankha kuti, “Mbuyanga, gulu limene lija ndi lanu, kuti inuyo mundikomere mtima.” 9Koma Esau adati, “Mbale wanga, zoŵeta zotere ndili nazo zambiri. Uli nazozi zikhale zako.” 10Yakobe adati, “Ai chonde, ngati mwandikomera mtima, landirani mphatso yanga. Ine ndikamaona nkhope yanu, ndiye ngati ndaona nkhope ya Mulungu, poti mwandilandira chonchi ndi manja aŵiri. 11Chonde landirani mphatso ndakutengeraniyi. Mulungu adandikomera mtima, ndipo adandipatsa zosoŵa zanga zonse.” Adapitirira kumuumiriza, mpaka Esau adalandira.
12Ndipo Esau adati, “Tiyeni tinyamuke, tizipita. Ine nditsogolako.” 13Tsono Yakobe adati, “Mbuyanga, mukudziŵa kuti anaŵa atopa, ndipo ndiyenera kusamalanso nkhosa ndi ng'ombe zimene zili ndi tiana. Ndikazikusa mofulumira kwambiri, ngakhale tsiku limodzi lokha, zifa. 14Chonde mbuyanga, tsogolaniko, ine ndiziyenda pang'onopang'ono pambuyo pa zoŵeta ndi ana anga, mpaka ndikakupezani ku Seiri.”
15Apo Esau adati, “Tsono undilole kuti ndikusiyire anthu anga enaŵa.” Koma Yakobe adati, “Iyai mbuyanga, zimenezo sizifunika kwenikweni, ndingofuna kukukondwetsani.” 16Motero pa tsiku limenelo Esau adanyamuka ulendo kubwerera ku Seiri. 17Koma Yakobe adapita ku Sukoti, ndipo adamangako nyumba yake, pamodzi ndi makola a zoŵeta zake. Nchifukwa chake malowo adatchedwa Sukoti. 18Pambuyo pake Yakobe adakafika bwino ku mzinda wa Sekemu m'dziko la Kanani, atabwerera kuchokera ku Mesopotamiya. Adamanga mahema pamalo pena, poyang'anana ndi mzindawo. 19#Yos. 24.32; Yoh. 4.5Malo amenewo adagula kwa zidzukulu za Hamori, bambo wake wa Sekemu, pa mtengo wa ndalama 100 zasiliva. 20Adamanga guwa pomwepo, nalitcha El-Elohe-Israele, ndiye kuti Mulungu, Mulungu wa Israele.
ที่ได้เลือกล่าสุด:
Gen. 33: BLY-DC
เน้นข้อความ
แบ่งปัน
คัดลอก

ต้องการเน้นข้อความที่บันทึกไว้ตลอดทั้งอุปกรณ์ของคุณหรือไม่? ลงทะเบียน หรือลงชื่อเข้าใช้
Bible Society of Malawi