Gen. 31
31
Yakobe athaŵa kwa Labani
1Yakobe adamva kuti ana a Labani ankanena kuti, “Yakobe watenga zonse za bambo wathu. Wapeza chuma chake m'chuma cha bambo wathu.” 2Yakobe adazindikiranso kuti Labani sankamuwonetsa nkhope yabwino ngati kale. 3Tsono Chauta adamuuza kuti, “Bwerera ku dziko la atate ako ndi kwa abale ako. Ine ndidzakhala nawe.” 4Tsono Yakobe adatumiza mau kwa Rakele ndi kwa Leya kuti akakumane naye kubusa kumene kunali zoŵeta zake. 5Atafikako, iye adaŵauza kuti, “Ndaona kuti bambo wanu tsopano sakundipenya ndi maso abwino ngati kale. Koma Mulungu wa atate anga wakhala nane. 6Nonse aŵirinu mukudziŵa bwino kuti ndidagwira ntchito kwa bambo wanu ndi mphamvu zanga zonse. 7Komabe iye wandipusitsa, ndipo malipiro anga waasinthasintha kakhumi konse. Koma Mulungu sadamlole kuti andichite choipa. 8Nthaŵi zonse Labani akanena kuti, ‘Zoŵeta zamathothomathotho zidzakhala malipiro ako,’ zoŵeta zonse zinkakhala zamathothomathotho. Ndipo akanena kuti, ‘Zamipyololo zikhala malipiro ako,’ zoŵeta zonse zinkangokhala zamipyololo. 9Mulungu watenga zoŵeta zonse kwa bambo wanu, wapatsa ine. 10Pa nthaŵi yakuti zoŵeta zitenga maŵere, ine ndidalota maloto, ndipo ndidaona kuti atonde amene ankakwerawo anali amipyololomipyololo, amathothomathotho ndi amaŵangamaŵanga. 11Ndipo mngelo wa Mulungu adalankhula nane m'maloto momwemo nandiitana kuti, ‘Yakobe,’ ine ndidayankha kuti, ‘Ee Ambuye!’ 12Iye adati, ‘Tayang'ana, ndipo upenye kuti atonde onse amene akukweraŵa ndi amipyololomipyololo, amathothomathotho ndi amaŵangamaŵanga. Zimenezi ndachita ndine, popeza kuti ndaona zimene Labani akukuchita. 13#Gen. 28.18-22 Ine ndine Mulungu amene ndidakuwonekera ku Betele kuja kumene udaimika mwala wachikumbutso ndi kuudzoza mafuta, ndipo kumeneko iwe udalumbira. Konzeka tsopano, uchoke kuno, ubwerere ku dziko lakwanu.’ ” 14Rakele ndi Leya adayankha kuti, “Palibe chomwe chatitsalira ife kwa bambo wathu choti chikhale choloŵa chathu. 15Ife bambo wathu akutiyesa alendo. Adatigulitsa, ndipo ndalama zomwe adazipezera pa ifezo, adamwaza zonse. 16Chuma chonse chimene Mulungu wachotsa kwa bambo wathu, ndi chathu ndi cha ana athu. Chitani zimene Mulungu wakuuzani.”
17Motero Yakobe adakonzekera kuti achoke, kubwerera kwa bambo wake ku dziko la Kanani. Tsono ana ake onse pamodzi ndi akazi ake omwe adaŵakweza pa ngamira. 18Ndipo zoŵeta zonse adazitsogoza namazikusa, pamodzi ndi zonse zimene adazipeza ku Mesopotamiya kuja. 19Labani anali atapita kokameta nkhosa. Ndipo akadali komweko, Rakele adaba timilungu ta m'nyumba mwa Labani, bambo wake. 20Motero Yakobe adampusitsa Labani Mwaramu uja posamuuza kuti akuchoka. 21Adatenga zake zonse, nachoka chothaŵa. Adanyamuka, naoloka mtsinje wa Yufurate, nkuyamba ulendo wopita ku dziko lamapiri la Giliyadi.
Labani athamangira Yakobe
22Patapita masiku atatu, Labani adamva kuti Yakobe adathaŵa. 23Tsono adatenga anthu ake, nkulondola Yakobeyo masiku asanu ndi aŵiri, mpaka adakampezera ku dziko lamapiri la Giliyadi. 24Labani Mwaramu uja adalota maloto usiku womwewo. Mulungu adadza namuuza kuti, “Usamuwopseze Yakobe mwa njira iliyonse.”
25Labani adampeza Yakobe atamanga mahema kumapiriko. Nayenso Labaniyo adamanga mahema ake komweko ku dziko lamapiri la Giliyadi. 26Labani adafunsa Yakobe kuti, “Chifukwa chiyani wandinyenga ndi kutenga ana anga aakazi ngati ogwidwa pa nkhondo? 27Chifukwa chiyani wandinyenga ndi kundizemba osandiwuza? Ukadandiwuza, bwenzi nditakulola mokondwa, ndipo bwenzi pali kumaimba nyimbo ndi ting'oma ndi azeze. 28Sudandilole kuti nditsazikane ndi adzukulu anga ndi ana anga. Udachita zopusa. 29Ndili nazo mphamvu zakukuchita choipa. Koma usiku wapitawu, Mulungu wa atate ako wandiwuza kuti, ‘Usamuwopseze Yakobe mwa njira iliyonse.’ 30Ndikudziŵa kuti udachoka chifukwa unkafunitsitsa kubwerera kwanu. Koma bwanji wandibera timilungu tanga?” 31Yakobe adayankha kuti, “Ndinkaopa, chifukwa ndinkaganiza kuti mundilanda ana anuŵa. 32Koma mukapeza kuti wina aliyense pano ali ndi timilungu tanu, aphedwe ameneyo. Anthu tili nawoŵa akhale mboni pano pamene inu muyang'ane zinthu zanu m'katundu yenseyu. Tsono mukazipeza zanuzo mutenge.” Monsemo nkuti Yakobe ali wosadziŵa kuti Rakele adaaba timilunguto.
33Labani adakaloŵa m'hema la Yakobe ndi m'hema la Leya ndiponso m'hema la adzakazi aŵiri aja, koma sadatipeze timilungu taketo. Kenaka adakaloŵa m'hema la Rakele. 34Rakeleyo anali ataibisa milungu ya m'nyumba mwa Labaniyo, ataiika pa chishalo cha pamsana pa ngamira, iyeyo nkukhala pomwepo. Labani adafunafuna m'hema monsemo, koma osaipeza. 35Rakele adauza bambo wake kuti, “Ngati ndikulephera kuimirira pamaso panu, musandikwiyire bambo, chifukwa sindili bwino malinga nza ife akazife.” Motero Labani adalephera kutipeza timilungu ta m'nyumba mwake tija.
36Apo Yakobe adapsa mtima kwambiri ndipo adalankhula ndi Labani mokalipa, adati, “Kodi ndakulakwirani chiyani? Kodi ndaphwanya lamulo lotani, kuti mundilondole? 37Tsono mwafunafuna m'katundu wanga yense, kodi mwapeza chiyani chanu? Chomwe mwapezacho muchiike poyera pano, kuti anthu anu ndi anthu angaŵa achiwone. Ndipo iwowo ndiwo aone wokhoza pakati pa aŵirife. 38Ndakhala nanu zaka makumi aŵiri tsopano, ndipo nkhosa zanu pamodzi ndi mbuzi zomwe sizidapolozepo ai. Ine sindidadyeko nkhosa za m'khola mwanu. 39Nkhosa ikajiwa ndi zilombo, ine ndinkalipira nthaŵi zonse, sindinkabwera nayo kwa inu, kuwonetsa kuti sindidalakwe. Munkafuna kuti ndilipire chilichonse chobedwa usiku kapena usana. 40Nthaŵi zambiri ndinkavutika ndi kutentha masana ndiponso ndi kuzizira usiku. Sindinkatha kuwona tulo. 41Umu ndi m'mene zidaaliri zinthu pa zaka makumi aŵiri zomwe ndidakhala ndi inu. Ndidakugwirirani ntchito zaka khumi ndi zinai chifukwa cha ana anu aŵiriŵa, ndipo zaka zisanu ndi chimodzi ndidagwirira zoŵeta. Komabe malipiro anga mwakhala mukusintha kakhumi konse. 42Mulungu wa atate anga, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu amene Isaki ankamuwopa, akadapanda kukhala nane, bwenzi mutandichotsa kale ndili chimanjamanja. Koma Mulungu adaona mavuto anga ndi ntchito za manja anga, ndipo usiku wapitawu Iye wakutsutsani.”
Yakobe ndi Labani achita chipangano
43Labani adayankha Yakobe kuti, “Ana aakaziŵa ndi anga, ana ao ndi anga, pamodzi ndi zoŵeta zomwezi. Zonse ukuziwonazi nzanga. Koma tsopano ndiŵachitire chiyani ana anga aakaziŵa pamodzi ndi ana aoŵa? 44Chabwino, tiye tichite chipangano, chikhale mboni pakati pa ine ndi iwe.” 45Yakobe adaimiritsa mwala. 46Adauza anthu ake kuti asonkhanitse miyala, aunjike mulu. Ndipo pambali pake pa muluwo adadyerapo chakudya. 47Tsono muluwo Labani adautcha Yagara-Sahaduta, koma mulu womwewo Yakobe adautcha Galedi. 48Pambuyo pake Labani adati, “Mulu wamiyalawu udzakhala chikumbutso kwa ine ndi iwe.” Nchifukwa chake malowo adaŵatcha Galedi. 49Labani adanenanso kuti, “Chauta atiyang'anire ife tonse aŵiri pamene tikulekana. Motero malowo adaŵatcha Mizipa. 50Labani adapitirira kunena kuti, Ukamakaŵazunza ana angaŵa, kapena ukakakwatira akazi ena, ngakhale palibe wina ali nafe pano, ukumbukire kuti Mulungu ndiye mboni pakati pa ine ndi iwe.” 51Tsono Labani adauza Yakobe kuti, “Pano pali miyala imene ndaunjika pakati pathu, ndipo pompano pali mwala wachikumbutso. 52Mulu umenewu pamodzi ndi mwala wachikumbutsowu, zonsezi ndi mboni. Ine sindidzapyola mulu umenewu kuti ndilimbane nawe. Iwenso usadzapyole muluwu kuti ulimbane ndi ine. 53Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Nahori,#31.53: Mulungu wa Abrahamu…wa Nahori: Abrahamu anali gogo wa Yakobe; Nahori anali bambo wake wa Labani. Mulungu wa atate ao, ndiye adzatiweruze ife aŵiri.” Motero Yakobe adalumbira m'dzina la Mulungu amene Isaki bambo wake ankamuwopa. 54Tsono Yakobe adapereka nsembe paphiripo, naitana anthu ake kuti adzadye chakudya. Atamaliza kudyako, adagona paphiri pomwepo.
55M'maŵa mwake, m'mamaŵa, Labani adampsompsona adzukulu ake aja pamodzi ndi ana ake aakaziwo naŵatsazika, ndipo ataŵadalitsa adachoka namapita kwao.
ที่ได้เลือกล่าสุด:
Gen. 31: BLY-DC
เน้นข้อความ
แบ่งปัน
คัดลอก

ต้องการเน้นข้อความที่บันทึกไว้ตลอดทั้งอุปกรณ์ของคุณหรือไม่? ลงทะเบียน หรือลงชื่อเข้าใช้
Bible Society of Malawi