Gen. 30

30
1Rakele ataona kuti sakumubalira ana Yakobe, adayamba kuchita nsanje ndi mkulu wake uja, ndipo adauza Yakobe kuti, “Mundipatse ana, apo ai, ndingofa basi.” 2Yakobe adapsera mtima Rakele, namuuza kuti, “Sindingathe kuloŵa m'malo mwa Mulungu. Iyeyo ndiye akukuletsa kubala ana.” 3Apo Rakele adati, “Nayu mdzakazi wanga Biliha, khala nayeni kuti andibalire mwana. Motere podzera mwa iye, inenso ndidzakhala ndi ana.” 4Choncho Rakele adapereka Biliha kwa mwamuna wake, ndipo adakhala naye. 5Biliha adatenga pathupi namubalira Yakobe mwana wamwamuna. 6Tsono Rakele adati, “Mulungu waweruza mondikomera mtima. Wamva pemphero langa, ndipo wandipatsa mwana wamwamuna.” Motero mwanayo adamutcha Dani. 7Biliha mdzakazi wa Rakele adatenganso pathupi namubaliranso Yakobe mwana wamwamuna. 8Pamenepo Rakele adati, “Ndalimbana naye kwambiri mkulu wanga, ndipo ndapambana.” Motero mwanayo adamutcha Nafutali.
9Leya ataona kuti waleka kubala, adapereka mdzakazi wake Zilipa kwa Yakobe. 10Ndipo Zilipa adabala mwana wamwamuna. 11Tsono Leya adati, “Ndachita mwai.” Motero mwanayo adamutcha Gadi. 12Zilipa mdzakazi wa Leyayo adamubaliranso Yakobe mwana wamwamuna wachiŵiri. 13Apo Leya adati, “Ndakondwa! Ndipo akazi adzanditchula wamwai.” Motero mwanayo adamutcha Asere.
14Pa nthaŵi yodula tirigu, Rubeni adapita ku minda, nakapezako zipatso za mankhwala a chisulo,#30.14: Mankhwala a chisulo: Ameneŵa anali mankhwala othandiza akazi osabereka kuti ayambe kubereka. Omwewonso anali mankhwala aja a chikoka otchedwa “Kondaine.” ndipo adadzapatsa Leya mai wake. Rakele adauza Leya kuti, “Chonde patseko mankhwala amene mwana wako wakufuniraŵa.” 15Leya adayankha kuti, “Kodi sunakhutitsidwebe ndi mwamuna wanga udandilandayu? Tsopano ufuna kutenganso mankhwala a chisulo amene mwana wanga wandifunira?” Rakele adati, “Ukandipatsa mankhwala a chisulo ochokera kwa mwana wakoŵa, ŵamunaŵa akhala ndi iwe usiku uno.” 16Pamenepo Yakobe ankabwera madzulo kuchokera ku munda, Leya adatuluka kukamlonjera, nati “Lero mugone kunyumba kwanga kuno, chifukwa cha mankhwala a chisulo ondifunira mwana wanga.” Motero Yakobe adakhala ndi Leya usiku umenewo. 17Mulungu adamva pemphero la Leya, choncho adatenga pathupi, namubalira Yakobe mwana wamwamuna wachisanu. 18Tsono adati, “Mulungu wandipatsa mphotho chifukwa ndidapereka mdzakazi wanga kwa mwamuna wanga.” Motero mwanayo adamutcha Isakara. 19Leya adatenganso pena pathupi, namubalira Yakobe mwana wamwamuna wachisanu ndi chimodzi. 20Ndipo adati, “Mulungu wandipatsa mphotho yokoma. Tsopano mwamuna wanga adzakhala nane chifukwa ndamubalira ana aamuna asanu ndi mmodzi.” Motero mwanayo adamutcha Zebuloni. 21Pambuyo pake adabala mwana wamkazi, namutcha Dina. 22Tsono Mulungu adakumbukira Rakele, namva pemphero lake, nkulola kuti abale ana. 23Iyenso adatenga pathupi, nabala mwana wamwamuna. Ndipo adati, “Mulungu wandichotsa manyazi a uchumba wanga.” 24Motero mwanayo adamutcha Yosefe, nanena kuti, “Mulungu andipatse wina mwana.”
Yakobe achita chipangano ndi Labani
25Atabadwa Yosefe, Yakobe adauza Labani kuti, “Mundilole ndizibwerera kwathu. 26Patseni akazi anga ndakugwirirani ntchitoŵa, pamodzi ndi ana anga, ndipo ndichoke. Mukudziŵa kuti ndakugwirirani bwino ntchito.” 27Labani adamuuza kuti, “Undilole kuti ndinenepo mau aŵa, ‘Ine ndi nzeru zamtundu ndadziŵadi kuti Chauta wandidalitsa chifukwa cha iwe. 28Tandiwuza malipiro ako, ndikupatsa.’ ” 29Yakobe adayankha kuti, “Mukudziŵa m'mene ndakugwirirani ntchito, ndi m'mene zoŵeta zanu zaswanirana kwambiri pozisamala ine. 30Kale munali ndi zoŵeta pang'ono koma tsopano zachuluka, ndipo Chauta wakudalitsani chifukwa cha ine. Tsopano ndiyenera kusamala banja langa.” 31Apo Labani adamufunsa kuti, “Kodi ndikulipire chiyani?” Yakobe adayankha kuti, “Sindifuna malipiro ena aliwonse. Komabe ndidzapitirira kukuŵeterani zoŵeta zanu, mukavomera kuchita zimene ndinene. 32Lero ndipita pakati pa zoŵeta zanu zonse. Ndipatula nkhosa zonse zakuda, ndiponso mbuzi zonse zamaŵangamaŵanga ndi zamathothomathotho. Malipiro amene ndifuna ine ndi ameneŵa. 33Patsogolo pake mudzazindikira ngati ndachita zimenezi mokhulupirika pamene mubwere kudzaona malipiro anga. Mukadzaona kuti ndili ndi mbuzi yopanda mathotho kapena maŵanga kapena mwanawankhosa amene sali wakuda, mudzadziŵe kuti imeneyo ndi yakuba.” 34Labani adavomera, adati, “Chabwino. Tichite monga waneneramo.” 35Koma tsiku limenelo, Labani adachotsa atonde onse amathothomathotho ndi amaŵangamaŵanga, kudzanso mbuzi zazikazi zamathothomathotho ndi zamaŵangamaŵanga, zonse za maŵanga oyera. Adachotsanso nkhosa zonse zakuda, nauza ana ake kuti aziyang'anire zoŵeta zonsezo. 36Atatero adasiyana naye Yakobe uja nayenda mtunda wa masiku atatu. M'menemo nkuti Yakobeyo akuŵeta zoŵeta zina za Labani.
37Tsono Yakobe adatenga nthambi zaziŵisi za mitengo ya mitundu itatu yakudzikolo, nazikungunula makungwa, kotero kuti nthambizo zinkaoneka za mipyololo yoyera. 38Nthambizo adaziika patsogolo pa zoŵeta kumene zinkamwera madzi, kuti zoŵetazo ziziyang'ana nthambizo pomwa madzi, chifukwa zoŵetazo zinkakwerewa podzamwa madzi. 39Motero zoŵetazo zikatenga maŵere zitayang'ana nthambizo, ana ake ankakhala ndi maonekedwe amathothomathotho ndiponso amaŵangamaŵanga. 40Yakobe adaika anaankhosa padera, naika nkhosa zina kuti ziyang'anane ndi zoŵeta za Labani zamathothomathotho ndi zakuda. Mwa njira imeneyi adapeza zoŵeta zakezake, ndipo sadazisokoneze ndi zoŵeta za Labani. 41Zoŵeta zamphamvu zikamakwerewa, Yakobe ankazikhazikira nthambi zija kumaso kwake pa malo omwera, kuti pakutero zitenge maŵere pafupi ndi nthambizo. 42Choncho zoŵeta zikakhala zofooka zinali za Labani, koma zamphamvu zinali za Yakobe. 43Mwa njira imeneyi Yakobe adalemera kwambiri. Adakhala ndi zoŵeta zambiri, akapolo aamuna ndi aakazi, ngamira ndi abulu.

ที่ได้เลือกล่าสุด:

Gen. 30: BLY-DC

เน้นข้อความ

แบ่งปัน

คัดลอก

None

ต้องการเน้นข้อความที่บันทึกไว้ตลอดทั้งอุปกรณ์ของคุณหรือไม่? ลงทะเบียน หรือลงชื่อเข้าใช้

วิดีโอสำหรับ Gen. 30