Yoh. 17
17
Yesu adzipempherera
1Yesu atanena zimenezi, adayang'ana kumwamba nati, “Atate, yafika nthaŵi. Lemekezani Mwana wanu, kuti Mwanayo akulemekezeni Inu. 2Pajatu mudampatsa mphamvu zolamulira anthu onse, kuti apereke moyo wosatha kwa onse amene mudampatsa. 3#Lun. 15.3Moyo wosathawo ndi wakuti akudziŵeni Inu, amene nokhanu ndinu Mulungu weniweni, ndipo adziŵenso Yesu Khristu amene mudamtuma. 4Ndakulemekezani pansi pano pakutsiriza ntchito imene mudandipatsa. 5Ndipo tsopano Inu Atate mundilemekeze pamaso panu ndi ulemerero uja umene ndinali nawo kwa Inu lisanalengedwe dziko lapansi.”
Yesu apempherera ophunzira ake
6“Amene mudaŵapatula mwa anthu onse ndi kundipatsa Ine, ndaŵadziŵitsa dzina lanu. Anali anu, Inu mudaŵapereka kwa Ine, ndipo adasunga mau anu. 7Tsopano akudziŵa kuti zonse zimene mudandipatsa nzochokera kwa Inu. 8Pakuti ndaŵapatsa mau amene mudandiwuza Ine, ndipo aŵalandira. Akudziŵadi kuti ndidachokera kwa Inu, ndipo sakayika kuti ndinu mudandituma.
9“Ine ndikuŵapempherera. Sindikupempherera anthu ena onse, koma ndikupempherera iwoŵa amene mudandipatsa, chifukwa ndi anu. 10Zanga zonse nzanu, monga zanu zonse nzanga, motero ndimalemekezedwa mwa iwowo. 11Ndilikudza kwa Inu. Ine sindikhalanso pansi pano ai, koma iwoŵa akhala pansi pano. Atate oyera, asungeni iwoŵa m'dzina lanu limene mudandipatsa, kuti akhale amodzi monga ife. 12#Mas. 41.9; 2Es. 2.26; Yoh. 13.18 Pamene ndinali nawo pamodzi, ndinkaŵasunga ndi mphamvu za dzina lanu, zimene mudandipatsa. Ndidaŵalondoloza bwino, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adatayika, kupatula yekha uja amene adayenera kutayika, kuti zipherezere zimene Malembo adaaneneratu.
13“Tsopano ndilikudza kwa Inu. Ndikulankhula zimenezi pamene ndili pansi pano, kuti chimwemwe changa chikhalenso chodzaza mwa iwowo. 14Ndaŵaphunzitsa mau anu. Anthu odalira zapansipano amadana nawo, chifukwa iwo sali anzao, monga Inenso sindili mnzao. 15Sindikupempha kuti muŵachotse pansi pano ai, koma kuti muŵatchinjirize kwa Woipa uja. 16Iwo sali a dziko lapansi, monga Inenso sindili wa dziko lapansi. 17Muziŵapatula ndi mau anu kuti akhale anthu anu. Mau anuwo ngoona zedi. 18Monga mudandituma Ine pansi pano, Inenso ndaŵatuma pansi pano. 19Ndipo chifukwa cha iwoŵa ndikudzipereka kwa Inu, kuti iwonso akhale odzipereka moonadi kwa Inu.”
Yesu apempherera onse odzamkhulupirira
20“Sindikupempherera iwo okhaŵa ai, komanso amene adzandikhulupirira chifukwa cha mau ao. 21Ndikuŵapempherera kuti iwo onse akhale amodzi. Monga Inu Atate mumakhala mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, iwonso akhale mwa Ife. Motero anthu onse adzakhulupirira kuti mudandituma. 22Ulemerero womwewo umene mudandipatsa, ndaŵapatsanso iwoŵa. Akhale amodzi monga Ife tili amodzi. 23Ine ndikhale mwa iwo, Inu mwa Ine, kuti akhale amodzi kwenikweni. Motero anthu onse adzazindikira kuti mudandituma ndinu, ndipo kuti mumaŵakonda monga momwe mumandikondera Ine.
24“Atate, ndifuna kuti amene mudandipatsa, iwonso akhale pamodzi ndi Ine kumene ndili. Ndifuna kuti aone ulemerero wanga umene mudandipatsa, chifukwa mudandikonda dziko lapansi lisanalengedwe. 25Atate olungama, anthu odalira zapansipano sadakudziŵeni ai, koma Ine ndimakudziŵani, ndipo aŵa ali panoŵa akudziŵa kuti ndinu mudandituma. 26Ndidaŵadziŵitsa dzina lanu, ndipo ndidzaŵaphunzitsabe. Ndifuna kuti chikondi chimene mumandikonda nacho, chikhalenso mwa iwo, ndipo Ine mwa iwo.”
Currently Selected:
Yoh. 17: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi