YouVersion Logo
Search Icon

Yoh. 18

18
Yesu agwidwa
(Mt. 26.47-56; Mk. 14.43-50; Lk. 22.47-53)
1Yesu atanena zimenezi, adapita ndi ophunzira ake kutsidya kwa kamtsinje ka Kedroni.#18.1: Kamtsinje ka Kedroni: Kale padaalidi kamtsinje kamene kankadutsa pakati pa Yerusalemu ndi Phiri la Olivi. Kankakhala ndi madzi pa nthaŵi yamvula (yachisanu) yokha. Masiku ano pamangooneka khwaŵa chabe. Nkuwona m'mabaibulo mwina amati Khwaŵa la Kedroni. Kumeneko kunali munda, ndipo adaloŵa m'menemo. 2Yudasi yemwe, amene adapereka Yesu kwa adani ake, ankaŵadziŵa malowo, pakuti Yesu ankapita kumeneko kaŵirikaŵiri ndi ophunzira ake. 3Yudasiyo adatenga gulu la asilikali achiroma pamodzi ndi asilikali a ku Nyumba ya Mulungu amene akulu a ansembe ndi Afarisi adaaŵatuma. Iwo adapita kumundako atatenga nyale ndi miyuni ndi zida zankhondo. 4Yesu adaadziŵiratu zonse zimene zinalikudzamugwera. Nchifukwa chake Iye adaima poyera, naŵafunsa kuti, “Kodi mukufuna yani?” 5Adamuyankha kuti, “Tikufuna Yesu wa ku Nazarete.” Yesu adati, “Ndine, ndilipo.” Yudasi, wompereka kwa adani ake uja, anali nao pomwepo. 6Pamene Yesu adaŵayankha kuti, “Ndine, ndilipo,” iwo adabwerera m'mbuyo nagwa pansi. 7Yesu adaŵafunsanso kuti, “Mukufuna yani kodi?” Iwo aja adati “Tikufuna Yesu wa ku Nazarete.” 8Yesu adati, “Ndakuuzani kuti ndine, ndilipo. Tsono ngati mukufuna Ine, aŵa alekeni apite.” 9(Adaatero kuti zipherezere zimene Iye adaanena kale kuti, “Sindidatayepo ndi mmodzi yemwe mwa amene mudandipatsa.”)
10Simoni Petro anali ndi lupanga. Adalisolola, natema kapolo wa mkulu wa ansembe onse, mpaka kumusenga khutu la ku dzanja lamanja. Kapoloyo dzina lake anali Malkusi. 11#Mt. 26.39; Mk. 14.36; Lk. 22.42Apo Yesu adauza Petro kuti, “Bwezera lupanga lako m'chimake. Kodi ukuti ndisamwe chikho cha masautso chimene Atate andipatsa?”
Yesu kwa Anasi
(Mt. 26.57-58; Mk. 14.53-54; Lk. 22.54)
12Gulu la asilikali achiroma lija, pamodzi ndi mtsogoleri wao, ndiponso asilikali achiyuda, adagwira Yesu nammanga. 13Poyamba adapita naye kwa Anasi, chifukwa anali mpongozi wa Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe onse chaka chimenecho. 14#Yoh. 11.49, 50 Kayafayo ndi yemwe uja amene adaalangiza anzake kuti nkwabwino koposa kuti munthu mmodzi afe m'malo mwa anthu onse.
Petro akana Yesu
(Mt. 26.69-70; Mk. 14.66-68; Lk. 22.55-57)
15Simoni Petro ndi wophunzira wina adatsatira Yesu. Wophunzira winayo anali wodziŵika kwa mkulu wa ansembe onse. Tsono iye adaloŵa pamodzi ndi Yesu m'bwalo la nyumba ya mkulu wa ansembeyo. 16Koma Petro adaima pa khomo kunja. Wophunzira wina uja, amene anali wodziŵikayo, adatuluka nakalankhula ndi mtsikana wolonda pa khomo, nkumuloŵetsa Petroyo. 17Mtsikanayo adafunsa Petro kuti, “Kodi inu sindinunso mmodzi mwa ophunzira a munthuyu?” Iye adati, “Ineyo? Iyai.”
18Antchito pamodzi ndi asilikali achiyuda aja adaaimirira pamenepo atasonkha moto nkumaotha, chifukwa kunkazizira. Petro nayenso adaaimirira pomwepo nkumaotha nao motowo.
Mkulu wa ansembe onse afunsa Yesu mafunso
(Mt. 26.59-66; Mk. 14.55-64; Lk. 22.66-71)
19Tsono mkulu wa ansembe onse adafunsa Yesu za ophunzira ake, ndiponso za zimene Iye ankaphunzitsa. 20Yesu adati, “Ine ndinkalankhula mosabisa pamaso pa anthu onse. Ndinkaphunzitsa m'nyumba zamapemphero ndiponso m'Nyumba ya Mulungu, m'mene anthu onse amasonkhana. Sindidalankhule kanthu mobisa ai. 21Nanga tsono mukundifunsiranji Ineyo? Funsani amene adamva zomwe ndinkaŵauza. Iwowo akudziŵa zimene ndinkanena.” 22Atanena zimenezi, mmodzi mwa asilikali oimirira pomwepo adamenya Yesu kumaso, adati, “Ungayankhe choncho kwa mkulu wa ansembe onse?” 23Yesu adamuyankha kuti, “Ngati ndalankhula moipa, chitchule choipacho. Koma ngati ndalankhula moona, ukundimenyeranji?”
24Anasi adatumiza Yesu ali chimangire kwa Kayafa, mkulu wa ansembe onse.
Petro akananso Yesu
(Mt. 26.71-75; Mk. 14.69-72; Lk. 22.58-62)
25Simoni Petro anali chililibe akuwotha nao moto. Tsono ena adamufunsa kuti, “Kodi iwenso sindiwe mmodzi mwa ophunzira a munthu uja?” Petro adakana, adati, “Iyai.” 26Wantchito wina wa mkulu wa ansembe onse, mbale wa munthu uja amene Petro adaamusenga khutu, adamufunsa kuti, “Kodi sindidakuwone m'munda muja uli naye?” 27Petro adakananso, nthaŵi yomweyo tambala adalira.
Yesu ku bwalo la Pilato
(Mt. 27.1-2, 11-14; Mk. 15.1-5; Lk. 23.1-5)
28Adamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita naye ku bwalo la bwanamkubwa. Akuluakulu a Ayuda sadaloŵe nao m'bwalo la bwanamkubwalo, kuwopa kuti angaipitsidwe, pakuti ankafuna kudya phwando la Paska. 29Motero Pilato adatulukira kwa iwo naŵafunsa kuti, “Mwampeza cholakwa chanji munthuyu?” 30Iwo adati, “Akadapanda kuchita choipa ameneyu, sibwenzi titadzampereka kwa inu ai.” 31Choncho Pilato adaŵauza kuti, “Mtengenitu tsono inuyo, mukamuweruze potsata malamulo anu.” Koma Ayudawo adati, “Ife sitiloledwa kupha munthu ai.” 32#Yoh. 3.14; 12.32 (Zidaatero kuti zipherezere zimene Yesu adaanena za imfa yake.)
33Pilato adaloŵanso m'nyumba yake ija, naitana Yesu. Adamufunsa kuti, “Kodi iwe, ndiwe Mfumu ya Ayuda?” 34Yesu adati, “Kodi mukunena zimenezi mwa inu nokha, kapena ena adakuuzani za Ine?” 35Pilato adati, “Ine ndine Myuda kodi? Anthu a mtundu wako womwe ndiponso akulu a ansembe ndiwo akupereka kwa ine. Udachita chiyani?” 36Yesu adayankha kuti, “Ufumu wanga si wapansipano ai. Ufumu wanga ukadakhala wapansipano, bwenzi anyamata anga atamenya nkhondo kuti ndisaperekedwe kwa akulu a Ayuda. Komatu ai, ufumu wanga si wapansipano.” 37Pilato adati, “Tsono ndiye kuti ndiwedi mfumu, ati?” Yesu adati, “Mwanena nokha kuti ndine mfumu. Ine ndidabwera pansi pano ndipo ndidabadwa kuti ndidzachitire umboni choona. Aliyense wokonda choona amamva mau anga.” 38Pilato adamufunsa kuti, “Choona nchiyaninso?”
Pilato agamula kuti Yesu aphedwe
(Mt. 27.15-31; Mk. 15.6-20; Lk. 23.13-25)
Pilato atanena mau ameneŵa, adatulukiranso kwa Ayuda, naŵauza kuti, “Ine munthuyu sindikumpeza chifukwa chilichonse. 39Koma potsata chizoloŵezi chanu, pa nthaŵi ya chikondwerero cha Paska ndimakumasulirani mkaidi mmodzi. Tsono kodi mukufuna kuti ndikumasulireni Mfumu ya Ayudayi?” 40Pamenepo iwo adafuulanso kuti, “Ameneyu ai, koma Barabasi.” (Barabasiyo anali chigaŵenga.)

Currently Selected:

Yoh. 18: BLY-DC

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in