Yoh. 16
16
Akhristu adzazunzidwa
1“Ndakuuziranitu zonsezi kuti mungadzataye mtima. 2Adzakudulani ku mpingo. Komanso nthaŵi ilikudza yakuti aliyense amene adzakuphani, adzayesa kuti akutumikira Mulungu. 3Adzachita zimenezi chifukwa sadadziŵe Atate kapenanso Ine. 4Koma ndimati muzimve zimenezi kuti nthaŵi yakeyo ikadzafika, mudzakumbukire kuti ndidaakuuziranitu.”
Za ntchito ya Mzimu Woyera
“Sindidakuuzeni zimenezi poyamba paja ai, chifukwa ndinali nanu pamodzi. 5Koma tsopano ndikupita kwa amene adandituma, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu wondifunsa kuti, ‘Mukupita kuti?’ 6M'mitima mwanu mwadzaza chisoni chifukwa ndakuuzani zimenezi. 7Komabe ndikukuuzani zoona, kuti nkwabwino koposa kwa inu kuti ndichoke. Pakuti ngati sindichoka, Nkhoswe ija siidzabwera kwa inu. Koma ngati ndipita, ndidzaitumiza kwa inu. 8Ndipo Iyeyu atafika, adzaŵatsimikiza anthu a pansi pano kuti ngolakwa pa za kuchimwa, za kulungama, ndiponso za kuweruza. 9Ngolakwa pa za kuchimwa, chifukwa sandikhulupirira. 10Ngolakwa pa za kulungama, chifukwa ndikupita kwa Atate ndipo simudzandiwonanso. 11Ngolakwa pa za kuweruza, chifukwa Satana, mfumu ya anthu oipa a dziko lino lapansi, waweruzidwa kale.
12“Ndili nawo mau ena ambiri oti ndikuuzeni, koma simungathe kuŵamvetsa tsopano ai. 13#Lun. 9.11Koma akadzafika Mzimu wodziŵitsa zoona uja adzakuphunzitsani zoona zonse. Pakuti sadzalankhula zochokera kwa Iye yekha ai, koma zilizonse zimene Atate adzamuuze, ndizo zimene adzalankhula. Ndipo adzakudziŵitsani zinthu zam'tsogolo. 14Adzandilemekeza, pakuti adzatenga zochokera kwa Ine nadzakudziŵitsani. 15Zonse za Atate nzanga. Nchifukwa chake ndanena kuti adzatenga zochokera kwa Ine, nadzakudziŵitsani inu.”
Chisoni chidzasanduka chimwemwe
16“Kanthaŵi pang'ono ndipo simudzandiwonanso, koma patapitanso kanthaŵi pang'ono, mudzandiwona.”
17Ophunzira ake ena adayamba kufunsana kuti, “Kodi nchiyani akutiwuzachi? Akuti, ‘Kanthaŵi pang'ono ndipo simudzandiwonanso, koma patapitanso kanthaŵi pang'ono, mudzandiwona.’ Akutinso, ‘Chifukwa ndikupita kwa Atate.’ 18Kodi nchiyani akunenachi kuti, ‘Kanthaŵi pang'ono?’ Sitikumvetsa zimene akufuna kunena.”
19Yesu adaazindikira kuti ophunzirawo akufuna kumufunsa. Choncho adati, “Kodi mukufunsana za mau amene ndanenaŵa akuti, ‘Kanthaŵi pang'ono ndipo simudzandiwonanso, koma patapitanso kanthaŵi pang'ono, mudzandiwona?’ 20Ndithu ndikunenetsa kuti inu mudzalira ndi kukhuza, koma anthu odalira zapansi pano adzakondwa. Inu mudzamva chisoni, koma chisoni chanu chidzasanduka chimwemwe. 21Pa nthaŵi yochira mai amavutika chifukwa nthaŵi yake yafika. Koma pamene wabadwa mwana, saganizakonso za kuzunzikako, chifukwa cha chimwemwe chakuti kunja kuno kwabadwa mwana. 22Chomwecho inunso mukuvutika tsopano, koma ndidzakuwonaninso. Pamenepo mtima wanu udzakondwa, ndipo palibe munthu amene adzakulandani chimwemwe chanucho. 23Pa tsiku limenelo simudzandifunsa kanthu. Ndithu ndikunenetsa kuti chilichonse chimene mungapemphe kwa Atate potchula dzina langa, adzakupatsani. 24Mpaka tsopano simunapemphe kanthu potchula dzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikhale chathunthu.”
Yesu wagonjetsa dziko lapansi
25“Ndakuuzani zimenezi mophiphiritsa. Nthaŵi ilikudza pamene sindidzalankhula nanunso mophiphiritsa, koma ndidzakudziŵitsani momveka za Atate. 26Tsiku limenelo mudzapempha potchula dzina langa, ndipo sindikuti Ine ndidzakupempherani kwa Atate ai, 27pakuti okukondani ndi Atate amene. Amakukondani chifukwa mumandikonda, ndipo mumakhulupirira kuti ndidachokera kwa Iwo. 28Ndidachokeradi kwa Atate kudza pansi pano. Tsopano ndikuchokanso pansi pano kupita kwa Atate.”
29Ophunzira ake adati, “Apo ndipo. Tsopano mukulankhula momveka, osatinso mophiphiritsa ai. 30Tsopano tadziŵa kuti mumadziŵa zonse, ndipo palibenso chifukwa choti munthu akufunseni mafunso. Nchifukwa chake tikukhulupirira kuti ndinu ochokera kwa Mulungu.” 31Yesu adaŵayankha kuti, “Kani mwakhulupiriratu tsopano? 32Nthaŵi ilikudza, ndipo yafika kale, pamene mudzabalalikana aliyense kunka kwao, Ine kundisiya ndekha. Komabe sindili ndekha, pakuti Atate ali nane. 33Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”
Currently Selected:
Yoh. 16: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi