Gen. 17

17
Kuumbala: chizindikiro cha chipangano
1Abramu ali wa zaka 99, Chauta adamuwonekera namuuza kuti, “Ine ndine Mulungu Mphambe. Tsono uzindimvera nthaŵi zonse, ndipo uzichita zolungama. 2Ndidzachita nawe chipangano, ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zambiri.” 3Pomwepo Abramu adagwada pansi ndipo Mulungu adati, 4“Nachi chipangano chimene ndidzachite nawe. Ndikulonjeza kuti udzakhala kholo la anthu a mitundu yambiri. 5#Aro. 4.17 Dzina lako silidzakhalanso Abramu, koma Abrahamu.#17.5: Abrahamu: Dzina limeneli limamveka chimodzimodzi ngati mau achihebri otanthauza kuti “kholo la anthu ambiri”. Limeneli ndilo dzina lako, chifukwa ndikukusandutsa kholo la anthu a mitundu yambiri. 6Ndidzakupatsa zidzukulu zambiri, ndipo zina mwa izo zidzakhala mafumu. Udzakhala ndi zidzukulu zambiri kotero kuti zidzakhala mitundu yaikulu. 7#Lk. 1.55 Chipangano changachi ndidzachikhazikitsa pakati pa Ine ndi iwe ndi zidzukulu zako zam'tsogolo, ndipo chidzakhala chipangano chosatha. Ine ndidzakhala Mulungu wako ndi Mulungu wa zidzukulu zako. 8#Ntc. 7.5Dziko lino limene ukukhalamo ngati mlendoli, ndidzakupatsa iwe ndi zidzukulu zako. Dziko lonse la Kanani lidzakhala la zidzukulu zako mpaka muyaya, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao.”
9Mulungu adauzanso Abrahamu kuti, “Iwenso tsono uyenera kuvomera kusunga chipangano changa, pamodzi ndi zidzukulu zako zam'tsogolo. 10#Ntc. 7.8; Aro. 4.11 Iwe pamodzi ndi zidzukulu zako, muyenera kusunga chipangano ichi chakuti mwamuna aliyense pakati panupa aziwumbalidwa. 11Kuyambira tsopano muziwumbalidwa. Chimenechi chidzakhala chizindikiro cha chipangano pakati pa Ine ndi inu. 12Muziwumbala mwana wamwamuna aliyense akakwanitsa masiku asanu ndi atatu. Muziwumbala mwamuna aliyense pa mibadwo yanu yonse, mbadwa kapena kapolo amene mudamgula kwa mlendo wosakhala wa mbumba yanu. 13Inde aliyense aumbalidwe, ndipo chimenechi chidzakhala chizindikiro pa matupi anu, choonetsa kuti chipangano changa ndi inu nchamuyaya. 14Munthu wamwamuna wosaumbalidwa adzachotsedwa pakati pa anthu a mtundu wake, chifukwa sadasunge chipangano changa.”
15Pambuyo pake Mulungu adauza Abrahamu kuti, “Mkazi wakoyu usamutchulenso kuti Sarai. Tsopano dzina lake ndi Sara. 16Iyeyu ndidzamdalitsa ndipo adzakubalira mwana wamwamuna. Ndidzamdalitsa, ndipo adzakhala mai wa mitundu ya anthu. Pakati pa zidzukulu zakezo padzatuluka mafumu.” 17Apo Abrahamu adagwada pansi. Adayamba kuseka, nati, “Kodi mwamuna woti ali ndi zaka 100, angathe kuberekanso? Kodi Sara, amene ali ndi zaka 90, angathe kubalanso?” 18Ndipo adauza Mulungu kuti, “Ndikukupemphani kuti mungodalitsa Ismaele yemweyu.” 19Koma Mulungu adati, “Iyai, ndi mkazi wako Sara amene adzakubalira mwana wamwamuna ndipo udzamutcha Isaki.#17.19: Isaki: Dzina limeneli m'chihebri limatanthauza kuti “akuseka”. Onani pa Gen. 6. Ndidzasunga chipangano changa ndi iyeyo ndiponso ndi zidzukulu zake, ndipo chipanganocho chidzakhala chamuyaya. 20Koma kunena za Ismaeleyu, ndidzamdalitsa, ndipo ndidzampatsa ana ambiri pamodzi ndi zidzukulu. Adzakhala bambo wa mafumu khumi ndi aŵiri, ndipo zidzukulu zake ndidzakhala mtundu waukulu. 21Koma ndidzasunga chipangano changa ndi mwana wako Isaki amene adzabadwa mwa Sara pa nyengo yonga yomwe ino chaka chamaŵachi.”
22Mulungu atatha kulankhula ndi Abrahamu, adamsiya pomwepo. 23Tsiku lomwelo Abrahamu adakumbukira zimene Mulungu adamuuza, ndipo adatenga mwana wake Ismaele ndi akapolo onse obadwira m'nyumba mwake, kapena amene Abrahamu adaŵagula, kungoti amuna onse a m'nyumba mwake, naŵaumbala monga momwe Mulungu adaamuuzira. 24Abrahamu anali wa zaka 99 pa nthaŵi imene adaumbalidwa. 25Mwana wake Ismaele anali wa zaka 13 pamene adaumbalidwa. 26Pa tsiku limeneli Abrahamu ndi mwana wake Ismaele adaumbalidwa, 27pamodzi ndi anthu aamuna onse, amuna obadwira m'banja mwake ndiponso ena amene adaŵagula ndi ndalama kwa alendo, onsewo adaumbalidwa pamodzi ndi iyeyo.

Jelenleg kiválasztva:

Gen. 17: BLY-DC

Kiemelés

Megosztás

Másolás

None

Szeretnéd, hogy a kiemeléseid minden eszközödön megjelenjenek? Regisztrálj vagy jelentkezz be