1
Gen. 17:1
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
Abramu ali wa zaka 99, Chauta adamuwonekera namuuza kuti, “Ine ndine Mulungu Mphambe. Tsono uzindimvera nthaŵi zonse, ndipo uzichita zolungama.
Összehasonlít
Fedezd fel: Gen. 17:1
2
Gen. 17:5
Dzina lako silidzakhalanso Abramu, koma Abrahamu. Limeneli ndilo dzina lako, chifukwa ndikukusandutsa kholo la anthu a mitundu yambiri.
Fedezd fel: Gen. 17:5
3
Gen. 17:7
Chipangano changachi ndidzachikhazikitsa pakati pa Ine ndi iwe ndi zidzukulu zako zam'tsogolo, ndipo chidzakhala chipangano chosatha. Ine ndidzakhala Mulungu wako ndi Mulungu wa zidzukulu zako.
Fedezd fel: Gen. 17:7
4
Gen. 17:4
“Nachi chipangano chimene ndidzachite nawe. Ndikulonjeza kuti udzakhala kholo la anthu a mitundu yambiri.
Fedezd fel: Gen. 17:4
5
Gen. 17:19
Koma Mulungu adati, “Iyai, ndi mkazi wako Sara amene adzakubalira mwana wamwamuna ndipo udzamutcha Isaki. Ndidzasunga chipangano changa ndi iyeyo ndiponso ndi zidzukulu zake, ndipo chipanganocho chidzakhala chamuyaya.
Fedezd fel: Gen. 17:19
6
Gen. 17:8
Dziko lino limene ukukhalamo ngati mlendoli, ndidzakupatsa iwe ndi zidzukulu zako. Dziko lonse la Kanani lidzakhala la zidzukulu zako mpaka muyaya, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao.”
Fedezd fel: Gen. 17:8
7
Gen. 17:17
Apo Abrahamu adagwada pansi. Adayamba kuseka, nati, “Kodi mwamuna woti ali ndi zaka 100, angathe kuberekanso? Kodi Sara, amene ali ndi zaka 90, angathe kubalanso?”
Fedezd fel: Gen. 17:17
8
Gen. 17:15
Pambuyo pake Mulungu adauza Abrahamu kuti, “Mkazi wakoyu usamutchulenso kuti Sarai. Tsopano dzina lake ndi Sara.
Fedezd fel: Gen. 17:15
9
Gen. 17:11
Kuyambira tsopano muziwumbalidwa. Chimenechi chidzakhala chizindikiro cha chipangano pakati pa Ine ndi inu.
Fedezd fel: Gen. 17:11
10
Gen. 17:21
Koma ndidzasunga chipangano changa ndi mwana wako Isaki amene adzabadwa mwa Sara pa nyengo yonga yomwe ino chaka chamaŵachi.”
Fedezd fel: Gen. 17:21
11
Gen. 17:12-13
Muziwumbala mwana wamwamuna aliyense akakwanitsa masiku asanu ndi atatu. Muziwumbala mwamuna aliyense pa mibadwo yanu yonse, mbadwa kapena kapolo amene mudamgula kwa mlendo wosakhala wa mbumba yanu. Inde aliyense aumbalidwe, ndipo chimenechi chidzakhala chizindikiro pa matupi anu, choonetsa kuti chipangano changa ndi inu nchamuyaya.
Fedezd fel: Gen. 17:12-13
Kezdőoldal
Biblia
Olvasótervek
Videók